يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا لَا تُقَدِّمُوا بَيْنَ يَدَيِ اللَّهِ وَرَسُولِهِ ۖ وَاتَّقُوا اللَّهَ ۚ إِنَّ اللَّهَ سَمِيعٌ عَلِيمٌ (1) Oh inu anthu okhulupirira! Musadzikweze pamaso pa Mulungu ndi pa Mthenga wake, koma opani Mulungu chifukwa Iye ndiye amene amamva ndi kudziwa chinthu china chilichonse |
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا لَا تَرْفَعُوا أَصْوَاتَكُمْ فَوْقَ صَوْتِ النَّبِيِّ وَلَا تَجْهَرُوا لَهُ بِالْقَوْلِ كَجَهْرِ بَعْضِكُمْ لِبَعْضٍ أَن تَحْبَطَ أَعْمَالُكُمْ وَأَنتُمْ لَا تَشْعُرُونَ (2) Oh inu anthu okhulupirira! Musakweze mawu anu kuposa a Mtumwi ndipo musayankhule ndi mawu okweza kwa iye monga momwe mumachitira mukamayankhulana nokhanokhanu chifukwa ntchito zanu zingasanduke zopanda pake pamene inu simuli kudziwa |
إِنَّ الَّذِينَ يَغُضُّونَ أَصْوَاتَهُمْ عِندَ رَسُولِ اللَّهِ أُولَٰئِكَ الَّذِينَ امْتَحَنَ اللَّهُ قُلُوبَهُمْ لِلتَّقْوَىٰ ۚ لَهُم مَّغْفِرَةٌ وَأَجْرٌ عَظِيمٌ (3) Ndithudi iwo amene amayankhula motsitsa pamaso pa Mtumwi wa Mulungu ndiwo amene Mulungu wayesa mitima yawo kuti ndi yabwino, ndipo iwo adzalandira chikhululukiro ndi mphotho yaikulu |
إِنَّ الَّذِينَ يُنَادُونَكَ مِن وَرَاءِ الْحُجُرَاتِ أَكْثَرُهُمْ لَا يَعْقِلُونَ (4) Ndithudi iwo amene amafuulira iwe kunja kwa zipinda, onse alibe nzeru |
وَلَوْ أَنَّهُمْ صَبَرُوا حَتَّىٰ تَخْرُجَ إِلَيْهِمْ لَكَانَ خَيْرًا لَّهُمْ ۚ وَاللَّهُ غَفُورٌ رَّحِيمٌ (5) Iwo akadapirira mpaka pamene iwe udza kwa iwo, ndithudi, zikadakhala bwino ndipo Mulungu ndi wokhululukira ndi wachisoni chosatha |
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا إِن جَاءَكُمْ فَاسِقٌ بِنَبَإٍ فَتَبَيَّنُوا أَن تُصِيبُوا قَوْمًا بِجَهَالَةٍ فَتُصْبِحُوا عَلَىٰ مَا فَعَلْتُمْ نَادِمِينَ (6) oh inu anthu okhulupirira! Ngati munthu wochita zoipa adza kwa inu ndi nkhani, ifufuzeni poyamba chifukwa mwina mukhoza kupweteka anthu mosadziwa ndi kuyamba kumva chisoni pambuyo pake chifukwa cha zimene mwachita |
وَاعْلَمُوا أَنَّ فِيكُمْ رَسُولَ اللَّهِ ۚ لَوْ يُطِيعُكُمْ فِي كَثِيرٍ مِّنَ الْأَمْرِ لَعَنِتُّمْ وَلَٰكِنَّ اللَّهَ حَبَّبَ إِلَيْكُمُ الْإِيمَانَ وَزَيَّنَهُ فِي قُلُوبِكُمْ وَكَرَّهَ إِلَيْكُمُ الْكُفْرَ وَالْفُسُوقَ وَالْعِصْيَانَ ۚ أُولَٰئِكَ هُمُ الرَّاشِدُونَ (7) Ndipo dziwani kuti pakati panu pali Mtumwi wa Mulungu ndipo iye akamachita zimene Al Hujurat 553 mufuna, ndithudi, inu mukadavutika kwambiri. Koma Mulungu wakusungitsani inu chipembedzo chake ndipo wachipanga icho kukhala chokongola m’mitima mwanu, ndi kupanga kusakhulupirira kukhala chinthu choipa ndiponso kuswa malamulo ndi kusamvera. Awa ndiwo amene amatsatira njira yoyenera |
