طه (1) Ta Ha |
مَا أَنزَلْنَا عَلَيْكَ الْقُرْآنَ لِتَشْقَىٰ (2) Ife sitidavumbulutse Korani ino kwa iwe ndi cholinga choti uvutike |
إِلَّا تَذْكِرَةً لِّمَن يَخْشَىٰ (3) Koma kuti chikhale chilangizo kwa anthu oopa Mulungu |
تَنزِيلًا مِّمَّنْ خَلَقَ الْأَرْضَ وَالسَّمَاوَاتِ الْعُلَى (4) Ndi chivumbulutso chochokera kwa Iye amene adalenga dziko lapansi ndi kumwamba kwenikweniko |
الرَّحْمَٰنُ عَلَى الْعَرْشِ اسْتَوَىٰ (5) Mwini chisoni chosatha amene adaoneka ali pamwamba pa Mpando wa Chifumu |
لَهُ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَمَا فِي الْأَرْضِ وَمَا بَيْنَهُمَا وَمَا تَحْتَ الثَّرَىٰ (6) Zake ndi zonse zimene zili kumwamba ndi pa dziko lapansi ndi zonse zimene zimakhala m’menemo ndiponso zimene zili pansi pa nthaka |
وَإِن تَجْهَرْ بِالْقَوْلِ فَإِنَّهُ يَعْلَمُ السِّرَّ وَأَخْفَى (7) Ngati iwe utchula mawu mokweza, ndithudi Iye amadziwa chinsinsi ndiponso chobisika |
اللَّهُ لَا إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ ۖ لَهُ الْأَسْمَاءُ الْحُسْنَىٰ (8) Mulungu! Kulibe wina wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye yekha. Ake ndi mayina okongola |
وَهَلْ أَتَاكَ حَدِيثُ مُوسَىٰ (9) Kodi udamva za mbiri ya Mose |
إِذْ رَأَىٰ نَارًا فَقَالَ لِأَهْلِهِ امْكُثُوا إِنِّي آنَسْتُ نَارًا لَّعَلِّي آتِيكُم مِّنْهَا بِقَبَسٍ أَوْ أَجِدُ عَلَى النَّارِ هُدًى (10) Pamene iye adaona moto adawauza abale ake kuti, “Dikirani! Ndithudi ine ndaona moto. Mwina ndikubweretserani muuni kuti ndipeze ulangizi pa motopo.” |
فَلَمَّا أَتَاهَا نُودِيَ يَا مُوسَىٰ (11) Pamene iye adafika pafupi ndi moto, adaitanidwa pomutchula dzina lake kuti, “Oh Mose!” |
إِنِّي أَنَا رَبُّكَ فَاخْلَعْ نَعْلَيْكَ ۖ إِنَّكَ بِالْوَادِ الْمُقَدَّسِ طُوًى (12) “Ndithudi, Ine ndine Ambuye wako! Motero chotsa nsapato zako. Ndithudi iwe uli m’dambo lodalitsika la Tuwa.” |
وَأَنَا اخْتَرْتُكَ فَاسْتَمِعْ لِمَا يُوحَىٰ (13) “Ndipo Ine ndakusankha iwe. Kotero mvetsera chimene chikuvumbulutsidwa kwa iwe.” |
إِنَّنِي أَنَا اللَّهُ لَا إِلَٰهَ إِلَّا أَنَا فَاعْبُدْنِي وَأَقِمِ الصَّلَاةَ لِذِكْرِي (14) Ndithudi Ine ndine Mulungu. Palibe wina wopembedzedwa mwachoonadi koma Ine ndekha motero ndipembedze Ine ndipo pitiriza mapemphero pondikumbukira Ine.” |
إِنَّ السَّاعَةَ آتِيَةٌ أَكَادُ أُخْفِيهَا لِتُجْزَىٰ كُلُّ نَفْسٍ بِمَا تَسْعَىٰ (15) “Ndithudi ola lili nkudza ndipo cholinga changa ndi kulibisa kuti mzimu ulionse udzalipidwe malipiro molingana ndi ntchito zake.” |
فَلَا يَصُدَّنَّكَ عَنْهَا مَن لَّا يُؤْمِنُ بِهَا وَاتَّبَعَ هَوَاهُ فَتَرْدَىٰ (16) “Ndipo usalole kuti munthu amene sakhulupirira za olali ndipo yemwe amachita zimene mtima wake umafuna kuti akusocheretse chifukwa ukhoza kuonongeka.” |
وَمَا تِلْكَ بِيَمِينِكَ يَا مُوسَىٰ (17) “Kodi ndi chiyani chimene chili m’dzanja lako la manja iwe Mose?” |
قَالَ هِيَ عَصَايَ أَتَوَكَّأُ عَلَيْهَا وَأَهُشُّ بِهَا عَلَىٰ غَنَمِي وَلِيَ فِيهَا مَآرِبُ أُخْرَىٰ (18) Iye adati, “Iyi ndi ndodo yanga, ndi iyoyi ine ndimayedzamira ndipo ndimagwetsera masamba akudya nyama zanga. Imeneyi imandithandiza pa ntchito zambiri kuonjezera pa zimenezi.” |
قَالَ أَلْقِهَا يَا مُوسَىٰ (19) Mulungu adati, “Ndodoyo iponye pansi iwe Mose.” |
فَأَلْقَاهَا فَإِذَا هِيَ حَيَّةٌ تَسْعَىٰ (20) Mose adaiponya pansi, ndipo taonani! Iyo idasanduka njoka yoyenda mwaliwiro |
قَالَ خُذْهَا وَلَا تَخَفْ ۖ سَنُعِيدُهَا سِيرَتَهَا الْأُولَىٰ (21) Mulungu adati, “Igwire ndipo usachite mantha ayi. Ife tidzaibwezera monga momwe idalili poyamba.” |
وَاضْمُمْ يَدَكَ إِلَىٰ جَنَاحِكَ تَخْرُجْ بَيْضَاءَ مِنْ غَيْرِ سُوءٍ آيَةً أُخْرَىٰ (22) “Tsopano kanikiza dzanja lako m’khwapa mwako. Ilo lidzasanduka loyera lopanda matenda ngati chizindikiro china.” |
