Quran with Chichewa translation - Surah Al-An‘am ayat 144 - الأنعَام - Page - Juz 8
﴿وَمِنَ ٱلۡإِبِلِ ٱثۡنَيۡنِ وَمِنَ ٱلۡبَقَرِ ٱثۡنَيۡنِۗ قُلۡ ءَآلذَّكَرَيۡنِ حَرَّمَ أَمِ ٱلۡأُنثَيَيۡنِ أَمَّا ٱشۡتَمَلَتۡ عَلَيۡهِ أَرۡحَامُ ٱلۡأُنثَيَيۡنِۖ أَمۡ كُنتُمۡ شُهَدَآءَ إِذۡ وَصَّىٰكُمُ ٱللَّهُ بِهَٰذَاۚ فَمَنۡ أَظۡلَمُ مِمَّنِ ٱفۡتَرَىٰ عَلَى ٱللَّهِ كَذِبٗا لِّيُضِلَّ ٱلنَّاسَ بِغَيۡرِ عِلۡمٍۚ إِنَّ ٱللَّهَ لَا يَهۡدِي ٱلۡقَوۡمَ ٱلظَّٰلِمِينَ ﴾
[الأنعَام: 144]
﴿ومن الإبل اثنين ومن البقر اثنين قل آلذكرين حرم أم الأنثيين أما﴾ [الأنعَام: 144]
Khaled Ibrahim Betala “Ndipo (adalenganso) ngamira ziwiri, (yaikazi ndi yaimuna). Ng’ombe (adalenganso) ziwiri, (yaimuna ndi yaikazi). Nena: “Kodi (Iye) adakuletsani zazimuna zonse ziwiri (ngamira ndi ng’ombe), kapena zazikazi zonse ziwiri (ngamira ndi ng’ombe), kapena zomwe zili m’mimba mwa zazikazi ziwirizo? Kodi mudali mboni pamene Allah ankakulamulani izi? Kodi ndi ndani woipitsitsa kuposa amene akupekera bodza Allah kuti asokeretse anthu popanda kudziwa (malamulo a Allah)? Ndithu Allah saongola anthu ochita zoipa |