Quran with Chichewa translation - Surah Al-Baqarah ayat 25 - البَقَرَة - Page - Juz 1
﴿وَبَشِّرِ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ أَنَّ لَهُمۡ جَنَّٰتٖ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُۖ كُلَّمَا رُزِقُواْ مِنۡهَا مِن ثَمَرَةٖ رِّزۡقٗا قَالُواْ هَٰذَا ٱلَّذِي رُزِقۡنَا مِن قَبۡلُۖ وَأُتُواْ بِهِۦ مُتَشَٰبِهٗاۖ وَلَهُمۡ فِيهَآ أَزۡوَٰجٞ مُّطَهَّرَةٞۖ وَهُمۡ فِيهَا خَٰلِدُونَ ﴾
[البَقَرَة: 25]
﴿وبشر الذين آمنوا وعملوا الصالحات أن لهم جنات تجري من تحتها الأنهار﴾ [البَقَرَة: 25]
Khaled Ibrahim Betala “Ndipo auze nkhani yabwino amene akhulupirira nachita ntchito zabwino (molungama) kuti ndithu adzalandira minda ya mtendere momwe mitsinje ikuyenda pansi pake (ndi patsogolo pake). Nthawi iliyonse kumeneko akapatsidwa zipatso ngati chakudya, adzakhala akunena: “Izi ndizomwe tidapatsidwa kale,” (chifukwa chakuti) adzapatsidwa zipatso zofanana (m’maonekedwe ake ndi zimene adapatsidwapo kale. Koma makomedwe ake ngosiyana). Ndiponso akalandira m’menemo akazi oyeretsedwa (kuuve wamtundu uliwonse); ndipo iwo adzakhala m’menemo nthawi yaitali |