لِنُرِيَكَ مِنْ آيَاتِنَا الْكُبْرَى (23) “Kuti tikusonyeze zizindikiro zathu zazikulu.” |
اذْهَبْ إِلَىٰ فِرْعَوْنَ إِنَّهُ طَغَىٰ (24) “Pita kwa Farawo! Ndithudi iye wadumpha malire onse.” |
قَالَ رَبِّ اشْرَحْ لِي صَدْرِي (25) Mose adati, “Ambuye tsekulani chifuwa changa” |
وَيَسِّرْ لِي أَمْرِي (26) “Ndipo pepukitsani ntchito yanga.” |
وَاحْلُلْ عُقْدَةً مِّن لِّسَانِي (27) “Masulani lilime langa ku chibwibwi.” |
يَفْقَهُوا قَوْلِي (28) “Kuti anthu azindikire zonena zanga.” |
وَاجْعَل لِّي وَزِيرًا مِّنْ أَهْلِي (29) “Ndipo ndisankhileni munthu wondithandiza kuchokera ku banja langa.” |
هَارُونَ أَخِي (30) “Aroni m’bale wanga.” |
اشْدُدْ بِهِ أَزْرِي (31) “Onjezereni mphamvu zanga ndi iye.” |
وَأَشْرِكْهُ فِي أَمْرِي (32) “Ndipo muloleni nayenso kugwira ntchito yanga.” |
كَيْ نُسَبِّحَكَ كَثِيرًا (33) “Kuti tizikulemekezani kwambiri.” |
وَنَذْكُرَكَ كَثِيرًا (34) “Ndi kukukumbukirani kwambiri.” |
إِنَّكَ كُنتَ بِنَا بَصِيرًا (35) “Ndithudi! Inu muli kutiona nthawi zonse.” |
قَالَ قَدْ أُوتِيتَ سُؤْلَكَ يَا مُوسَىٰ (36) Mulungu adati, “Pempho lako lalandiridwa, iwe Mose.” |
وَلَقَدْ مَنَنَّا عَلَيْكَ مَرَّةً أُخْرَىٰ (37) “Ndithudi Ife tidakuonetsa chifundo chathu nthawi ina.” |
إِذْ أَوْحَيْنَا إِلَىٰ أُمِّكَ مَا يُوحَىٰ (38) “Pamene tidawauza Amayi ako mawu athu.” |
أَنِ اقْذِفِيهِ فِي التَّابُوتِ فَاقْذِفِيهِ فِي الْيَمِّ فَلْيُلْقِهِ الْيَمُّ بِالسَّاحِلِ يَأْخُذْهُ عَدُوٌّ لِّي وَعَدُوٌّ لَّهُ ۚ وَأَلْقَيْتُ عَلَيْكَ مَحَبَّةً مِّنِّي وَلِتُصْنَعَ عَلَىٰ عَيْنِي (39) Ponena kuti, “Ika mwana wako m’bokosi ndipo umuponye mu mtsinje ndipo mtsinje udzamulavula iye pa mtunda ndipo adzatoledwa ndi mdani wanga ndiponso ndi mdani wake. Ndipo Ine ndidaonetsa chikondi changa pa iwe kuti uleredwa moyang’aniridwa ndi Ine.” |
إِذْ تَمْشِي أُخْتُكَ فَتَقُولُ هَلْ أَدُلُّكُمْ عَلَىٰ مَن يَكْفُلُهُ ۖ فَرَجَعْنَاكَ إِلَىٰ أُمِّكَ كَيْ تَقَرَّ عَيْنُهَا وَلَا تَحْزَنَ ۚ وَقَتَلْتَ نَفْسًا فَنَجَّيْنَاكَ مِنَ الْغَمِّ وَفَتَنَّاكَ فُتُونًا ۚ فَلَبِثْتَ سِنِينَ فِي أَهْلِ مَدْيَنَ ثُمَّ جِئْتَ عَلَىٰ قَدَرٍ يَا مُوسَىٰ (40) “Ndipo pamene mlongo wako adapita kwa iwo ndi kunena kuti, Kodi ndikusonyezeni Mayi amene akhoza kumusamala iye? M’menemo ndi mmene tidakubwezera kwa Amayi ako kuti mtima wawo ukhoza kukhazikika ndipo kuti asakhumudwe. Ndipo pamene iwe udapha munthu, Ife tidakupulumutsa ku mavuto ako, ndipo tidakuyesa ndi mayeso ena. Iwe udakhala pakati pa anthu a ku Midiyani zaka zambiri ndipo pomaliza, iwe Mose, udabwera kuno monga momwe zidakonzedwera.” |
وَاصْطَنَعْتُكَ لِنَفْسِي (41) “Ine ndakusankha iwe kuti unditumikire Ine.” |
اذْهَبْ أَنتَ وَأَخُوكَ بِآيَاتِي وَلَا تَنِيَا فِي ذِكْرِي (42) “Pita iwe ndi m’bale wako ndi zizindikiro zanga ndipo musatope pondikumbukira Ine.” |
اذْهَبَا إِلَىٰ فِرْعَوْنَ إِنَّهُ طَغَىٰ (43) “Pitani, nonsenu, kwa Farawo yemwe wadumpha malire.” |
فَقُولَا لَهُ قَوْلًا لَّيِّنًا لَّعَلَّهُ يَتَذَكَّرُ أَوْ يَخْشَىٰ (44) “Ndipo mukayankhule naye ndi mawu oleza kuti mwina akhoza kumva chenjezo kapena kuopa Mulungu.” |
قَالَا رَبَّنَا إِنَّنَا نَخَافُ أَن يَفْرُطَ عَلَيْنَا أَوْ أَن يَطْغَىٰ (45) Iwo adati, “Ambuye wathu! Ndithudi! Ife tiopa kuti abweretsa chilango chake msanga kapena achita zoipa zambiri kwa ife.” |
قَالَ لَا تَخَافَا ۖ إِنَّنِي مَعَكُمَا أَسْمَعُ وَأَرَىٰ (46) Iye adati, “Musaope! Ndithudi! Ine ndili pamodzi ndi inu. Ine ndimamva zonse ndipo ndimaona.” |
فَأْتِيَاهُ فَقُولَا إِنَّا رَسُولَا رَبِّكَ فَأَرْسِلْ مَعَنَا بَنِي إِسْرَائِيلَ وَلَا تُعَذِّبْهُمْ ۖ قَدْ جِئْنَاكَ بِآيَةٍ مِّن رَّبِّكَ ۖ وَالسَّلَامُ عَلَىٰ مَنِ اتَّبَعَ الْهُدَىٰ (47) “Motero pitani nonse kwa iye ndipo mukati, ‘Ndithudi ife ndife Atumwi Ambuye wako motero aleke ana a Israyeli kuti apite ndi ife ndipo usawazunzenso ayi. Ndithudi ife takubweretsera zizindikiro zochokera kwa Ambuye wako! Ndipo mtendere udzakhala kwa iye amene atsatira langizo.” |
