×

سورة سبأ باللغة نيانجا

ترجمات القرآنباللغة نيانجا ⬅ سورة سبأ

ترجمة معاني سورة سبأ باللغة نيانجا - Chichewa

القرآن باللغة نيانجا - سورة سبأ مترجمة إلى اللغة نيانجا، Surah Saba in Chichewa. نوفر ترجمة دقيقة سورة سبأ باللغة نيانجا - Chichewa, الآيات 54 - رقم السورة 34 - الصفحة 428.

بسم الله الرحمن الرحيم

الْحَمْدُ لِلَّهِ الَّذِي لَهُ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَمَا فِي الْأَرْضِ وَلَهُ الْحَمْدُ فِي الْآخِرَةِ ۚ وَهُوَ الْحَكِيمُ الْخَبِيرُ (1)
Kuyamikidwa konse ndi kwa Mulungu Mwini wa chilichonse chakumwamba ndi dziko lapansi ndipo kuyamikidwa konse ndi kwake m’dziko limene lili nkudza. Ndipo Iye ndi waluntha ndi wozindikira
يَعْلَمُ مَا يَلِجُ فِي الْأَرْضِ وَمَا يَخْرُجُ مِنْهَا وَمَا يَنزِلُ مِنَ السَّمَاءِ وَمَا يَعْرُجُ فِيهَا ۚ وَهُوَ الرَّحِيمُ الْغَفُورُ (2)
Iye amadziwa chilichonse chimene chimalowa m’nthaka ndi chilichonse chimene chimatuluka mu iyo ndi chilichonse chimene chimatsika kuchokera kumwamba ndi chimene chimakwera kunka kumwamba. Ndipo Iye ndiye Mwini chifundo ndi Mwini kukhululukira
وَقَالَ الَّذِينَ كَفَرُوا لَا تَأْتِينَا السَّاعَةُ ۖ قُلْ بَلَىٰ وَرَبِّي لَتَأْتِيَنَّكُمْ عَالِمِ الْغَيْبِ ۖ لَا يَعْزُبُ عَنْهُ مِثْقَالُ ذَرَّةٍ فِي السَّمَاوَاتِ وَلَا فِي الْأَرْضِ وَلَا أَصْغَرُ مِن ذَٰلِكَ وَلَا أَكْبَرُ إِلَّا فِي كِتَابٍ مُّبِينٍ (3)
Ndipoiwoamenesakhulupiriraamati,“Olasilidzabwera kwaife.” Nena,“Inde! PaliAmbuyewanga, ameneamadziwa zinthu zosaoneka. Ndithudi, olalo lidzadza kwa inu.” Palibe chinthu cholemera ngati mbewu ya mpiru chimene chimabisika kwa Iye kumwamba kapena pa dziko lapansi kapena chochepera kuposa ichi kapena chachikulu kuposa ichi chifukwa zonse ndi zolembedwa bwino m’Buku
لِّيَجْزِيَ الَّذِينَ آمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ ۚ أُولَٰئِكَ لَهُم مَّغْفِرَةٌ وَرِزْقٌ كَرِيمٌ (4)
KoterokutiIyeakhozakulipiraonseameneamakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino. Awa ndiwo amene adzakhululukidwa ndiponso adzalandira malipiro abwino
وَالَّذِينَ سَعَوْا فِي آيَاتِنَا مُعَاجِزِينَ أُولَٰئِكَ لَهُمْ عَذَابٌ مِّن رِّجْزٍ أَلِيمٌ (5)
Ndipo iwo amene amalimbikira kutsutsa chivumbulutso chathu, awa ndiwo amene chilango chowawa ndi chonyansa chili kuwadikirira
وَيَرَى الَّذِينَ أُوتُوا الْعِلْمَ الَّذِي أُنزِلَ إِلَيْكَ مِن رَّبِّكَ هُوَ الْحَقَّ وَيَهْدِي إِلَىٰ صِرَاطِ الْعَزِيزِ الْحَمِيدِ (6)
Ndipo iwo amene adapatsidwa nzeru amaona kuti chimene chapatsidwa kwa iwe kuchoka kwa Ambuye wako ndi choonadi ndipo chimatsogolera ku njira ya Mwini mphamvu ndi Mwini kuyamikidwa
وَقَالَ الَّذِينَ كَفَرُوا هَلْ نَدُلُّكُمْ عَلَىٰ رَجُلٍ يُنَبِّئُكُمْ إِذَا مُزِّقْتُمْ كُلَّ مُمَزَّقٍ إِنَّكُمْ لَفِي خَلْقٍ جَدِيدٍ (7)
Ndipo iwo amene sakhulupirira amati, “Kodi tingakulangizeni amene amakuuzani kuti pamene inu musanduka dothi mudzalengendwanso kukhala m’badwo watsopano?”
