Quran with Chichewa translation - Surah Al-An‘am ayat 70 - الأنعَام - Page - Juz 7
﴿وَذَرِ ٱلَّذِينَ ٱتَّخَذُواْ دِينَهُمۡ لَعِبٗا وَلَهۡوٗا وَغَرَّتۡهُمُ ٱلۡحَيَوٰةُ ٱلدُّنۡيَاۚ وَذَكِّرۡ بِهِۦٓ أَن تُبۡسَلَ نَفۡسُۢ بِمَا كَسَبَتۡ لَيۡسَ لَهَا مِن دُونِ ٱللَّهِ وَلِيّٞ وَلَا شَفِيعٞ وَإِن تَعۡدِلۡ كُلَّ عَدۡلٖ لَّا يُؤۡخَذۡ مِنۡهَآۗ أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ أُبۡسِلُواْ بِمَا كَسَبُواْۖ لَهُمۡ شَرَابٞ مِّنۡ حَمِيمٖ وَعَذَابٌ أَلِيمُۢ بِمَا كَانُواْ يَكۡفُرُونَ ﴾
[الأنعَام: 70]
﴿وذر الذين اتخذوا دينهم لعبا ولهوا وغرتهم الحياة الدنيا وذكر به أن﴾ [الأنعَام: 70]
Khaled Ibrahim Betala “Asiye amene achita chipembedzo chawo kukhala masewera ndi chibwana. Ndipo wawanyenga moyo wadziko lapansi. Choncho, akumbutse ndi Qur’aniyo (kuti achenjere), kuti ungaonongedwe mtima uliwonse (ndi kuikidwa m’ndende) kupyolera mu zomwe udapata. Ndipo sukhala ndi mtetezi ngakhale muomboli posakhala Allah, ngakhale utayesera kupereka dipo lamtundu uliwonse silingavomerezedwe (kwa mzimuwo). Awo ndi omwe aonongeka ndi kunjatidwa chifukwa cha zomwe adapeza. Iwo adzakhala ndi chakumwa cha madzi a moto owira kwambiri, ndi chilango chopweteka chifukwa cha kusakhulupirira kwawo (Allah) |