Quran with Chichewa translation - Surah Al-A‘raf ayat 163 - الأعرَاف - Page - Juz 9
﴿وَسۡـَٔلۡهُمۡ عَنِ ٱلۡقَرۡيَةِ ٱلَّتِي كَانَتۡ حَاضِرَةَ ٱلۡبَحۡرِ إِذۡ يَعۡدُونَ فِي ٱلسَّبۡتِ إِذۡ تَأۡتِيهِمۡ حِيتَانُهُمۡ يَوۡمَ سَبۡتِهِمۡ شُرَّعٗا وَيَوۡمَ لَا يَسۡبِتُونَ لَا تَأۡتِيهِمۡۚ كَذَٰلِكَ نَبۡلُوهُم بِمَا كَانُواْ يَفۡسُقُونَ ﴾
[الأعرَاف: 163]
﴿واسألهم عن القرية التي كانت حاضرة البحر إذ يعدون في السبت إذ﴾ [الأعرَاف: 163]
Khaled Ibrahim Betala “Tawafunsani nkhani ya mudzi umene udali m’mphepete mwa nyanja; (anthu am’mudziwo) pamene adali kuswa (lamulo la) tsiku la Sabata (lomwe adauzidwa kuti pa tsikuli asamachite usodzi wa nsomba, koma m’malo mwake azichita mapemphero okha). Nsomba zawo zinkawadzera yandayanda patsiku la Sabata, koma patsiku lomwe silidali la Sabata sizidali kuwabwerera (yandayanda). Motero tidawayesa mayeso chifukwa chakuchimwa kwawo |