×

Chikakhala chipupa chija, eni ake adali ana awiri a masiye amene amakhala 18:82 Chichewa translation

Quran infoChichewaSurah Al-Kahf ⮕ (18:82) ayat 82 in Chichewa

18:82 Surah Al-Kahf ayat 82 in Chichewa (نيانجا)

Quran with Chichewa translation - Surah Al-Kahf ayat 82 - الكَهف - Page - Juz 16

﴿وَأَمَّا ٱلۡجِدَارُ فَكَانَ لِغُلَٰمَيۡنِ يَتِيمَيۡنِ فِي ٱلۡمَدِينَةِ وَكَانَ تَحۡتَهُۥ كَنزٞ لَّهُمَا وَكَانَ أَبُوهُمَا صَٰلِحٗا فَأَرَادَ رَبُّكَ أَن يَبۡلُغَآ أَشُدَّهُمَا وَيَسۡتَخۡرِجَا كَنزَهُمَا رَحۡمَةٗ مِّن رَّبِّكَۚ وَمَا فَعَلۡتُهُۥ عَنۡ أَمۡرِيۚ ذَٰلِكَ تَأۡوِيلُ مَا لَمۡ تَسۡطِع عَّلَيۡهِ صَبۡرٗا ﴾
[الكَهف: 82]

Chikakhala chipupa chija, eni ake adali ana awiri a masiye amene amakhala mu mzinda uja ndipo pansi pa chipupacho padali chuma chawo. Ndipo bambo wawo adali munthu wabwino motero Ambuye wako adafuna kuti anawo akule kuti adzatulutse okha chuma chawo ngati chifundo chochokera kwa Ambuye wako. Ine sindidachite zimenezi mwachifuniro changa ayi. Limeneli ndilo tanthauzo lake la zinthu zimene umalephera kupirira nazo

❮ Previous Next ❯

ترجمة: وأما الجدار فكان لغلامين يتيمين في المدينة وكان تحته كنـز لهما وكان, باللغة نيانجا

﴿وأما الجدار فكان لغلامين يتيمين في المدينة وكان تحته كنـز لهما وكان﴾ [الكَهف: 82]

Khaled Ibrahim Betala
““Tsopano chipupa chija, chidali cha ana awiri amasiye mu mzindamo; ndipo pansi pake padali chuma chawo (chimene adawasiira bambo wawo) ndipo tate wawo adali munthu wabwino choncho Mbuye wako adafuna kuti akule misinkhu yawo ndipo adzadzitulutsire chuma chawocho; ichi ndi chifundo chochokera kwa Mbuye wako. Ndipo ine sindidachite zinthu zimenezi mwandekha. Limenelo ndilo tanthauzo la zomwe sudathe kupirira nazo.”
❮ Previous Next ❯

Verse in more languages

Transliteration Bangla Bosnian German English Persian French Hindi Indonesian Kazakh Dutch Russian Spanish Turkish Urdu Uzbek