إِنَّا قَدْ أُوحِيَ إِلَيْنَا أَنَّ الْعَذَابَ عَلَىٰ مَن كَذَّبَ وَتَوَلَّىٰ (48) “Ndithudi zavumbulutsidwa kwa ife kuti chilango chake chidzagwa pa iye amene amakana zizindikiro zake ndipo sazimvera ayi.” |
قَالَ فَمَن رَّبُّكُمَا يَا مُوسَىٰ (49) Farawo adati, “Kodi Mose, Ambuye wanu ndani?” |
قَالَ رَبُّنَا الَّذِي أَعْطَىٰ كُلَّ شَيْءٍ خَلْقَهُ ثُمَّ هَدَىٰ (50) Iye adati, “Ambuye wathu ndiye amene adapereka maonekedwe osiyanasiyana ku zolengedwa zake ndipo adazilangiza bwinobwino.” |
قَالَ فَمَا بَالُ الْقُرُونِ الْأُولَىٰ (51) Farawo adati, “Nanga zinali bwanji ndi anthu a masiku akale?” |
قَالَ عِلْمُهَا عِندَ رَبِّي فِي كِتَابٍ ۖ لَّا يَضِلُّ رَبِّي وَلَا يَنسَى (52) Iye adati, “Ambuye wanga yekha ndiye amene adziwa zimenezo ndipo zidalembedwa mu Buku lake. Iye salakwa ndiponso saiwala.” |
الَّذِي جَعَلَ لَكُمُ الْأَرْضَ مَهْدًا وَسَلَكَ لَكُمْ فِيهَا سُبُلًا وَأَنزَلَ مِنَ السَّمَاءِ مَاءً فَأَخْرَجْنَا بِهِ أَزْوَاجًا مِّن نَّبَاتٍ شَتَّىٰ (53) Amene adakupangirani dziko lapansi kukhala ngati kama ndipo adakhazikitsa njira zoti inu muziyendamo ndipo watumiza mvula kuchokera kumwamba. Ndipo ameretsa ndi iyo mitundu yosiyanasiyana ya mbewu |
كُلُوا وَارْعَوْا أَنْعَامَكُمْ ۗ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَآيَاتٍ لِّأُولِي النُّهَىٰ (54) Idyani ndiponso dyetsani ziweto zanu. Ndithudi muzimenezi muli zizindikiro kwa anthu ozindikira |
۞ مِنْهَا خَلَقْنَاكُمْ وَفِيهَا نُعِيدُكُمْ وَمِنْهَا نُخْرِجُكُمْ تَارَةً أُخْرَىٰ (55) Kuchokera ku dothi tidakulengani inu ndipo ndi ku nthaka kumene tidzakubwezerani ndipo kuchoka ku iyo tidzakuutsani kuti mukhalenso ndi moyo kachiwiri |
وَلَقَدْ أَرَيْنَاهُ آيَاتِنَا كُلَّهَا فَكَذَّبَ وَأَبَىٰ (56) Ndithudi tidamulangiza Farawo zizindikiro ndi umboni wathu koma iye adazikana zonse ndipo sadamvere ayi |
قَالَ أَجِئْتَنَا لِتُخْرِجَنَا مِنْ أَرْضِنَا بِسِحْرِكَ يَا مُوسَىٰ (57) Iye adati, “Kodi iwe Mose wadza kudzatichotsa m’dziko lathu ndi matsenga ako?” |
فَلَنَأْتِيَنَّكَ بِسِحْرٍ مِّثْلِهِ فَاجْعَلْ بَيْنَنَا وَبَيْنَكَ مَوْعِدًا لَّا نُخْلِفُهُ نَحْنُ وَلَا أَنتَ مَكَانًا سُوًى (58) “Ndithudi ife tikhoza kukubweretsera matsenga olingana ndi ako. Motero sankha tsiku limene ife kapena iwe siudzalephera kusunga loti tidzakumane iwe ndi ife, pa bwalo pamene tonse tidzakhala ndi mwai wofanana.” |
قَالَ مَوْعِدُكُمْ يَوْمُ الزِّينَةِ وَأَن يُحْشَرَ النَّاسُ ضُحًى (59) Mose adati, “Tsiku lokumana lidzakhale tsiku la chisangalalo ndipo anthu adzasonkhanitsidwe nthawi ya ku m’mawa dzuwa litakwera pang’ono.” |
فَتَوَلَّىٰ فِرْعَوْنُ فَجَمَعَ كَيْدَهُ ثُمَّ أَتَىٰ (60) Farawo adachokapo ndipo adasonkhanitsa a matsenga ake ndipo adadza nawo kwa Mose |
قَالَ لَهُم مُّوسَىٰ وَيْلَكُمْ لَا تَفْتَرُوا عَلَى اللَّهِ كَذِبًا فَيُسْحِتَكُم بِعَذَابٍ ۖ وَقَدْ خَابَ مَنِ افْتَرَىٰ (61) Mose adati kwa iwo, “Tsoka kwa inu! Musapeke mabodza okhudza Mulungu chifukwa akhoza kukuonongani ndi chilango. Ndipo, ndithudi, aliyense amene apeka bodza adzalephera mochititsa manyazi |
فَتَنَازَعُوا أَمْرَهُم بَيْنَهُمْ وَأَسَرُّوا النَّجْوَىٰ (62) Anthu a matsenga adakambirana wina ndi mnzake pa zimene angachite ndipo adasunga zokambirana zawo |
قَالُوا إِنْ هَٰذَانِ لَسَاحِرَانِ يُرِيدَانِ أَن يُخْرِجَاكُم مِّنْ أَرْضِكُم بِسِحْرِهِمَا وَيَذْهَبَا بِطَرِيقَتِكُمُ الْمُثْلَىٰ (63) Iwo adati, “Anthu awiriwa ndi anthu a matsenga amene afuna kuti akuchotseni m’dziko lanu pogwiritsa ntchito matsenga awo ndikugonjetsa mafumu ndi anthu anu aulemu wawo.” |
