×

سورة القمر باللغة نيانجا

ترجمات القرآنباللغة نيانجا ⬅ سورة القمر

ترجمة معاني سورة القمر باللغة نيانجا - Chichewa

القرآن باللغة نيانجا - سورة القمر مترجمة إلى اللغة نيانجا، Surah Al Qamar in Chichewa. نوفر ترجمة دقيقة سورة القمر باللغة نيانجا - Chichewa, الآيات 55 - رقم السورة 54 - الصفحة 528.

بسم الله الرحمن الرحيم

اقْتَرَبَتِ السَّاعَةُ وَانشَقَّ الْقَمَرُ (1)
Ola lachiweruzo lili pafupi ndipo mwezi wagawanika pakati
وَإِن يَرَوْا آيَةً يُعْرِضُوا وَيَقُولُوا سِحْرٌ مُّسْتَمِرٌّ (2)
Koma iwo akaona chozizwitsa, sakhulupirira ndipo amati, “Ichi sichina ayi koma matsenga ozama.”
وَكَذَّبُوا وَاتَّبَعُوا أَهْوَاءَهُمْ ۚ وَكُلُّ أَمْرٍ مُّسْتَقِرٌّ (3)
Iwo amakana choonadi koma amatsatira zilakolako zawo. Koma chinthu chilichonse chili ndi kumaliza kwake
وَلَقَدْ جَاءَهُم مِّنَ الْأَنبَاءِ مَا فِيهِ مُزْدَجَرٌ (4)
Ndithudi uthenga waperekedwa kale kwa iwo umene uli ndi chenjezo
حِكْمَةٌ بَالِغَةٌ ۖ فَمَا تُغْنِ النُّذُرُ (5)
Wodzadzidwa ndi nzeru koma machenjezo ake sawathandiza iwo china chilichonse
فَتَوَلَّ عَنْهُمْ ۘ يَوْمَ يَدْعُ الدَّاعِ إِلَىٰ شَيْءٍ نُّكُرٍ (6)
Kotero iwe, asiye okha. Patsiku limene woitana adzawaitana kudza ku chinthu choopsa
خُشَّعًا أَبْصَارُهُمْ يَخْرُجُونَ مِنَ الْأَجْدَاثِ كَأَنَّهُمْ جَرَادٌ مُّنتَشِرٌ (7)
Iwo adzadza kumeneko ndi nkhope zogwa pansi, kuchokera kumanda awo monga dzombe louluka ponseponse
مُّهْطِعِينَ إِلَى الدَّاعِ ۖ يَقُولُ الْكَافِرُونَ هَٰذَا يَوْمٌ عَسِرٌ (8)
Adzadza mofulumira kwa oitana anthu osakhulupirira adzati, “Ili ndi tsiku lovuta kwambiri.”
۞ كَذَّبَتْ قَبْلَهُمْ قَوْمُ نُوحٍ فَكَذَّبُوا عَبْدَنَا وَقَالُوا مَجْنُونٌ وَازْدُجِرَ (9)
Asanadze iwo, anthu a Nowa adakana kapolo wathu ndipo adati, “Uyu ndi munthu wamisala.” Ndipo iwo adamuthamangitsa iye ndi kumunyoza kwambiri
فَدَعَا رَبَّهُ أَنِّي مَغْلُوبٌ فَانتَصِرْ (10)
Ndipo iye adadandaula kwa Ambuye wake nati, “Ndagonjetsedwa kotero idzani kuti mundithandize.”
فَفَتَحْنَا أَبْوَابَ السَّمَاءِ بِمَاءٍ مُّنْهَمِرٍ (11)
Motero Ife tidatsekula makomo a kumwamba, ndipo mvula idagwa nthawi yomweyo
وَفَجَّرْنَا الْأَرْضَ عُيُونًا فَالْتَقَى الْمَاءُ عَلَىٰ أَمْرٍ قَدْ قُدِرَ (12)
Ndipo tidatumphutsa a kasupe padziko lapansi kotero madzi onse adakumana monga mwa lamulo lathu
وَحَمَلْنَاهُ عَلَىٰ ذَاتِ أَلْوَاحٍ وَدُسُرٍ (13)
Ndipo tidamunyamula iye m’chombo chopangidwandimatabwandichokhomedwandimisomali
تَجْرِي بِأَعْيُنِنَا جَزَاءً لِّمَن كَانَ كُفِرَ (14)
Chidanyamuka potsogozedwa ndi Ife. Mphotho kwa iye amene adakanidwa
وَلَقَد تَّرَكْنَاهَا آيَةً فَهَلْ مِن مُّدَّكِرٍ (15)
Ndithudi tidachisiya icho ngati chizindikiro koma kodi alipo ena amene adzachenjezedwa
فَكَيْفَ كَانَ عَذَابِي وَنُذُرِ (16)
Kodi chilango changa ndi chenjezo langa zidali zalikulu bwanji
وَلَقَدْ يَسَّرْنَا الْقُرْآنَ لِلذِّكْرِ فَهَلْ مِن مُّدَّكِرٍ (17)
