Quran with Chichewa translation - Surah At-Taubah ayat 13 - التوبَة - Page - Juz 10
﴿أَلَا تُقَٰتِلُونَ قَوۡمٗا نَّكَثُوٓاْ أَيۡمَٰنَهُمۡ وَهَمُّواْ بِإِخۡرَاجِ ٱلرَّسُولِ وَهُم بَدَءُوكُمۡ أَوَّلَ مَرَّةٍۚ أَتَخۡشَوۡنَهُمۡۚ فَٱللَّهُ أَحَقُّ أَن تَخۡشَوۡهُ إِن كُنتُم مُّؤۡمِنِينَ ﴾
[التوبَة: 13]
﴿ألا تقاتلون قوما نكثوا أيمانهم وهموا بإخراج الرسول وهم بدءوكم أول مرة﴾ [التوبَة: 13]
Khaled Ibrahim Betala “Kodi nchotani kuti musamenyane nawo anthu omwe aswa malonjezo awo, natsimikiza kumtulutsa (kumpirikitsa mu mzinda wa Makka, kapena kumupha) Mtumiki? Iwo ndi amene adayamba kukuputani pachiyambi, nanga mukuwaopa chotani? Allah ndiye wofunika kumuopa, ngati inu mulidi okhulupirira |