Quran with Chichewa translation - Surah Al-Baqarah ayat 26 - البَقَرَة - Page - Juz 1
﴿۞ إِنَّ ٱللَّهَ لَا يَسۡتَحۡيِۦٓ أَن يَضۡرِبَ مَثَلٗا مَّا بَعُوضَةٗ فَمَا فَوۡقَهَاۚ فَأَمَّا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ فَيَعۡلَمُونَ أَنَّهُ ٱلۡحَقُّ مِن رَّبِّهِمۡۖ وَأَمَّا ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ فَيَقُولُونَ مَاذَآ أَرَادَ ٱللَّهُ بِهَٰذَا مَثَلٗاۘ يُضِلُّ بِهِۦ كَثِيرٗا وَيَهۡدِي بِهِۦ كَثِيرٗاۚ وَمَا يُضِلُّ بِهِۦٓ إِلَّا ٱلۡفَٰسِقِينَ ﴾
[البَقَرَة: 26]
﴿إن الله لا يستحيي أن يضرب مثلا ما بعوضة فما فوقها فأما﴾ [البَقَرَة: 26]
Khaled Ibrahim Betala “Ndithu Allah sachita manyazi kupereka fanizo la udzudzu ndi choposerapo (pa udzudzuwo). Koma amene akhulupirira akuzindikira kuti (fanizolo) ndiloona ndi lochokera kwa Mbuye wawo. Koma amene sadakhulupirire, akunena: “Kodi Allah akufunanji pa fanizo lotereli?” (Allah) amawalekelera ambiri kusokera ndi fanizo lotere, komanso amawaongola ambiri ndi fanizonso lotere. Komatu sawalekelera kusokera nalo kupatula okhawo opandukira chilamulo (Chake) |