Quran with Chichewa translation - Surah al-‘Imran ayat 152 - آل عِمران - Page - Juz 4
﴿وَلَقَدۡ صَدَقَكُمُ ٱللَّهُ وَعۡدَهُۥٓ إِذۡ تَحُسُّونَهُم بِإِذۡنِهِۦۖ حَتَّىٰٓ إِذَا فَشِلۡتُمۡ وَتَنَٰزَعۡتُمۡ فِي ٱلۡأَمۡرِ وَعَصَيۡتُم مِّنۢ بَعۡدِ مَآ أَرَىٰكُم مَّا تُحِبُّونَۚ مِنكُم مَّن يُرِيدُ ٱلدُّنۡيَا وَمِنكُم مَّن يُرِيدُ ٱلۡأٓخِرَةَۚ ثُمَّ صَرَفَكُمۡ عَنۡهُمۡ لِيَبۡتَلِيَكُمۡۖ وَلَقَدۡ عَفَا عَنكُمۡۗ وَٱللَّهُ ذُو فَضۡلٍ عَلَى ٱلۡمُؤۡمِنِينَ ﴾
[آل عِمران: 152]
﴿ولقد صدقكم الله وعده إذ تحسونهم بإذنه حتى إذا فشلتم وتنازعتم في﴾ [آل عِمران: 152]
Khaled Ibrahim Betala “Ndithudi, Allah adakutsimikizirani lonjezo lake (lakuti muwagonjetsa adani). Choncho mudali kuwapha mwachilolezo Chake kufikira pamene mudafooka ndikuyamba kukangana za lamulolo, tero mudalinyozera pambuyo pokuonetsani zimene mumazikonda; (pamenepo mpomwe adasiya kukuthangatani). Alipo ena mwa inu amene akukonda dziko lapansi (zamdziko), ndipo alipo ena mwa inu amene akukonda tsiku lachimaliziro. Kenako (Allah) adakuchotsani pa iwo (adakusiitsani kuwamenya osakhulupirirawo) kuti akuyeseni mayeso. Koma Iye tsopano wakukhululukirani. Ndipo Allah ndi mwini kuchita zabwino pa okhulupirira |