فَأَجْمِعُوا كَيْدَكُمْ ثُمَّ ائْتُوا صَفًّا ۚ وَقَدْ أَفْلَحَ الْيَوْمَ مَنِ اسْتَعْلَىٰ (64) “Motero konzekani ndipo muime mu mzere. Iwo amene apambane lero, ndithudi, adzakhala opambanadi.” |
قَالُوا يَا مُوسَىٰ إِمَّا أَن تُلْقِيَ وَإِمَّا أَن نَّكُونَ أَوَّلَ مَنْ أَلْقَىٰ (65) Iwo adati, “Iwe Mose! Kodi udzayamba ndiwe kuponya ndodo yako kapena tiyambe ndife kuponya ndodo zathu?” |
قَالَ بَلْ أَلْقُوا ۖ فَإِذَا حِبَالُهُمْ وَعِصِيُّهُمْ يُخَيَّلُ إِلَيْهِ مِن سِحْرِهِمْ أَنَّهَا تَسْعَىٰ (66) Iye adati, “Iyayi. Ponyani zanu poyamba.” Ndipo taona ndi mphamvu ya matsenga awo, zingwe ndi ndodo zawo zidaoneka, m’maso mwa Mose, kuti zinali kuyenda mofulumira |
فَأَوْجَسَ فِي نَفْسِهِ خِيفَةً مُّوسَىٰ (67) Motero Mose adachita mantha mu mtima mwake |
قُلْنَا لَا تَخَفْ إِنَّكَ أَنتَ الْأَعْلَىٰ (68) Koma Ife tidamuuza kuti, “Usaope! Ndithudi iwe udzapambana.” |
وَأَلْقِ مَا فِي يَمِينِكَ تَلْقَفْ مَا صَنَعُوا ۖ إِنَّمَا صَنَعُوا كَيْدُ سَاحِرٍ ۖ وَلَا يُفْلِحُ السَّاحِرُ حَيْثُ أَتَىٰ (69) “Ndipo ponya chimene chili m’dzanja lako la manja. Icho chidzameza zinthu zimene iwo akonza chimene ndi chinyengo cha matsenga ndipo munthu wa matsenga sadzapambana ngakhale atakhala odziwa chotani.” |
فَأُلْقِيَ السَّحَرَةُ سُجَّدًا قَالُوا آمَنَّا بِرَبِّ هَارُونَ وَمُوسَىٰ (70) Anthu a matsenga adagwa pansi kulambira nati, “Ife takhulupirira mwa Ambuye wa Aroni ndi Mose.” |
قَالَ آمَنتُمْ لَهُ قَبْلَ أَنْ آذَنَ لَكُمْ ۖ إِنَّهُ لَكَبِيرُكُمُ الَّذِي عَلَّمَكُمُ السِّحْرَ ۖ فَلَأُقَطِّعَنَّ أَيْدِيَكُمْ وَأَرْجُلَكُم مِّنْ خِلَافٍ وَلَأُصَلِّبَنَّكُمْ فِي جُذُوعِ النَّخْلِ وَلَتَعْلَمُنَّ أَيُّنَا أَشَدُّ عَذَابًا وَأَبْقَىٰ (71) Farawo adati, “Kodi inu mukumukhulupirira iye wopanda chilolezo changa? Ndithudi munthu uyu ayenera kukhala mkulu wanu amene adakuphunzitsani matsenga. Ndithudi ine ndidzadula manja anu ndi miyendo yanu mosiyanitsa ndipo, ndithudi, ine ndidzakupachikani pa thunthu la mtengo wa mgwalangwa. Ndipo, ndithudi, inu mudzadziwa kuti ndani mwa ife amene akhoza kupereka chilango chowawa kwambiri ndiponso chosatha.” |
قَالُوا لَن نُّؤْثِرَكَ عَلَىٰ مَا جَاءَنَا مِنَ الْبَيِّنَاتِ وَالَّذِي فَطَرَنَا ۖ فَاقْضِ مَا أَنتَ قَاضٍ ۖ إِنَّمَا تَقْضِي هَٰذِهِ الْحَيَاةَ الدُّنْيَا (72) Iwo adati, “Ife sitifuna iwe kuposa zizindikiro zimene zadza kwa ife ndi Iye amene adatilenga ife. Kotero iwe chita chimene ufuna kuchita chifukwa iwe ukhoza kulamulira za m’moyo uno zokha.” |
إِنَّا آمَنَّا بِرَبِّنَا لِيَغْفِرَ لَنَا خَطَايَانَا وَمَا أَكْرَهْتَنَا عَلَيْهِ مِنَ السِّحْرِ ۗ وَاللَّهُ خَيْرٌ وَأَبْقَىٰ (73) “Ndithudi ife taika chikhulupiriro chathumwaAmbuyewathukutiatikhululukireifemachimo athu ndiponso pa matsenga amene udatikakamiza kuti tichite ndipo malipiro a Mulungu ndi abwino ndiponso osatha pofanizira ndi malipiro ako.” |
إِنَّهُ مَن يَأْتِ رَبَّهُ مُجْرِمًا فَإِنَّ لَهُ جَهَنَّمَ لَا يَمُوتُ فِيهَا وَلَا يَحْيَىٰ (74) Ndithudi! Aliyense amene adza pamaso pa Ambuye wake ali wamachimo, ndithudi, iye adzaponyedwa ku Gahena kumene sadzakhala ndi moyo kapena imfa |
وَمَن يَأْتِهِ مُؤْمِنًا قَدْ عَمِلَ الصَّالِحَاتِ فَأُولَٰئِكَ لَهُمُ الدَّرَجَاتُ الْعُلَىٰ (75) Koma iye amene adza kwa Iye ndi chikhulupiriro choonadi ndiponso ntchito zabwino, adzakhala ndi ulemerero wapamwamba zedi |
جَنَّاتُ عَدْنٍ تَجْرِي مِن تَحْتِهَا الْأَنْهَارُ خَالِدِينَ فِيهَا ۚ وَذَٰلِكَ جَزَاءُ مَن تَزَكَّىٰ (76) Minda yamuyaya yomwe pansi pake pamayenda mitsinje m’menemo iwo adzakhalamo nthawi zonse. Amenewa ndiwo malipiro a iwo amene amadziyeretsa |