أَفْتَرَىٰ عَلَى اللَّهِ كَذِبًا أَم بِهِ جِنَّةٌ ۗ بَلِ الَّذِينَ لَا يُؤْمِنُونَ بِالْآخِرَةِ فِي الْعَذَابِ وَالضَّلَالِ الْبَعِيدِ (8)
Kodi iye wapeka bodza lokhudza Mulungu kapenaiyendiwamisala? Iyayi! Iwondiamenesakhulupirira m’moyo umene uli nkudza ndipo ali mu chilango chachikulu m’maganizo ndiponso ndi olakwa kwambiri
أَفَلَمْ يَرَوْا إِلَىٰ مَا بَيْنَ أَيْدِيهِمْ وَمَا خَلْفَهُم مِّنَ السَّمَاءِ وَالْأَرْضِ ۚ إِن نَّشَأْ نَخْسِفْ بِهِمُ الْأَرْضَ أَوْ نُسْقِطْ عَلَيْهِمْ كِسَفًا مِّنَ السَّمَاءِ ۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَآيَةً لِّكُلِّ عَبْدٍ مُّنِيبٍ (9)
Kodi iwo saganiza za chimene chili patsogolo pawo ndi chimene chili pambuyo pawo chokhudza zinthu za kumwamba ndi pa dziko lapansi? Ngati Ife titafuna, tidzawachotsa pa dziko kapena kuwabweretsera gulu lochokera kumwamba. Ndithudi muli chiphunzitso mu chimenechi kwa kapolo aliyense amene amatembenukira kwa Mulungu
۞ وَلَقَدْ آتَيْنَا دَاوُودَ مِنَّا فَضْلًا ۖ يَا جِبَالُ أَوِّبِي مَعَهُ وَالطَّيْرَ ۖ وَأَلَنَّا لَهُ الْحَدِيدَ (10)
Ndithudi tidamupatsa Davide zabwino zochokera kwa Ife. Oh inu mapiri! Imbani nyimbo zotamanda pamodzi ndi iye ndipo pamodzi ndi mbalame. Ndipo tidapanga chitsulo kukhala chofewa kwa iye
أَنِ اعْمَلْ سَابِغَاتٍ وَقَدِّرْ فِي السَّرْدِ ۖ وَاعْمَلُوا صَالِحًا ۖ إِنِّي بِمَا تَعْمَلُونَ بَصِيرٌ (11)
Tidati, “Panga majasi okwanira ndipo khazikitsa nthawi yopangira zovala ndipo chita ntchito zabwino. Ndithudi Ine ndili kuona chilichonse chimene umachita.”
وَلِسُلَيْمَانَ الرِّيحَ غُدُوُّهَا شَهْرٌ وَرَوَاحُهَا شَهْرٌ ۖ وَأَسَلْنَا لَهُ عَيْنَ الْقِطْرِ ۖ وَمِنَ الْجِنِّ مَن يَعْمَلُ بَيْنَ يَدَيْهِ بِإِذْنِ رَبِّهِ ۖ وَمَن يَزِغْ مِنْهُمْ عَنْ أَمْرِنَا نُذِقْهُ مِنْ عَذَابِ السَّعِيرِ (12)
Ndipo tidalenga mphepo kukhala yoleza kwa Solomoni imene inali kuyenda ulendo wa mwezi umodzi masana ndi ulendo wa mwezi umodzi usiku. Ndipo tidalenga kasupe amene anali kumutulutsira mkuwa. Ndipo padali majini amene anali kumugwirira ntchito ndi chilolezo chaAmbuye wake ndipo aliyense amene sanali kumvera malamulo athu, tinali kumulanga ndi moto
يَعْمَلُونَ لَهُ مَا يَشَاءُ مِن مَّحَارِيبَ وَتَمَاثِيلَ وَجِفَانٍ كَالْجَوَابِ وَقُدُورٍ رَّاسِيَاتٍ ۚ اعْمَلُوا آلَ دَاوُودَ شُكْرًا ۚ وَقَلِيلٌ مِّنْ عِبَادِيَ الشَّكُورُ (13)
Iwo adamuchitira zonse zimene ankazifuna, malinga ndi zithunzithunzi ndi mbiya zazikulu zothirira maluwa ndi zophikiramo zokhazikika. Thokozani a m’banja la Davide! Koma ochepa mwa akapolo anga ndiwo amathokoza
فَلَمَّا قَضَيْنَا عَلَيْهِ الْمَوْتَ مَا دَلَّهُمْ عَلَىٰ مَوْتِهِ إِلَّا دَابَّةُ الْأَرْضِ تَأْكُلُ مِنسَأَتَهُ ۖ فَلَمَّا خَرَّ تَبَيَّنَتِ الْجِنُّ أَن لَّوْ كَانُوا يَعْلَمُونَ الْغَيْبَ مَا لَبِثُوا فِي الْعَذَابِ الْمُهِينِ (14)