فَضْلًا مِّنَ اللَّهِ وَنِعْمَةً ۚ وَاللَّهُ عَلِيمٌ حَكِيمٌ (8) Chisomo ndi chifundo chochokera kwa Mulungu. Ndipo Mulungu amadziwa chinthu china chilichonse ndipo ndi wanzeru kwambiri |
وَإِن طَائِفَتَانِ مِنَ الْمُؤْمِنِينَ اقْتَتَلُوا فَأَصْلِحُوا بَيْنَهُمَا ۖ فَإِن بَغَتْ إِحْدَاهُمَا عَلَى الْأُخْرَىٰ فَقَاتِلُوا الَّتِي تَبْغِي حَتَّىٰ تَفِيءَ إِلَىٰ أَمْرِ اللَّهِ ۚ فَإِن فَاءَتْ فَأَصْلِحُوا بَيْنَهُمَا بِالْعَدْلِ وَأَقْسِطُوا ۖ إِنَّ اللَّهَ يُحِبُّ الْمُقْسِطِينَ (9) Ngati magulu awiri ochokera kwa anthu okhulupirira amenyana, khazikitsa mtendere pakati pawo. Koma ngati gulu lina liswa malamulo mopyola muyeso, nonse menyanani nalo gulu lotero mpaka pamene limvera lamulo la Mulungu. Ndipo ngati ilo limvera, khazikitsani mtendere pakati pawo mwachilungamo. Ndithudi Mulungu amakonda iwo amene amachita chilungamo |
إِنَّمَا الْمُؤْمِنُونَ إِخْوَةٌ فَأَصْلِحُوا بَيْنَ أَخَوَيْكُمْ ۚ وَاتَّقُوا اللَّهَ لَعَلَّكُمْ تُرْحَمُونَ (10) Onse okhulupirira ali pachibale. Kotero khazikitsani mtendere ndi kukhululukirana ndi abale anu ndipo opani Mulungu kuti mulandire chisomo chake |
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا لَا يَسْخَرْ قَوْمٌ مِّن قَوْمٍ عَسَىٰ أَن يَكُونُوا خَيْرًا مِّنْهُمْ وَلَا نِسَاءٌ مِّن نِّسَاءٍ عَسَىٰ أَن يَكُنَّ خَيْرًا مِّنْهُنَّ ۖ وَلَا تَلْمِزُوا أَنفُسَكُمْ وَلَا تَنَابَزُوا بِالْأَلْقَابِ ۖ بِئْسَ الِاسْمُ الْفُسُوقُ بَعْدَ الْإِيمَانِ ۚ وَمَن لَّمْ يَتُبْ فَأُولَٰئِكَ هُمُ الظَّالِمُونَ (11) oh inu anthu okhulupirira! Musalole kuti anthu ena aziseka anzawo. Mwina kungatheke kuti gulu limene lisekedwa likhoza kukhala labwino kuposa limene likuseka. Ndiponso musalole akazi kuti aseke anzawo chifukwa mwina kungatheke kuti osekedwawo akhoza kukhala abwino kuposa osekawo. Musafunirane zifukwa wina ndi mnzake kapena kuitanana ndi mayina a mchedzera. Mayina a mchedzera ndi oipa kwa amene wakhulupirira. Ndipo aliyense amene sasiya kuitana anzake ndi maina a mchedzera , ameneyo ndiye wopanda chilungamo |
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا اجْتَنِبُوا كَثِيرًا مِّنَ الظَّنِّ إِنَّ بَعْضَ الظَّنِّ إِثْمٌ ۖ وَلَا تَجَسَّسُوا وَلَا يَغْتَب بَّعْضُكُم بَعْضًا ۚ أَيُحِبُّ أَحَدُكُمْ أَن يَأْكُلَ لَحْمَ أَخِيهِ مَيْتًا فَكَرِهْتُمُوهُ ۚ وَاتَّقُوا اللَّهَ ۚ إِنَّ اللَّهَ تَوَّابٌ رَّحِيمٌ (12) oh inu anthu akhulupirira! Pewani kukaikirana chifukwa kukhala ndi chikayiko ndi tchimo. Ndipo musachite ukazitape pakati panu kapena amiseche. Kodi wina wa inu angakondwere kudya mnofu wa mnzake amene ndi wakufa? Kodi koma inu mumakana kudya.. Kotero opani Mulungu. Ndithudi Mulungu amabwezera chisoni chifukwa ndiye Mwini Chisoni Chosatha |