وَلَقَدْ أَوْحَيْنَا إِلَىٰ مُوسَىٰ أَنْ أَسْرِ بِعِبَادِي فَاضْرِبْ لَهُمْ طَرِيقًا فِي الْبَحْرِ يَبَسًا لَّا تَخَافُ دَرَكًا وَلَا تَخْشَىٰ (77) Ndithudi Ife tidamuuza Mose kuti, “Nyamuka nthawi yausiku pamodzi ndi akapolo anga ndipo uwatsekulire njira pakati pa nyanja ndipo usaope kuti akupeza, kapena kumira m’nyanja.” |
فَأَتْبَعَهُمْ فِرْعَوْنُ بِجُنُودِهِ فَغَشِيَهُم مِّنَ الْيَمِّ مَا غَشِيَهُمْ (78) Ndipo Farawo adawatsatira ndi asirikali ake koma madzi adawamiza onse |
وَأَضَلَّ فِرْعَوْنُ قَوْمَهُ وَمَا هَدَىٰ (79) Farawo adasocheretsa anthu ake ndipo sadawatsogolere ayi |
يَا بَنِي إِسْرَائِيلَ قَدْ أَنجَيْنَاكُم مِّنْ عَدُوِّكُمْ وَوَاعَدْنَاكُمْ جَانِبَ الطُّورِ الْأَيْمَنَ وَنَزَّلْنَا عَلَيْكُمُ الْمَنَّ وَالسَّلْوَىٰ (80) oh Inu ana a Israyeli! Ife tidakupulumutsani inu kwa adani anu ndipo tidachita lonjezo ndi inu pambali yakumanja kwa Phiri ndipo tidakutsitsirani manna ndi mbalame zokoma |
كُلُوا مِن طَيِّبَاتِ مَا رَزَقْنَاكُمْ وَلَا تَطْغَوْا فِيهِ فَيَحِلَّ عَلَيْكُمْ غَضَبِي ۖ وَمَن يَحْلِلْ عَلَيْهِ غَضَبِي فَقَدْ هَوَىٰ (81) Idyani zinthu zabwino zimene tidakupatsani ndipo musaswe malamulo chifukwa mkwiyo wanga ungagwe pa inu. Ndipo yense amene umpeza mkwiyo wanga ndithudi watha |
وَإِنِّي لَغَفَّارٌ لِّمَن تَابَ وَآمَنَ وَعَمِلَ صَالِحًا ثُمَّ اهْتَدَىٰ (82) Ndipo, ndithudi, Ine ndimakhululukira aliyense amene alapa, akhulupirira ndipo achita ntchito zabwino ndiponso apitiriza kuzichita |
۞ وَمَا أَعْجَلَكَ عَن قَوْمِكَ يَا مُوسَىٰ (83) “Kodi Mose chakufulumizitsa kubwera kuno ndi kusiya anthu ako ndi chiyani?” |
قَالَ هُمْ أُولَاءِ عَلَىٰ أَثَرِي وَعَجِلْتُ إِلَيْكَ رَبِّ لِتَرْضَىٰ (84) Mose adati, “Iwo ali kumbuyo kwangaku akunditsatira. Ndadza mofulumira kwa Inu, Ambuye, kuti musangalale.” |
قَالَ فَإِنَّا قَدْ فَتَنَّا قَوْمَكَ مِن بَعْدِكَ وَأَضَلَّهُمُ السَّامِرِيُّ (85) Mulungu adati, “Ndithudi! Ife tawayesa mayeso anthu ako popembedza ng’ombe pamene iwe unachoka ndipo Msamiri wawasocheretsa.” |
فَرَجَعَ مُوسَىٰ إِلَىٰ قَوْمِهِ غَضْبَانَ أَسِفًا ۚ قَالَ يَا قَوْمِ أَلَمْ يَعِدْكُمْ رَبُّكُمْ وَعْدًا حَسَنًا ۚ أَفَطَالَ عَلَيْكُمُ الْعَهْدُ أَمْ أَرَدتُّمْ أَن يَحِلَّ عَلَيْكُمْ غَضَبٌ مِّن رَّبِّكُمْ فَأَخْلَفْتُم مَّوْعِدِي (86) Mose adabwerera kwa anthu ake ndi mkwiyo ndiponso mwachisoni. Iye adati, “Anthu anga! Kodi Ambuye wanu sadakulonjezeni lonjezo labwino? Kodi munaona nthawi ya lonjezo kutalika? Kapena chinali cholinga chanu kuti mkwiyo wa Ambuye wanu udze pa inu ndipo inu muphwanye lonjezo lanu kwa ine?” |
قَالُوا مَا أَخْلَفْنَا مَوْعِدَكَ بِمَلْكِنَا وَلَٰكِنَّا حُمِّلْنَا أَوْزَارًا مِّن زِينَةِ الْقَوْمِ فَقَذَفْنَاهَا فَكَذَٰلِكَ أَلْقَى السَّامِرِيُّ (87) Iwo adati, “Ife sitinaphwanye lonjezo lako pa chifukwa chathu ayi. Koma ife anatinyamulitsa katundu wa anthu, ndolo, ndipo tinaziponya pa moto. Zimenezo ndizo zimene Msamiri anatiuza.” |
فَأَخْرَجَ لَهُمْ عِجْلًا جَسَدًا لَّهُ خُوَارٌ فَقَالُوا هَٰذَا إِلَٰهُكُمْ وَإِلَٰهُ مُوسَىٰ فَنَسِيَ (88) Ndipo iye adawatulutsira iwo chifanizo cha thupi la ng’ombe chimene chidali ndi mawu. Iwo adati, “Uyu ndi mulungu wanu ndi mulungu wa Mose yemwe adamuiwala.” |
أَفَلَا يَرَوْنَ أَلَّا يَرْجِعُ إِلَيْهِمْ قَوْلًا وَلَا يَمْلِكُ لَهُمْ ضَرًّا وَلَا نَفْعًا (89) Kodi iwo sanaone kuti sichidawayankhe china chilichonse ndipo kuti chinalibe mphamvu yowapweteka kapena kuwathandiza iwo |
وَلَقَدْ قَالَ لَهُمْ هَارُونُ مِن قَبْلُ يَا قَوْمِ إِنَّمَا فُتِنتُم بِهِ ۖ وَإِنَّ رَبَّكُمُ الرَّحْمَٰنُ فَاتَّبِعُونِي وَأَطِيعُوا أَمْرِي (90) Ndithudi Aroni adawauza iwo poyamba kuti, “Oh Anthu anga! Inu muli kungoyesedwa nacho ichi koma, ndithudi, Ambuye wanu ndiye Mwini chisoni chosatha motero tsatireni ine ndipo mverani malamulo anga.” |
