Quran with Chichewa translation - Surah At-Taubah ayat 40 - التوبَة - Page - Juz 10
﴿إِلَّا تَنصُرُوهُ فَقَدۡ نَصَرَهُ ٱللَّهُ إِذۡ أَخۡرَجَهُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ ثَانِيَ ٱثۡنَيۡنِ إِذۡ هُمَا فِي ٱلۡغَارِ إِذۡ يَقُولُ لِصَٰحِبِهِۦ لَا تَحۡزَنۡ إِنَّ ٱللَّهَ مَعَنَاۖ فَأَنزَلَ ٱللَّهُ سَكِينَتَهُۥ عَلَيۡهِ وَأَيَّدَهُۥ بِجُنُودٖ لَّمۡ تَرَوۡهَا وَجَعَلَ كَلِمَةَ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ ٱلسُّفۡلَىٰۗ وَكَلِمَةُ ٱللَّهِ هِيَ ٱلۡعُلۡيَاۗ وَٱللَّهُ عَزِيزٌ حَكِيمٌ ﴾
[التوبَة: 40]
﴿إلا تنصروه فقد نصره الله إذ أخرجه الذين كفروا ثاني اثنين إذ﴾ [التوبَة: 40]
Khaled Ibrahim Betala “Ngati simumthandiza (Mtumuki Muhammad {s.a.w} palibe kanthu), ndithu Allah adamthandiza pamene adamtulutsa aja amene sadakhulupirire. Pamene adali awiriwiri kuphanga, pamene ankanena kwa mnzake: “Usadandaule. Ndithu Allah ali nafe pamodzi.” Ndipo Allah adatsitsa mpumulo Wake pa iye, ndipo adaamthangata ndi asilikali a nkhondo omwe simudawaone. Ndipo mawu a amene sadakhulupirire adawachita kukhala apansi ndipo mawu a Allah ndiwo apamwamba. Ndipo Allah Ngopambana, Ngwanzeru zakuya |