Quran with Chichewa translation - Surah Al-Baqarah ayat 229 - البَقَرَة - Page - Juz 2
﴿ٱلطَّلَٰقُ مَرَّتَانِۖ فَإِمۡسَاكُۢ بِمَعۡرُوفٍ أَوۡ تَسۡرِيحُۢ بِإِحۡسَٰنٖۗ وَلَا يَحِلُّ لَكُمۡ أَن تَأۡخُذُواْ مِمَّآ ءَاتَيۡتُمُوهُنَّ شَيۡـًٔا إِلَّآ أَن يَخَافَآ أَلَّا يُقِيمَا حُدُودَ ٱللَّهِۖ فَإِنۡ خِفۡتُمۡ أَلَّا يُقِيمَا حُدُودَ ٱللَّهِ فَلَا جُنَاحَ عَلَيۡهِمَا فِيمَا ٱفۡتَدَتۡ بِهِۦۗ تِلۡكَ حُدُودُ ٱللَّهِ فَلَا تَعۡتَدُوهَاۚ وَمَن يَتَعَدَّ حُدُودَ ٱللَّهِ فَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلظَّٰلِمُونَ ﴾
[البَقَرَة: 229]
﴿الطلاق مرتان فإمساك بمعروف أو تسريح بإحسان ولا يحل لكم أن تأخذوا﴾ [البَقَرَة: 229]
Khaled Ibrahim Betala “Twalaq (mawu achilekaniro cha ukwati omwe akupereka mwayi kwa mwamuna kubwereranso kwa mkazi wake), ndi omwe anenedwa kawiri. Kenako amkhazike (mkaziyo) mwa ubwino (ngati afuna kubwererana naye) kapena alekane mwa ubwino (ngati atafunadi kumleka. Ndipo sangathe kubwererana naye ngati atamunenera kachitatu mawu achilekano pokhapokha atakwatiwa kaye ndi mwamuna wina ndi kusiidwa ndi mwamunayo). Ndipo sizili zololedwa kwa inu kuti mutenge (kulanda) chilichonse chimene mudawapatsa (akazi anu) pokhapokha (onse awiri) ngati akuopa kuti satha kusunga malire a Allah (malamulo a Allah). Ngati muopa kuti sasunga malire a Allah, ndiye kuti pamenepo pakhala popanda tchimo kwa iwo (mwamuna woyamba ndi mkaziyu) kulandira (kapena kupereka) chodziombolera mkazi. Awa ndiwo malire a Allah; choncho musawalumphe. Ndipo amene alumphe malire a Allah (powaswa), iwowo ndiwo anthu ochita zoipa |