Ndithudi talipanga Buku la Korani kukhala losavuta kulidziwa ndi kulikumbukira. Kodi alipo ena amene adzachenjezedwa
كَذَّبَتْ عَادٌ فَكَيْفَ كَانَ عَذَابِي وَنُذُرِ (18)
Anthu a Aad adakana. Kodi chilango changa ndi chenjezo langa zidali zoopsa bwanji
إِنَّا أَرْسَلْنَا عَلَيْهِمْ رِيحًا صَرْصَرًا فِي يَوْمِ نَحْسٍ مُّسْتَمِرٍّ (19)
Ndithudi Ife tidatumiza mphepo yamkhuntho pa tsiku latsoka losasimbika
تَنزِعُ النَّاسَ كَأَنَّهُمْ أَعْجَازُ نَخْلٍ مُّنقَعِرٍ (20)
Kugwetsa anthu ngati kuti adali mathunthu a mitengo ya mgwalangwa yozulidwa
فَكَيْفَ كَانَ عَذَابِي وَنُذُرِ (21)
Kodi chilango changa ndipo chenjezo langa zidali zoopsa bwanji
وَلَقَدْ يَسَّرْنَا الْقُرْآنَ لِلذِّكْرِ فَهَلْ مِن مُّدَّكِرٍ (22)
Ndithudi talipanga Buku la Korani kukhala losavuta kulizindikira ndi kulikumbukira. Kodi alipo ena amene adzachenjezedwa
كَذَّبَتْ ثَمُودُ بِالنُّذُرِ (23)
Anthu a Thamoud adakana machenjezo
فَقَالُوا أَبَشَرًا مِّنَّا وَاحِدًا نَّتَّبِعُهُ إِنَّا إِذًا لَّفِي ضَلَالٍ وَسُعُرٍ (24)
Iwo adati, “Munthu! Mmodzi yekha wochokera ku mtundu wathu kuti timutsatire? Ndithudi ife tikhala olakwa kwambiri ndiponso a misala.”
أَأُلْقِيَ الذِّكْرُ عَلَيْهِ مِن بَيْنِنَا بَلْ هُوَ كَذَّابٌ أَشِرٌ (25)
“Kodi ndiye kuti uthenga waperekedwa kwa iye yekha pakati pa ife tonse? Iyayi! Iye ndi wabodza ndi wodzikweza.”
سَيَعْلَمُونَ غَدًا مَّنِ الْكَذَّابُ الْأَشِرُ (26)
Mawa iwo adzadziwa kuti wabodza ndi wodzikweza ndani
إِنَّا مُرْسِلُو النَّاقَةِ فِتْنَةً لَّهُمْ فَارْتَقِبْهُمْ وَاصْطَبِرْ (27)
Ndithudi Ife titumiza ngamira yaikazi ngati mayesero kwa iwo. Motero iwe uwapenyetsetse ndipo ukhale wopirira
وَنَبِّئْهُمْ أَنَّ الْمَاءَ قِسْمَةٌ بَيْنَهُمْ ۖ كُلُّ شِرْبٍ مُّحْتَضَرٌ (28)
Ndipo uwauze kuti azigawana madzi. Ndipo nthawi yomwera madzi idzakhazikitsidwa
فَنَادَوْا صَاحِبَهُمْ فَتَعَاطَىٰ فَعَقَرَ (29)
Ndipo iwo adaitana m’bale wawo ndipo iye adatulutsa lupanga ndi kuipha
فَكَيْفَ كَانَ عَذَابِي وَنُذُرِ (30)
Kodi chilango changa ndi chenjezo langa zidali zoopsa bwanji
إِنَّا أَرْسَلْنَا عَلَيْهِمْ صَيْحَةً وَاحِدَةً فَكَانُوا كَهَشِيمِ الْمُحْتَظِرِ (31)
Ndithudi tidawatumizira mfuwu umodzi ndipo onse adali ngati nkhuni zodula zimene munthu womanga mpanda amatola
وَلَقَدْ يَسَّرْنَا الْقُرْآنَ لِلذِّكْرِ فَهَلْ مِن مُّدَّكِرٍ (32)
Ndithudi talipanga Buku la Korani kukhala losavuta kulizindikira ndi kulikumbukira. Koma kodi alipo ena amene adzachenjezedwa
كَذَّبَتْ قَوْمُ لُوطٍ بِالنُّذُرِ (33)
Anthu a Loti adati chenjezo lathu ndi labodza
إِنَّا أَرْسَلْنَا عَلَيْهِمْ حَاصِبًا إِلَّا آلَ لُوطٍ ۖ نَّجَّيْنَاهُم بِسَحَرٍ (34)
Ndithudi Ife tidawatumizira mphepo yonyamula miyala kupatula a pa banja la Loti amene tidawapulumutsa mu ola lomaliza la usiku
نِّعْمَةً مِّنْ عِندِنَا ۚ كَذَٰلِكَ نَجْزِي مَن شَكَرَ (35)