Ndipo pamene tidalamula kuti afe, palibe china chilichonse chimene chidawadziwitsa kuti wafa koma mphutsi imene inali kudya ndodo yake ndipo pamene iye adagwa, majini adadziwa kuti iwo akadadziwa za zinthu zobisika, sakadapitirira kugwira ntchito yowawa yodikira
لَقَدْ كَانَ لِسَبَإٍ فِي مَسْكَنِهِمْ آيَةٌ ۖ جَنَّتَانِ عَن يَمِينٍ وَشِمَالٍ ۖ كُلُوا مِن رِّزْقِ رَبِّكُمْ وَاشْكُرُوا لَهُ ۚ بَلْدَةٌ طَيِّبَةٌ وَرَبٌّ غَفُورٌ (15)
Ndithudi kunali chizindikiro kwa onse a Saba m’chikhalidwe chawo. Minda iwiri ku dzanja lamanja ndi minda iwiri kudzanja lamanzere. Idyani zabwino zochokera kwa Ambuye wanu ndipo mumuyamike Iye. Kwa iye kuli dziko labwino ndiponso ndi Ambuye wokhululukira
فَأَعْرَضُوا فَأَرْسَلْنَا عَلَيْهِمْ سَيْلَ الْعَرِمِ وَبَدَّلْنَاهُم بِجَنَّتَيْهِمْ جَنَّتَيْنِ ذَوَاتَيْ أُكُلٍ خَمْطٍ وَأَثْلٍ وَشَيْءٍ مِّن سِدْرٍ قَلِيلٍ (16)
Koma iwo sadamvere ayi. Kotero ife tidawatumizira madzi osefukira kuchokera ku madamu amene sadathe kuwatseka ndipo m’malo mwa minda yawo iwiri, Ife tidawapatsa minda iwiri yobereka zipatso zowawa ndi mitengo ina ya minga
ذَٰلِكَ جَزَيْنَاهُم بِمَا كَفَرُوا ۖ وَهَلْ نُجَازِي إِلَّا الْكَفُورَ (17)
Ife tidawalanga chifukwa cha kusakhulupirira kwawo ndipo Ife sitilanga wina aliyense koma anthu osathokoza
وَجَعَلْنَا بَيْنَهُمْ وَبَيْنَ الْقُرَى الَّتِي بَارَكْنَا فِيهَا قُرًى ظَاهِرَةً وَقَدَّرْنَا فِيهَا السَّيْرَ ۖ سِيرُوا فِيهَا لَيَالِيَ وَأَيَّامًا آمِنِينَ (18)
Ndipo tidakhazikitsa pakati pawo mizinda imene tidaidalitsa ndi mizinda ina imene imaoneka msanga ndipo tidawakonzera ulendo wosavuta. Yendani mwamtendere usiku ndi usana
فَقَالُوا رَبَّنَا بَاعِدْ بَيْنَ أَسْفَارِنَا وَظَلَمُوا أَنفُسَهُمْ فَجَعَلْنَاهُمْ أَحَادِيثَ وَمَزَّقْنَاهُمْ كُلَّ مُمَزَّقٍ ۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَآيَاتٍ لِّكُلِّ صَبَّارٍ شَكُورٍ (19)
Ndipo iwo adati, “oh Ambuye wathu! Titalikitsireni mitunda yoti tiziyendamo.” Ndipo iwo adzipondereza okha. Kotero Ife tidawasandutsa kukhala nkhaniimeneimakambidwakambidwandipotidawamwaza m’magulumagulu. Ndithudi mu chimenechi muli phunziro kwa aliyense amene amapirira ndi kuthokoza
وَلَقَدْ صَدَّقَ عَلَيْهِمْ إِبْلِيسُ ظَنَّهُ فَاتَّبَعُوهُ إِلَّا فَرِيقًا مِّنَ الْمُؤْمِنِينَ (20)
Ndithudi Satana adakwanitsa zofuna zake pa iwo ndipo iwo adamutsatira iye kupatula gulu limene lidakhulupirira
وَمَا كَانَ لَهُ عَلَيْهِم مِّن سُلْطَانٍ إِلَّا لِنَعْلَمَ مَن يُؤْمِنُ بِالْآخِرَةِ مِمَّنْ هُوَ مِنْهَا فِي شَكٍّ ۗ وَرَبُّكَ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ حَفِيظٌ (21)
