Quran with Chichewa translation - Surah Hud ayat 40 - هُود - Page - Juz 12
﴿حَتَّىٰٓ إِذَا جَآءَ أَمۡرُنَا وَفَارَ ٱلتَّنُّورُ قُلۡنَا ٱحۡمِلۡ فِيهَا مِن كُلّٖ زَوۡجَيۡنِ ٱثۡنَيۡنِ وَأَهۡلَكَ إِلَّا مَن سَبَقَ عَلَيۡهِ ٱلۡقَوۡلُ وَمَنۡ ءَامَنَۚ وَمَآ ءَامَنَ مَعَهُۥٓ إِلَّا قَلِيلٞ ﴾
[هُود: 40]
﴿حتى إذا جاء أمرنا وفار التنور قلنا احمل فيها من كل زوجين﴾ [هُود: 40]
Khaled Ibrahim Betala “Kufikira pamene lidadza lamulo lathu, madzi naphulika mu uvuni, (chomwe chidali chisonyezo cha Nuh chosonyeza kudza kwa lamulo loona kwa anthu ake) tidamuuza (kuti): “Kweza m’menemo (m’chombo) mtundu uliwonse (wa nyama), ziwiriziwiri, (yaikazi ndi yaimuna), ndi anthu a kubanja lako kupatula omwe chiweruzo (cha Allah) chatsimikizidwa pa iwo (kuti aonongeke), ndipo (atengenso onse) amene akhulupirira.” Komatu ndi ochepa kwambiri amene adakhulupirira pamodzi ndi iye |