Quran with Chichewa translation - Surah Al-Ma’idah ayat 95 - المَائدة - Page - Juz 7
﴿يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لَا تَقۡتُلُواْ ٱلصَّيۡدَ وَأَنتُمۡ حُرُمٞۚ وَمَن قَتَلَهُۥ مِنكُم مُّتَعَمِّدٗا فَجَزَآءٞ مِّثۡلُ مَا قَتَلَ مِنَ ٱلنَّعَمِ يَحۡكُمُ بِهِۦ ذَوَا عَدۡلٖ مِّنكُمۡ هَدۡيَۢا بَٰلِغَ ٱلۡكَعۡبَةِ أَوۡ كَفَّٰرَةٞ طَعَامُ مَسَٰكِينَ أَوۡ عَدۡلُ ذَٰلِكَ صِيَامٗا لِّيَذُوقَ وَبَالَ أَمۡرِهِۦۗ عَفَا ٱللَّهُ عَمَّا سَلَفَۚ وَمَنۡ عَادَ فَيَنتَقِمُ ٱللَّهُ مِنۡهُۚ وَٱللَّهُ عَزِيزٞ ذُو ٱنتِقَامٍ ﴾
[المَائدة: 95]
﴿ياأيها الذين آمنوا لا تقتلوا الصيد وأنتم حرم ومن قتله منكم متعمدا﴾ [المَائدة: 95]
Khaled Ibrahim Betala “E inu amene mwakhulupirira! Musaphe nyama ya mtchire pomwe inu muli m’mapemphero a Hajj kapena Umrah. Ndipo mwa inu amene angaphe mwadala nyama ya mtchireyo, dipo (lake likhale kuzinga) yofanana ndi yomwe waphayo, mu mtundu wa nyama zowetedwa, (monga mmene) angaweruzire olungama awiri a mwa inu, kukhala nsembe yoperekedwa ku Ka’aba (kuti ikazingidwe kumeneko ndi kuwagawira osauka); kapena alipe dipo la chakudya kudyetsa masikini; kapena m’malo mwake asale kuti alawe kupweteka kwa chinthu chakecho. Ndipo Allah afafaniza zomwe zidapita kale. Koma amene achitenso, Allah amukhaulitsa ndi chilango chochokera kwa Iye. Ndipo Allah Ngwamphamvu zoposa, Wokhaulitsa koopsa |