Monga chisomo chochokera kwa Ife, motero ndi mmene timalipirira anthu oyamika
وَلَقَدْ أَنذَرَهُم بَطْشَتَنَا فَتَمَارَوْا بِالنُّذُرِ (36)
Ndithudi iye adawachenjeza za chilango chathu choopsa koma iwo adakana chenjezo lathu
وَلَقَدْ رَاوَدُوهُ عَن ضَيْفِهِ فَطَمَسْنَا أَعْيُنَهُمْ فَذُوقُوا عَذَابِي وَنُذُرِ (37)
Ndipo, ndithudi, iwo adafuna kuchititsa manyazi alendo ake. Motero Ife tidawachititsa khungu. Kotero inu lawani chilango changa ndi machenjezo anga
وَلَقَدْ صَبَّحَهُم بُكْرَةً عَذَابٌ مُّسْتَقِرٌّ (38)
Ndithudi chilango chowawa chidadza pa iwo nthawi yam’mawa
فَذُوقُوا عَذَابِي وَنُذُرِ (39)
Kotero inu lawani chilango changa ndi machenjezo anga
وَلَقَدْ يَسَّرْنَا الْقُرْآنَ لِلذِّكْرِ فَهَلْ مِن مُّدَّكِرٍ (40)
Ndithudi talipanga Buku la Korani kukhala losavuta kulizindikira ndi kulikumbukira. Kodi alipo ena amene adzachenjezedwa
وَلَقَدْ جَاءَ آلَ فِرْعَوْنَ النُّذُرُ (41)
Ndipo, ndithudi, machenjezo adadza kwa anthu a Farawo
كَذَّبُوا بِآيَاتِنَا كُلِّهَا فَأَخَذْنَاهُمْ أَخْذَ عَزِيزٍ مُّقْتَدِرٍ (42)
Iwo adati machenjezo athu onse ndi abodza motero tidawaononga ndi chilango champhamvu yochuluka
أَكُفَّارُكُمْ خَيْرٌ مِّنْ أُولَٰئِكُمْ أَمْ لَكُم بَرَاءَةٌ فِي الزُّبُرِ (43)
Kodi anthu anu osakhulupirira ndi abwino kuposa awa? Kapena inu muli ndi chitetezo mu m’mawu a Mulungu
أَمْ يَقُولُونَ نَحْنُ جَمِيعٌ مُّنتَصِرٌ (44)
Kodi kapena iwo amati, “Ife ndife ambiri ndipo tidzapambana?”
سَيُهْزَمُ الْجَمْعُ وَيُوَلُّونَ الدُّبُرَ (45)
Tsopano magulu awo ali kupirikitsidwa ndipo iwo ali kuthawa
بَلِ السَّاعَةُ مَوْعِدُهُمْ وَالسَّاعَةُ أَدْهَىٰ وَأَمَرُّ (46)
Iyayi, koma ola lachiweruzo ndi nthawi imene iwo adalonjezedwa ndipo ola limeneli lidzakhala loopsa kwambiri
إِنَّ الْمُجْرِمِينَ فِي ضَلَالٍ وَسُعُرٍ (47)
Ndithudi anthu osakhulupirira ndi olakwa adzapsya
يَوْمَ يُسْحَبُونَ فِي النَّارِ عَلَىٰ وُجُوهِهِمْ ذُوقُوا مَسَّ سَقَرَ (48)
Tsiku limene iwo adzaduduluzidwa pa nkhope zawo kunka ku moto, (zidzanenedwa) “Lawani ululu wa ku Moto.”
إِنَّا كُلَّ شَيْءٍ خَلَقْنَاهُ بِقَدَرٍ (49)
Ndithudi tidalenga chilichonse molingana ndi muyeso wake
وَمَا أَمْرُنَا إِلَّا وَاحِدَةٌ كَلَمْحٍ بِالْبَصَرِ (50)
Ndipo ulamuliro wathu ndi umodzi monga kuphenira kwa diso
وَلَقَدْ أَهْلَكْنَا أَشْيَاعَكُمْ فَهَلْ مِن مُّدَّكِرٍ (51)
Ndithudi Ife tidaononga kale anthu onga inu koma kodi alipo amene anga chenjezedwe
وَكُلُّ شَيْءٍ فَعَلُوهُ فِي الزُّبُرِ (52)
Ndipo zonse zimene adachita zidalembedwa
وَكُلُّ صَغِيرٍ وَكَبِيرٍ مُّسْتَطَرٌ (53)
Ndipo chilichonse chaching’ono ndi chachikulu chidalembedwa kale
إِنَّ الْمُتَّقِينَ فِي جَنَّاتٍ وَنَهَرٍ (54)
Ndithudi onse amene amalewa zoipa adzakhala m’kati mwa minda ndi mitsinje
فِي مَقْعَدِ صِدْقٍ عِندَ مَلِيكٍ مُّقْتَدِرٍ (55)
Ku Paradiso kufupi ndi Mfumu yamphamvu zonse
❮ السورة السابقة السورة التـالية ❯