Koma iye adalibe ulamuliro pa iwo kupatula kuti Ife tikhoza kuyesa munthu amene amakhulupirira za moyo umene uli nkudza ndi iye amene sakhulupirira za moyowo. Ndipo Ambuye wako amayang’ana chinthu china chilichonse
قُلِ ادْعُوا الَّذِينَ زَعَمْتُم مِّن دُونِ اللَّهِ ۖ لَا يَمْلِكُونَ مِثْقَالَ ذَرَّةٍ فِي السَّمَاوَاتِ وَلَا فِي الْأَرْضِ وَمَا لَهُمْ فِيهِمَا مِن شِرْكٍ وَمَا لَهُ مِنْهُم مِّن ظَهِيرٍ (22)
Nena, “Itanani onse amene mumawapembedza kuonjezera pa Mulungu. Iwo alibe ulamuliro pa chinthu ngakhale chaching’ono cha kumwamba kapena padziko lapansi ndipo iwo alibe gawo lililonse mu izo. Ndipo iye alibe wina aliyense womuthandiza kuchokera pakati pawo
وَلَا تَنفَعُ الشَّفَاعَةُ عِندَهُ إِلَّا لِمَنْ أَذِنَ لَهُ ۚ حَتَّىٰ إِذَا فُزِّعَ عَن قُلُوبِهِمْ قَالُوا مَاذَا قَالَ رَبُّكُمْ ۖ قَالُوا الْحَقَّ ۖ وَهُوَ الْعَلِيُّ الْكَبِيرُ (23)
Palibe dandaulo limene lingamveke kwa Iye kupatula lokhalo lochokera kwa iye amene walandira chilolezo chake. Mpaka pamene mantha adzachotsedwa m’mitima mwawo, iwo adzati, “Kodi ndi chiyani chimene Ambuye wanu walamulira?” Iwo adzati, “Choonadi. Ndipo Iye ndi wapamwamba ndi wamkulu.”
۞ قُلْ مَن يَرْزُقُكُم مِّنَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۖ قُلِ اللَّهُ ۖ وَإِنَّا أَوْ إِيَّاكُمْ لَعَلَىٰ هُدًى أَوْ فِي ضَلَالٍ مُّبِينٍ (24)
Nena, “Kodi ndani amene amakupatsani zabwino kuchokera kumwamba ndi pa dziko lapansi?” Nena: “Mulungu.” Ndithudi mwina ife kapena inu muli pa njira yachilungamo kapena ochimwa zedi
قُل لَّا تُسْأَلُونَ عَمَّا أَجْرَمْنَا وَلَا نُسْأَلُ عَمَّا تَعْمَلُونَ (25)
Nena “Inu simudzafunsidwa za machimo athu ndiponso ife sitidzafunsidwa za zimene mudachita.”
قُلْ يَجْمَعُ بَيْنَنَا رَبُّنَا ثُمَّ يَفْتَحُ بَيْنَنَا بِالْحَقِّ وَهُوَ الْفَتَّاحُ الْعَلِيمُ (26)
Nena, “Ambuye wathu adzatisonkhanitsa tonse pamodzi ndipo pomaliza adzaweruza pa mikangano yathu mwa choonadi ndi mwachilungamo. Iye ndiye amene adzaweruza. Ndipo Iye amadziwa zinthu zonse.”
قُلْ أَرُونِيَ الَّذِينَ أَلْحَقْتُم بِهِ شُرَكَاءَ ۖ كَلَّا ۚ بَلْ هُوَ اللَّهُ الْعَزِيزُ الْحَكِيمُ (27)
Nena, “Ndilangizeni zimene inu muli kuzipembedza kuonjezera pa Mulungu. Iyayi! Iye ndi Mulungu, Mwini mphamvu ndi Mwini nzeru.”
وَمَا أَرْسَلْنَاكَ إِلَّا كَافَّةً لِّلنَّاسِ بَشِيرًا وَنَذِيرًا وَلَٰكِنَّ أَكْثَرَ النَّاسِ لَا يَعْلَمُونَ (28)
Takutumiza iwe kwa anthu a mitundu yonse kuti uwauze uthenga wabwino ndi kuwachenjeza. Koma anthu ambiri sadziwa zimenezi
وَيَقُولُونَ مَتَىٰ هَٰذَا الْوَعْدُ إِن كُنتُمْ صَادِقِينَ (29)
Iwo amati, “Kodi lonjezo ili lidzakwaniritsidwa liti ngati uli kunena zoonadi?”