قَالُوا لَن نَّبْرَحَ عَلَيْهِ عَاكِفِينَ حَتَّىٰ يَرْجِعَ إِلَيْنَا مُوسَىٰ (91) Iwo adati, “Ife sitidzasiya kuchipembedza ichi mpaka pamene Mose adza kwa ife.” |
قَالَ يَا هَارُونُ مَا مَنَعَكَ إِذْ رَأَيْتَهُمْ ضَلُّوا (92) Mose adati, “oh Aroni! Kodi chidakuletsa ndi chiyani kuwatsutsa iwo pamene udaona kuti ali kusochera?” |
أَلَّا تَتَّبِعَنِ ۖ أَفَعَصَيْتَ أَمْرِي (93) “Kuti siunanditsatire ine. Kodi waswa lamulo langa?” |
قَالَ يَا ابْنَ أُمَّ لَا تَأْخُذْ بِلِحْيَتِي وَلَا بِرَأْسِي ۖ إِنِّي خَشِيتُ أَن تَقُولَ فَرَّقْتَ بَيْنَ بَنِي إِسْرَائِيلَ وَلَمْ تَرْقُبْ قَوْلِي (94) Aroni adati, “Mwana wa Amayi anga! Usandikoke ndevu zanga kapena tsitsi langa! Ndithudi! Ine ndidali ndi mantha kuti mwina iwe ukhoza kudzanena kuti, iwe wabzala mpatuko pakati pa ana a Israyeli ndipo siunalemekeze mau anga.” |
قَالَ فَمَا خَطْبُكَ يَا سَامِرِيُّ (95) Mose adati, “Iwe Msamiri, kodi chifukwa chiyani udachita izi?” |
قَالَ بَصُرْتُ بِمَا لَمْ يَبْصُرُوا بِهِ فَقَبَضْتُ قَبْضَةً مِّنْ أَثَرِ الرَّسُولِ فَنَبَذْتُهَا وَكَذَٰلِكَ سَوَّلَتْ لِي نَفْسِي (96) Iye adati, “Ine ndidaona zimene iwo sanali kuona. Motero ine ndidatenga dothi lodzala m’manja kuchokera ku fumbi lochokera ku phazi la Mtumwi ndi kulitaya. Kotero mzimu wanga udandikakamiza.” |
قَالَ فَاذْهَبْ فَإِنَّ لَكَ فِي الْحَيَاةِ أَن تَقُولَ لَا مِسَاسَ ۖ وَإِنَّ لَكَ مَوْعِدًا لَّن تُخْلَفَهُ ۖ وَانظُرْ إِلَىٰ إِلَٰهِكَ الَّذِي ظَلْتَ عَلَيْهِ عَاكِفًا ۖ لَّنُحَرِّقَنَّهُ ثُمَّ لَنَنسِفَنَّهُ فِي الْيَمِّ نَسْفًا (97) Mose adati, “Choka! Ndithudi chilango chako m’moyo uno ndi chakuti udzanena kuti, ‘Musandikhudze.’ Ndithudi iwe uli ndi lonjezo limene siliphwanyidwa ayi. Taona mulungu wako amene wamutumikira ndi mtima wako wonse. Ife tidzaliotcha m’moto ndipo tidzamwaza phulusa lake pa nyanja.” |
إِنَّمَا إِلَٰهُكُمُ اللَّهُ الَّذِي لَا إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ ۚ وَسِعَ كُلَّ شَيْءٍ عِلْمًا (98) Mulungu wanu ndi Mulungu mmodzi yekha. Iye amadziwa chilichonse |
كَذَٰلِكَ نَقُصُّ عَلَيْكَ مِنْ أَنبَاءِ مَا قَدْ سَبَقَ ۚ وَقَدْ آتَيْنَاكَ مِن لَّدُنَّا ذِكْرًا (99) Kotero Ife tili kukufotokozerani mbiri ya zinthu zimene zidachitika kale. Ndithudi takupatsa chikumbutso |
مَّنْ أَعْرَضَ عَنْهُ فَإِنَّهُ يَحْمِلُ يَوْمَ الْقِيَامَةِ وِزْرًا (100) Iwo amene adzachikana ndithudi adzanyamula katundu wolemera wamachimo pa tsiku la kuuka kwa akufa |
خَالِدِينَ فِيهِ ۖ وَسَاءَ لَهُمْ يَوْمَ الْقِيَامَةِ حِمْلًا (101) Iwo adzakhala m’menemo mpaka kalekale ndipo zidzakhala zoipa kwambiri kwa iwo osenza katundu wotereyu tsiku la kuuka kwa kufa |
يَوْمَ يُنفَخُ فِي الصُّورِ ۚ وَنَحْشُرُ الْمُجْرِمِينَ يَوْمَئِذٍ زُرْقًا (102) Tsiku limene lipenga lidzaimbidwa, patsiku limene Ife tidzasonkhanitsa anthu onse ochimwa, maso awo adzakhala obiriwira ndi nkhope zakuda |
يَتَخَافَتُونَ بَيْنَهُمْ إِن لَّبِثْتُمْ إِلَّا عَشْرًا (103) Monong’onezana adzakhala ali nkuyankhulana nati, “Inu simunakhale padziko lapansi kupatula masiku khumi okha.” |
نَّحْنُ أَعْلَمُ بِمَا يَقُولُونَ إِذْ يَقُولُ أَمْثَلُهُمْ طَرِيقَةً إِن لَّبِثْتُمْ إِلَّا يَوْمًا (104) Ife tili kudziwa kwambiri zimene adzayankhula, pamene anthu awo angwiro ndi anzeru adzati, “Inu simunakhale padziko kupatula tsiku limodzi lokha.” |
وَيَسْأَلُونَكَ عَنِ الْجِبَالِ فَقُلْ يَنسِفُهَا رَبِّي نَسْفًا (105) “Ndipo iwo ali kukufunsa za mapiri. Nena, “Ambuye wanga adzawachotsa iwo ndi kuwamwaza ngati fumbi la dothi.” |
فَيَذَرُهَا قَاعًا صَفْصَفًا (106) “Ndipo iye adzawasiya kukhala ngati bwalo lasesese.” |
لَّا تَرَىٰ فِيهَا عِوَجًا وَلَا أَمْتًا (107) “M’menemo sudzaona malo otsika kapena okwera.” |
