Quran with Chichewa translation - Surah Saba’ ayat 12 - سَبإ - Page - Juz 22
﴿وَلِسُلَيۡمَٰنَ ٱلرِّيحَ غُدُوُّهَا شَهۡرٞ وَرَوَاحُهَا شَهۡرٞۖ وَأَسَلۡنَا لَهُۥ عَيۡنَ ٱلۡقِطۡرِۖ وَمِنَ ٱلۡجِنِّ مَن يَعۡمَلُ بَيۡنَ يَدَيۡهِ بِإِذۡنِ رَبِّهِۦۖ وَمَن يَزِغۡ مِنۡهُمۡ عَنۡ أَمۡرِنَا نُذِقۡهُ مِنۡ عَذَابِ ٱلسَّعِيرِ ﴾
[سَبإ: 12]
﴿ولسليمان الريح غدوها شهر ورواحها شهر وأسلنا له عين القطر ومن الجن﴾ [سَبإ: 12]
Khaled Ibrahim Betala “Nayenso Sulaiman tidamgonjetsera mphepo (yomwe inkayenda mwa lamulo lake). Mayendedwe amphepoyo inkayenda kuyambira m’mawa mpaka masana ntunda wofanana ndi waulendo wa mwezi umodzi, ndiponso kuyambira masana mpaka madzulo inkayenda ntunda wofanana ndi waulendo wa mwezi umodzi. Ndipo tidamsungunulira kasupe wa mtovu. Ndiponso m’ziwanda (majini) zidaliponso zimene tidam’gonjetsera zomwe zinkam’gwilira ntchito mwa chilolezo cha Mbuye wake (Allah). Ndipo yense mwa iwo wonyoza lamulo Lathu (posiya kumumvera Sulaiman) timulawitsa chilango cha Moto woyaka |