Quran with Chichewa translation - Surah Ta-Ha ayat 131 - طه - Page - Juz 16
﴿وَلَا تَمُدَّنَّ عَيۡنَيۡكَ إِلَىٰ مَا مَتَّعۡنَا بِهِۦٓ أَزۡوَٰجٗا مِّنۡهُمۡ زَهۡرَةَ ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَا لِنَفۡتِنَهُمۡ فِيهِۚ وَرِزۡقُ رَبِّكَ خَيۡرٞ وَأَبۡقَىٰ ﴾
[طه: 131]
﴿ولا تمدن عينيك إلى ما متعنا به أزواجا منهم زهرة الحياة الدنيا﴾ [طه: 131]
Khaled Ibrahim Betala “Ndipo usazitong’olere maso ako (mozidololokera zinthu) zimene tawasangalatsa nazo ena mwa anthu pakati pawo; zimenezo nzokongoletsa za moyo wa pa dziko basi, kuti tiwayese mayeso pazimenezo; koma chopatsa cha Mbuye wako (chomwe nchololedwa ngakhale chikhale chochepa) nchabwino kwambiri ndiponso chokhalitsa |