Quran with Chichewa translation - Surah Al-Mujadilah ayat 8 - المُجَادلة - Page - Juz 28
﴿أَلَمۡ تَرَ إِلَى ٱلَّذِينَ نُهُواْ عَنِ ٱلنَّجۡوَىٰ ثُمَّ يَعُودُونَ لِمَا نُهُواْ عَنۡهُ وَيَتَنَٰجَوۡنَ بِٱلۡإِثۡمِ وَٱلۡعُدۡوَٰنِ وَمَعۡصِيَتِ ٱلرَّسُولِۖ وَإِذَا جَآءُوكَ حَيَّوۡكَ بِمَا لَمۡ يُحَيِّكَ بِهِ ٱللَّهُ وَيَقُولُونَ فِيٓ أَنفُسِهِمۡ لَوۡلَا يُعَذِّبُنَا ٱللَّهُ بِمَا نَقُولُۚ حَسۡبُهُمۡ جَهَنَّمُ يَصۡلَوۡنَهَاۖ فَبِئۡسَ ٱلۡمَصِيرُ ﴾
[المُجَادلة: 8]
﴿ألم تر إلى الذين نهوا عن النجوى ثم يعودون لما نهوا عنه﴾ [المُجَادلة: 8]
Khaled Ibrahim Betala “Kodi siudaone! Kwa amene aletsedwa kunong’onezana zoipa pakati pawo, kenako akubwereza zimene adaletsedwa? Akunong’onezana za machimo, mtopola ndi kunyoza Mtumiki. Akakudzera akukulonjera (ndi malonje achinyengo) amene Allah sadakulonjerepo nawo ndipo akunena m’mitima mwawo: “Kodi nchifukwa chiyani Allah sakutilanga ndi mawu tikunenawa (ngati iyeyu ndi Mtumikidi wa Allah?” Jahannam ikuwakwanira: adzailowa. Ndipo taonani kuipa malo (awo) wobwerera |