Quran with Chichewa translation - Surah Al-Ma’idah ayat 107 - المَائدة - Page - Juz 7
﴿فَإِنۡ عُثِرَ عَلَىٰٓ أَنَّهُمَا ٱسۡتَحَقَّآ إِثۡمٗا فَـَٔاخَرَانِ يَقُومَانِ مَقَامَهُمَا مِنَ ٱلَّذِينَ ٱسۡتَحَقَّ عَلَيۡهِمُ ٱلۡأَوۡلَيَٰنِ فَيُقۡسِمَانِ بِٱللَّهِ لَشَهَٰدَتُنَآ أَحَقُّ مِن شَهَٰدَتِهِمَا وَمَا ٱعۡتَدَيۡنَآ إِنَّآ إِذٗا لَّمِنَ ٱلظَّٰلِمِينَ ﴾
[المَائدة: 107]
﴿فإن عثر على أنهما استحقا إثما فآخران يقومان مقامهما من الذين استحق﴾ [المَائدة: 107]
Khaled Ibrahim Betala “Koma ngati kutaoneka kuti mboni ziwiri zija zanama pa umboni wawo, kapena zabisa chinthu, apo awiri achibale a wakufayo aimiire m’malo mwa mboni ziwirizo, (pambuyo pa Swala kuti aulule za bodza lawo). Choncho alumbilire m’dzina la Allah kuti: “Ndithu kulumbira kwathu nkoyenera kuvomerezedwa kuposa kulumbira kwawo; ndipo sitinapyole malire (mukulumbira kwathu). Ndipo sitikuzipekera mbonizo bodza. Ndithudi, ngati ife titachita zotere, ndiye kuti tikhala mwa ochita zoipa, (oyenera kulandira chilango cha Allah).” |