Quran with Chichewa translation - Surah Yunus ayat 71 - يُونس - Page - Juz 11
﴿۞ وَٱتۡلُ عَلَيۡهِمۡ نَبَأَ نُوحٍ إِذۡ قَالَ لِقَوۡمِهِۦ يَٰقَوۡمِ إِن كَانَ كَبُرَ عَلَيۡكُم مَّقَامِي وَتَذۡكِيرِي بِـَٔايَٰتِ ٱللَّهِ فَعَلَى ٱللَّهِ تَوَكَّلۡتُ فَأَجۡمِعُوٓاْ أَمۡرَكُمۡ وَشُرَكَآءَكُمۡ ثُمَّ لَا يَكُنۡ أَمۡرُكُمۡ عَلَيۡكُمۡ غُمَّةٗ ثُمَّ ٱقۡضُوٓاْ إِلَيَّ وَلَا تُنظِرُونِ ﴾
[يُونس: 71]
﴿واتل عليهم نبأ نوح إذ قال لقومه ياقوم إن كان كبر عليكم﴾ [يُونس: 71]
Khaled Ibrahim Betala “Ndipo awerengere (molakatula) nkhani za Nuh pamene adanena kwa anthu ake: “E inu anthu anga! Ngati kukhala kwanga pamodzi ndi inu ndi kukumbutsa kwanga Ayah za Allah kukukukulirani, ine ndatsamira kwa Allah (sindisiya ntchito yangayi). Choncho sonkhanitsani zinthu zanu pamodzi ndi milungu yanuyo; (sonkhanani kuti mundichitire choipa, ine sindilabadira chilichonse). Ndipo chinthu chanucho chisabisike kwa inu, (chitani moonekera. Ine sinditekeseka ndi chilichonse). Kenako chitani pa ine (chimene mufuna kuchita) ndipo musandipatse danga |