قراءة المزيد من سور القرآن الكريم :

1- الفاتحة2- البقرة3- آل عمران
4- النساء5- المائدة6- الأنعام
7- الأعراف8- الأنفال9- التوبة
10- يونس11- هود12- يوسف
13- الرعد14- إبراهيم15- الحجر
16- النحل17- الإسراء18- الكهف
19- مريم20- طه21- الأنبياء
22- الحج23- المؤمنون24- النور
25- الفرقان26- الشعراء27- النمل
28- القصص29- العنكبوت30- الروم
31- لقمان32- السجدة33- الأحزاب
34- سبأ35- فاطر36- يس
37- الصافات38- ص39- الزمر
40- غافر41- فصلت42- الشورى
43- الزخرف44- الدخان45- الجاثية
46- الأحقاف47- محمد48- الفتح
49- الحجرات50- ق51- الذاريات
52- الطور53- النجم54- القمر
55- الرحمن56- الواقعة57- الحديد
58- المجادلة59- الحشر60- الممتحنة
61- الصف62- الجمعة63- المنافقون
64- التغابن65- الطلاق66- التحريم
67- الملك68- القلم69- الحاقة
70- المعارج71- نوح72- الجن
73- المزمل74- المدثر75- القيامة
76- الإنسان77- المرسلات78- النبأ
79- النازعات80- عبس81- التكوير
82- الإنفطار83- المطففين84- الانشقاق
85- البروج86- الطارق87- الأعلى
88- الغاشية89- الفجر90- البلد
91- الشمس92- الليل93- الضحى
94- الشرح95- التين96- العلق
97- القدر98- البينة99- الزلزلة
100- العاديات101- القارعة102- التكاثر
103- العصر104- الهمزة105- الفيل
106- قريش107- الماعون108- الكوثر
109- الكافرون110- النصر111- المسد
112- الإخلاص113- الفلق114- الناس