يَا أَيُّهَا النَّاسُ إِنَّا خَلَقْنَاكُم مِّن ذَكَرٍ وَأُنثَىٰ وَجَعَلْنَاكُمْ شُعُوبًا وَقَبَائِلَ لِتَعَارَفُوا ۚ إِنَّ أَكْرَمَكُمْ عِندَ اللَّهِ أَتْقَاكُمْ ۚ إِنَّ اللَّهَ عَلِيمٌ خَبِيرٌ (13) oh anthu inu inu! Ndithudi Ife tidakulengani inu mwamuna ndi mkazi ndipo tidakupangani inu kukhala mitundu ya anthu ndi mabanja muzidziwana, Ndithudi wopambana kwambiri pakati panu ndiponso pamaso pa Mulungu ndi amene amaopa Mulungu. Ndithudi Mulungu ndi wodziwa chinthu china chilichonse |
۞ قَالَتِ الْأَعْرَابُ آمَنَّا ۖ قُل لَّمْ تُؤْمِنُوا وَلَٰكِن قُولُوا أَسْلَمْنَا وَلَمَّا يَدْخُلِ الْإِيمَانُ فِي قُلُوبِكُمْ ۖ وَإِن تُطِيعُوا اللَّهَ وَرَسُولَهُ لَا يَلِتْكُم مِّنْ أَعْمَالِكُمْ شَيْئًا ۚ إِنَّ اللَّهَ غَفُورٌ رَّحِيمٌ (14) Anthu okhala m’midzi amati, “Ife timakhulupirira.” Nena, “Inu mulibe chikhulupiriro. Koma nenani kuti, “Tadzipereka kwa Mulungu chifukwa chikhulupiriro sichidakhazikike m’mitima mwanu. Ndipo ngati inu mumvera Mulungu ndi Mtumwi wake, Iye sadzachepetsa ntchito zanu, ngakhale m’pang’ono pomwe. Ndithudi Mulungu ndi wokhululukira nthawi zonse ndi Mwini chisoni chosatha.” |
إِنَّمَا الْمُؤْمِنُونَ الَّذِينَ آمَنُوا بِاللَّهِ وَرَسُولِهِ ثُمَّ لَمْ يَرْتَابُوا وَجَاهَدُوا بِأَمْوَالِهِمْ وَأَنفُسِهِمْ فِي سَبِيلِ اللَّهِ ۚ أُولَٰئِكَ هُمُ الصَّادِقُونَ (15) okhulupirira ndi okhawo amene amakhulupirira mwa Mulungu ndi Mtumwi wake ndipo sakayika ngakhale ndi pang’ono pomwe. Iwo amadzipereka kwathunthu pamodzi ndi chuma chawo m’njira ya Mulungu. Ndipo iwo ndiwo olungama |
قُلْ أَتُعَلِّمُونَ اللَّهَ بِدِينِكُمْ وَاللَّهُ يَعْلَمُ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَمَا فِي الْأَرْضِ ۚ وَاللَّهُ بِكُلِّ شَيْءٍ عَلِيمٌ (16) Nena, “Kodi inu mungamuphunzitse Mulungu za chipembedzo chanu? Pamene Mulungu amadziwa chilichonse chili mlengalenga ndi padziko lapansi. Ndipo Mulungundi wodziwa chilichonse |
يَمُنُّونَ عَلَيْكَ أَنْ أَسْلَمُوا ۖ قُل لَّا تَمُنُّوا عَلَيَّ إِسْلَامَكُم ۖ بَلِ اللَّهُ يَمُنُّ عَلَيْكُمْ أَنْ هَدَاكُمْ لِلْإِيمَانِ إِن كُنتُمْ صَادِقِينَ (17) Iwo amaganiza kuti ali kukuchitira iwe chisoni pamene alowa Chisilamu. Nena, “Inu simuli kundichitira ine chisoni polowa chisilamu. Iyayi, koma ndi Mulungu amene wakuchitirani inu chisoni pokulangizani njira yoyenera ngati inu, muli anthu olungama.” |
إِنَّ اللَّهَ يَعْلَمُ غَيْبَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۚ وَاللَّهُ بَصِيرٌ بِمَا تَعْمَلُونَ (18) Ndithudi Mulungu amadziwa zobisika zonse zimene zili mlengalenga ndi padziko lapansi ndipo Mulungu amaona zonse zimene mumachita |