Quran with Chichewa translation - Surah Yusuf ayat 37 - يُوسُف - Page - Juz 12
﴿قَالَ لَا يَأۡتِيكُمَا طَعَامٞ تُرۡزَقَانِهِۦٓ إِلَّا نَبَّأۡتُكُمَا بِتَأۡوِيلِهِۦ قَبۡلَ أَن يَأۡتِيَكُمَاۚ ذَٰلِكُمَا مِمَّا عَلَّمَنِي رَبِّيٓۚ إِنِّي تَرَكۡتُ مِلَّةَ قَوۡمٖ لَّا يُؤۡمِنُونَ بِٱللَّهِ وَهُم بِٱلۡأٓخِرَةِ هُمۡ كَٰفِرُونَ ﴾
[يُوسُف: 37]
﴿قال لا يأتيكما طعام ترزقانه إلا نبأتكما بتأويله قبل أن يأتيكما ذلكما﴾ [يُوسُف: 37]
Khaled Ibrahim Betala “(Yûsuf) adati: “(Kupyolera mu uneneri umene ndapatsidwa ndingathe kukumasulirani maloto anuwa ndi zinthu zina zobisika kwa inu), sichikudzerani chakudya cha mtundu uliwonse choti mungapatsidwe koma ndikhala nditakumasulirani tanthauzo lake chisanakufikeni; (ngati mukufunadi ndikuchitirani zimenezi). Izi ndi zina mwa zomwe Mbuye wanga wandiphunzitsa. Ndithudi, ine ndasiya njira za anthu osakhulupirira Allah ndiponso omwe akukana za tsiku la chimaliziro.” |