Quran with Chichewa translation - Surah Al-hujurat ayat 11 - الحُجُرَات - Page - Juz 26
﴿يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لَا يَسۡخَرۡ قَوۡمٞ مِّن قَوۡمٍ عَسَىٰٓ أَن يَكُونُواْ خَيۡرٗا مِّنۡهُمۡ وَلَا نِسَآءٞ مِّن نِّسَآءٍ عَسَىٰٓ أَن يَكُنَّ خَيۡرٗا مِّنۡهُنَّۖ وَلَا تَلۡمِزُوٓاْ أَنفُسَكُمۡ وَلَا تَنَابَزُواْ بِٱلۡأَلۡقَٰبِۖ بِئۡسَ ٱلِٱسۡمُ ٱلۡفُسُوقُ بَعۡدَ ٱلۡإِيمَٰنِۚ وَمَن لَّمۡ يَتُبۡ فَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلظَّٰلِمُونَ ﴾
[الحُجُرَات: 11]
﴿ياأيها الذين آمنوا لا يسخر قوم من قوم عسى أن يكونوا خيرا﴾ [الحُجُرَات: 11]
Khaled Ibrahim Betala “E inu amene mwakhulupirira! Amuna asanyoze amuna anzawo; mwina (onyozedwa) nkukhala abwino (kwa Allah) kuposa iwo (onyoza). Nawonso akazi asanyoze akazi anzawo; mwina onyozedwa nkukhala abwino (kwa Allah) kuposa iwo (onyoza). Ndipo musatukwanizane pokumbana mitundu kapena kuitanana ndi maina oipa. Taonani kuipa kumuyitanira munthu ndi dzina loti fasiki (wotuluka m’malamulo a Allah) atakhulupirira kale; ndipo amene salapa (ku zimenezi), iwo ndiwo (ochimwa) odzichitira okha chinyengo |