يَوْمَئِذٍ يَتَّبِعُونَ الدَّاعِيَ لَا عِوَجَ لَهُ ۖ وَخَشَعَتِ الْأَصْوَاتُ لِلرَّحْمَٰنِ فَلَا تَسْمَعُ إِلَّا هَمْسًا (108) Pa tsiku limeneli, anthu adzatsatira woitana wa Mulungu, mopanda chinyengo. Ndipo mawu onse adzachepetsedwa chifukwa cha Mwini chisoni ndipo iwe siudzamva china kupatula mgugu wochepa wa mapazi awo |
يَوْمَئِذٍ لَّا تَنفَعُ الشَّفَاعَةُ إِلَّا مَنْ أَذِنَ لَهُ الرَّحْمَٰنُ وَرَضِيَ لَهُ قَوْلًا (109) Patsiku limeneli, palibe wina amene adzakhala ndi mphamvu yoyankhula m’malo mwawo kupatula yekhayo amene adzalandire chilolezo cha Mwini chisoni ndiponso amene mawu ake ngolandiridwa kwa Iye |
يَعْلَمُ مَا بَيْنَ أَيْدِيهِمْ وَمَا خَلْفَهُمْ وَلَا يُحِيطُونَ بِهِ عِلْمًا (110) Amadziwa zonse zimene zili kutsogolo kwawo ndiponso zimene zili kumbuyo kwawo ndi zimene zili nkudza pamene iwo sadziwa china chilichonse cha Iye |
۞ وَعَنَتِ الْوُجُوهُ لِلْحَيِّ الْقَيُّومِ ۖ وَقَدْ خَابَ مَنْ حَمَلَ ظُلْمًا (111) Ndipo nkhope zonse zidzachepetsedwa pamaso pa Mwini moyo wa nthawi zonse amene amateteza china chilichonse. Ndipo yense amene analakwa, ndithudi, ndi olephera |
وَمَن يَعْمَلْ مِنَ الصَّالِحَاتِ وَهُوَ مُؤْمِنٌ فَلَا يَخَافُ ظُلْمًا وَلَا هَضْمًا (112) Ndipo iye amene achita ntchito zabwino ndipo ndi munthu wokhulupirira, iye sadzaopa kuponderezedwa kapena kumanidwa malipiro |
وَكَذَٰلِكَ أَنزَلْنَاهُ قُرْآنًا عَرَبِيًّا وَصَرَّفْنَا فِيهِ مِنَ الْوَعِيدِ لَعَلَّهُمْ يَتَّقُونَ أَوْ يُحْدِثُ لَهُمْ ذِكْرًا (113) Motero Ife tidatumiza Korani mu Chiarabu ndipo tafotokoza m’menemo mowirikiza machenjezo kuti iwo akhale oopa Mulungu kapena kuti Koraniyo iwapatse chiphunzitso kuchokera mu ilo |
فَتَعَالَى اللَّهُ الْمَلِكُ الْحَقُّ ۗ وَلَا تَعْجَلْ بِالْقُرْآنِ مِن قَبْلِ أَن يُقْضَىٰ إِلَيْكَ وَحْيُهُ ۖ وَقُل رَّبِّ زِدْنِي عِلْمًا (114) Wolemekezeka ndi Mulungu, Mfumu ya choonadi! Ndipo usafulumire kulakatula Korani, chivumbulutso chake chisanathe koma uyenera kunena kuti, “Ambuye ndionjezereni nzeru.” |
وَلَقَدْ عَهِدْنَا إِلَىٰ آدَمَ مِن قَبْلُ فَنَسِيَ وَلَمْ نَجِدْ لَهُ عَزْمًا (115) Ndithudi IfetidachitalonjezondiAdamukalekomaiye adaiwala ndipo sitinapeze chipiriro kwa iye |
وَإِذْ قُلْنَا لِلْمَلَائِكَةِ اسْجُدُوا لِآدَمَ فَسَجَدُوا إِلَّا إِبْلِيسَ أَبَىٰ (116) Pamenepo Ife tidawauza angelo kuti, “Mugwadireni Adamu.” Ndipo onse adamugwadira koma Satana adakana |
فَقُلْنَا يَا آدَمُ إِنَّ هَٰذَا عَدُوٌّ لَّكَ وَلِزَوْجِكَ فَلَا يُخْرِجَنَّكُمَا مِنَ الْجَنَّةِ فَتَشْقَىٰ (117) Ife tidati, “oh iwe Adamu! Ndithudi uyu ndi mdani wako ndiponso mdani wa mkazi wako. Musalole kuti akutulutseni ku Paradiso ndi kukukhazikani m’mavuto.” |
إِنَّ لَكَ أَلَّا تَجُوعَ فِيهَا وَلَا تَعْرَىٰ (118) Ndithudi muli ndi lonjezo lathu kuti kumeneko inu simudzamva njala kapena kukhala wamaliseche |
وَأَنَّكَ لَا تَظْمَأُ فِيهَا وَلَا تَضْحَىٰ (119) Ndiponso inu simudzamva ludzu m’menemo kapena kutentha kwa dzuwa |
فَوَسْوَسَ إِلَيْهِ الشَّيْطَانُ قَالَ يَا آدَمُ هَلْ أَدُلُّكَ عَلَىٰ شَجَرَةِ الْخُلْدِ وَمُلْكٍ لَّا يَبْلَىٰ (120) Koma Satana adamunong’oneza nati, “Oh iwe Adamu! Kodi ndingakulangize mtengo wa moyo wosatha ndiponso ufumu wosatha?” |
فَأَكَلَا مِنْهَا فَبَدَتْ لَهُمَا سَوْآتُهُمَا وَطَفِقَا يَخْصِفَانِ عَلَيْهِمَا مِن وَرَقِ الْجَنَّةِ ۚ وَعَصَىٰ آدَمُ رَبَّهُ فَغَوَىٰ (121) Ndipo onse adadya chipatso cha mumtengo uja kotero udaonekera umaliseche wawo ndipo adayamba kudziveka masamba a m’munda muja. Kotero Adamu adanyoza lamulo la Ambuye wake ndipo adasochera |
ثُمَّ اجْتَبَاهُ رَبُّهُ فَتَابَ عَلَيْهِ وَهَدَىٰ (122) Ndipo Ambuye wake adamusankha iye ndipo adamukhululukira ndi kumutsogolera kunjira yoyenera |
