Quran with Chichewa translation - Surah al-‘Imran ayat 49 - آل عِمران - Page - Juz 3
﴿وَرَسُولًا إِلَىٰ بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ أَنِّي قَدۡ جِئۡتُكُم بِـَٔايَةٖ مِّن رَّبِّكُمۡ أَنِّيٓ أَخۡلُقُ لَكُم مِّنَ ٱلطِّينِ كَهَيۡـَٔةِ ٱلطَّيۡرِ فَأَنفُخُ فِيهِ فَيَكُونُ طَيۡرَۢا بِإِذۡنِ ٱللَّهِۖ وَأُبۡرِئُ ٱلۡأَكۡمَهَ وَٱلۡأَبۡرَصَ وَأُحۡيِ ٱلۡمَوۡتَىٰ بِإِذۡنِ ٱللَّهِۖ وَأُنَبِّئُكُم بِمَا تَأۡكُلُونَ وَمَا تَدَّخِرُونَ فِي بُيُوتِكُمۡۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَةٗ لَّكُمۡ إِن كُنتُم مُّؤۡمِنِينَ ﴾
[آل عِمران: 49]
﴿ورسولا إلى بني إسرائيل أني قد جئتكم بآية من ربكم أني أخلق﴾ [آل عِمران: 49]
Khaled Ibrahim Betala ““Ndipo (adzamchita kukhala) mneneri kwa ana a Israyeli (adzakhala akuwauza kuti): “Ine ndakudzerani ndi zizindikiro kuchokera kwa Mbuye wanu kuti ndikuumbireni dongo ngati chithunzi chambalame, nkuuzira m’menemo nkukhaladi mbalame mwa chilolezo cha Allah. Ndipo ndichiritsa osapenya chibadwire, ndiwamaangamaanga (chinawa), ndi kuukitsa akufa mwa chilolezo cha Allah. Ndipo ndikuuzani zomwe mudye ndi zimene musunge m’nyumba zanu. Ndithudi, m’zimenezi muli zizindikiro kwa inu ngati mulidi okhulupirira.” |