×

Kodi iwe siudaone kuti Mulungu amadziwa zonse zimene zili mlengalenga ndi chilichonse 58:7 Chichewa translation

Quran infoChichewaSurah Al-Mujadilah ⮕ (58:7) ayat 7 in Chichewa

58:7 Surah Al-Mujadilah ayat 7 in Chichewa (نيانجا)

Quran with Chichewa translation - Surah Al-Mujadilah ayat 7 - المُجَادلة - Page - Juz 28

﴿أَلَمۡ تَرَ أَنَّ ٱللَّهَ يَعۡلَمُ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِۖ مَا يَكُونُ مِن نَّجۡوَىٰ ثَلَٰثَةٍ إِلَّا هُوَ رَابِعُهُمۡ وَلَا خَمۡسَةٍ إِلَّا هُوَ سَادِسُهُمۡ وَلَآ أَدۡنَىٰ مِن ذَٰلِكَ وَلَآ أَكۡثَرَ إِلَّا هُوَ مَعَهُمۡ أَيۡنَ مَا كَانُواْۖ ثُمَّ يُنَبِّئُهُم بِمَا عَمِلُواْ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِۚ إِنَّ ٱللَّهَ بِكُلِّ شَيۡءٍ عَلِيمٌ ﴾
[المُجَادلة: 7]

Kodi iwe siudaone kuti Mulungu amadziwa zonse zimene zili mlengalenga ndi chilichonse chimene chili padziko lapansi? Palibe nkhani za chinsinsi pakati pa anthu atatu zimene Iye sakhala wachinayi, kapena pakati pa anthu asanu pamene Iye sakhala wa chisanu ndi chimodzi, kapena pakati pa anthu ochepa kapena ochuluka, koma Iye amakhala pakati pawo. Kulikonse kumene iwo angakhale pomaliza Iye adzawauza zonse zimene adachita patsiku lachiweruzo. Ndithudi Mulungu amadziwa chilichonse

❮ Previous Next ❯

ترجمة: ألم تر أن الله يعلم ما في السموات وما في الأرض ما, باللغة نيانجا

﴿ألم تر أن الله يعلم ما في السموات وما في الأرض ما﴾ [المُجَادلة: 7]

Khaled Ibrahim Betala
“Kodi sukudziwa (iwe, womvera wanzeru) kuti Allah akudziwa zakumwamba ndi zam’dziko lapansi? Sipakhala manong’onong’o a (anthu) atatu koma Iye Ngwachinayi wawo (ndi kudziwa kwake kosabisika chilichonse cha kumwamba ndi m’dziko), ngakhale a (anthu) asanu koma Iye Ngwachisanu ndi chimodzi wawo (mkudziwa Kwake), ngakhale ali ochepera kuposera pamenepa kapena ochulukira koma Iye ali nawo paliponse pomwe ati akhale (Allah ali nawo pamodzi mukudziwa Kwake kosabisika chilichonse), kenako adzawafotokozera pa tsiku la chiweruziro zimene adachita; ndithu Allah Ngodziwa chilichonse (mokwanira)
❮ Previous Next ❯

Verse in more languages

Transliteration Bangla Bosnian German English Persian French Hindi Indonesian Kazakh Dutch Russian Spanish Turkish Urdu Uzbek