قَالَ اهْبِطَا مِنْهَا جَمِيعًا ۖ بَعْضُكُمْ لِبَعْضٍ عَدُوٌّ ۖ فَإِمَّا يَأْتِيَنَّكُم مِّنِّي هُدًى فَمَنِ اتَّبَعَ هُدَايَ فَلَا يَضِلُّ وَلَا يَشْقَىٰ (123) Mulungu adati, “Chokani inu m’menemo, nonse awiri, ndipo inu mudzakhala adani a wina ndi mnzake. Pamene ulangizi wanga udzavumbulutsidwa kwa inu, iye amene adzautsatira sadzasochera kapena kuona mavuto.” |
وَمَنْ أَعْرَضَ عَن ذِكْرِي فَإِنَّ لَهُ مَعِيشَةً ضَنكًا وَنَحْشُرُهُ يَوْمَ الْقِيَامَةِ أَعْمَىٰ (124) “Koma iye amene safuna kumvera machenjezo anga, ndithudi, adzakhala movutika ndipo tidzamuukitsa ali wakhungu pa tsiku louka kwa akufa.” |
قَالَ رَبِّ لِمَ حَشَرْتَنِي أَعْمَىٰ وَقَدْ كُنتُ بَصِيرًا (125) Iye adzati, “Ambuye wanga! Bwanji mwandiukitsa wakhungu, pamene ine ndidali wopenya?” |
قَالَ كَذَٰلِكَ أَتَتْكَ آيَاتُنَا فَنَسِيتَهَا ۖ وَكَذَٰلِكَ الْيَوْمَ تُنسَىٰ (126) Mulungu adzati, “Chifukwa chakuti pamene chivumbulutso chathu chinadza kwa iwe udachiiwala. Chimodzimodzi tsiku lino nawenso waiwalidwa.” |
وَكَذَٰلِكَ نَجْزِي مَنْ أَسْرَفَ وَلَمْ يُؤْمِن بِآيَاتِ رَبِّهِ ۚ وَلَعَذَابُ الْآخِرَةِ أَشَدُّ وَأَبْقَىٰ (127) Mmenemundimmenetimalipiriramunthu oswa malamulo amene sakhulupirira chivumbulutso cha Ambuye wake. Koma chilango cha m’moyo umene uli nkudza ndi choopsa ndiponso chosatha |
أَفَلَمْ يَهْدِ لَهُمْ كَمْ أَهْلَكْنَا قَبْلَهُم مِّنَ الْقُرُونِ يَمْشُونَ فِي مَسَاكِنِهِمْ ۗ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَآيَاتٍ لِّأُولِي النُّهَىٰ (128) Kodi iwo saona mibadwo ya anthu imene tidaiononga iwo asanadze? Iwo amayenda pakati pa nyumba zimene iwo anali kukhalamo. Ndithudi mu zimenezi muli zizindikiro kwa anthu a nzeru |
وَلَوْلَا كَلِمَةٌ سَبَقَتْ مِن رَّبِّكَ لَكَانَ لِزَامًا وَأَجَلٌ مُّسَمًّى (129) Akadakhala kuti Ambuye wako sadalonjeze ndi kukhazikitsa nthawi, chilango chawo chikanadza kale |
فَاصْبِرْ عَلَىٰ مَا يَقُولُونَ وَسَبِّحْ بِحَمْدِ رَبِّكَ قَبْلَ طُلُوعِ الشَّمْسِ وَقَبْلَ غُرُوبِهَا ۖ وَمِنْ آنَاءِ اللَّيْلِ فَسَبِّحْ وَأَطْرَافَ النَّهَارِ لَعَلَّكَ تَرْضَىٰ (130) Motero pirira pa zimene ali kunena ndipo lemekeza ndi kutamanda Ambuye wako dzuwa lisanatuluke ndiponso lisanalowe. Ndipo muyamike Iye nthawi yausiku ndi yausana kuti iwe udzasangalale |
وَلَا تَمُدَّنَّ عَيْنَيْكَ إِلَىٰ مَا مَتَّعْنَا بِهِ أَزْوَاجًا مِّنْهُمْ زَهْرَةَ الْحَيَاةِ الدُّنْيَا لِنَفْتِنَهُمْ فِيهِ ۚ وَرِزْقُ رَبِّكَ خَيْرٌ وَأَبْقَىٰ (131) Usasirire zinthu zimene tawapatsa anthu chifukwa zimenezi ndi zosangalatsa za m’moyo uno. Ife tingofuna kuwayesa nazo. Koma mphotho ya Ambuye wako ndi yabwino ndipo ndi yosatha |
وَأْمُرْ أَهْلَكَ بِالصَّلَاةِ وَاصْطَبِرْ عَلَيْهَا ۖ لَا نَسْأَلُكَ رِزْقًا ۖ نَّحْنُ نَرْزُقُكَ ۗ وَالْعَاقِبَةُ لِلتَّقْوَىٰ (132) Ndipo lamulira banja lako kupemphera ndipo ukhale wopirira pokwaniritsa mapemphero. Ife sitipempha zinthu kwa iwe koma Ife timakupatsa zofuna zako. Ndipo mapeto abwino ndi a anthu oopa Mulungu |
وَقَالُوا لَوْلَا يَأْتِينَا بِآيَةٍ مِّن رَّبِّهِ ۚ أَوَلَمْ تَأْتِهِم بَيِّنَةُ مَا فِي الصُّحُفِ الْأُولَىٰ (133) Iwo adati, “Bwanji iye satipatsa ife chizindikiro chochokera kwa Ambuye wake?” Kodi iwo sadapatsidwe zizindikiro zambiri zimene zili m’mabuku a kale a Mulungu |
وَلَوْ أَنَّا أَهْلَكْنَاهُم بِعَذَابٍ مِّن قَبْلِهِ لَقَالُوا رَبَّنَا لَوْلَا أَرْسَلْتَ إِلَيْنَا رَسُولًا فَنَتَّبِعَ آيَاتِكَ مِن قَبْلِ أَن نَّذِلَّ وَنَخْزَىٰ (134) Ngati Ife tikadawaononga iwo ndi chilango tisadawatumizire ichi, iwo akadati, “Ambuye wathu! Inu mukadatitumizira Mtumwi, ndithudi, ife tikadatsatira chivumbulutso chanu tisadanyozedwe ndi kuchititsidwa manyazi.” |
قُلْ كُلٌّ مُّتَرَبِّصٌ فَتَرَبَّصُوا ۖ فَسَتَعْلَمُونَ مَنْ أَصْحَابُ الصِّرَاطِ السَّوِيِّ وَمَنِ اهْتَدَىٰ (135) Nena, “onse ali kudikira. Nanunso dikirani ndipo inu mudzadziwa kuti ndani amene adatsatira njira yoyenera ndiponso amene ali otsogozedwa.” |