قُل لَّكُم مِّيعَادُ يَوْمٍ لَّا تَسْتَأْخِرُونَ عَنْهُ سَاعَةً وَلَا تَسْتَقْدِمُونَ (30)
Nena, “Tsiku lanu lidakhazikika kale ndipo inu simungaonjezere kapena kubwezera m’mbuyo ngakhale ola limodzi.”
وَقَالَ الَّذِينَ كَفَرُوا لَن نُّؤْمِنَ بِهَٰذَا الْقُرْآنِ وَلَا بِالَّذِي بَيْنَ يَدَيْهِ ۗ وَلَوْ تَرَىٰ إِذِ الظَّالِمُونَ مَوْقُوفُونَ عِندَ رَبِّهِمْ يَرْجِعُ بَعْضُهُمْ إِلَىٰ بَعْضٍ الْقَوْلَ يَقُولُ الَّذِينَ اسْتُضْعِفُوا لِلَّذِينَ اسْتَكْبَرُوا لَوْلَا أَنتُمْ لَكُنَّا مُؤْمِنِينَ (31)
Ndipo iwo amene sakhulupirira amati, “Ife sitidzakhulupirira mu Buku la Korani kapena mu icho chimene chidadza kale. Ndipo iwe ukadaona pamene anthu ochita zoipa adzaimirira pamaso pa Ambuye wawo ali kudzudzulana wina ndi mnzake! Iwo amene ankati ndi ofoka adzanena kwa anthu opulupudza kuti, “Pakadapanda inu, ndithudi, ife tikadakhala okhulupirira!”
قَالَ الَّذِينَ اسْتَكْبَرُوا لِلَّذِينَ اسْتُضْعِفُوا أَنَحْنُ صَدَدْنَاكُمْ عَنِ الْهُدَىٰ بَعْدَ إِذْ جَاءَكُم ۖ بَلْ كُنتُم مُّجْرِمِينَ (32)
Iwo amene adali onyada adzati kwa iwo amene ankati ndi ofoka kuti, “Kodi ife tinakukanizani kutsatira langizo pamene lidadza kwa inu? Iyayi. Nokha mudachimwa.”
وَقَالَ الَّذِينَ اسْتُضْعِفُوا لِلَّذِينَ اسْتَكْبَرُوا بَلْ مَكْرُ اللَّيْلِ وَالنَّهَارِ إِذْ تَأْمُرُونَنَا أَن نَّكْفُرَ بِاللَّهِ وَنَجْعَلَ لَهُ أَندَادًا ۚ وَأَسَرُّوا النَّدَامَةَ لَمَّا رَأَوُا الْعَذَابَ وَجَعَلْنَا الْأَغْلَالَ فِي أَعْنَاقِ الَّذِينَ كَفَرُوا ۚ هَلْ يُجْزَوْنَ إِلَّا مَا كَانُوا يَعْمَلُونَ (33)
Iwo amene ankati ndi ofoka adzati kwa iwo amene adali onyada, “Iyayi! Inu munkakonza chiwembu usiku ndi usana ndipo mumatiuza ife kuti tisakhulupirire mwa Mulungu koma kukhazikitsa mafano kuonjezera pa Iye.” Ndipo iwo adzabisa kukhumudwa kwawo pamene adzaone chilango ndipo Ife tidzaika magoli m’makosi mwa iwo amene sadakhulupirire. Iwo sadzakhululukidwa pa zimene adachita
وَمَا أَرْسَلْنَا فِي قَرْيَةٍ مِّن نَّذِيرٍ إِلَّا قَالَ مُتْرَفُوهَا إِنَّا بِمَا أُرْسِلْتُم بِهِ كَافِرُونَ (34)
Ife sitidatumizepo Mchenjezi ku mzinda wina uliwonse umene anthu ake opeza bwino sadanenepo mawu oti, “Ndithudiifesitikhulupirirauthengaumenewatumizidwa.”
وَقَالُوا نَحْنُ أَكْثَرُ أَمْوَالًا وَأَوْلَادًا وَمَا نَحْنُ بِمُعَذَّبِينَ (35)
Ndipo iwo adati, “Ife tili ndi chuma chambiri ndiponso ana, kotero ife sitidzalangidwa ayi.”
قُلْ إِنَّ رَبِّي يَبْسُطُ الرِّزْقَ لِمَن يَشَاءُ وَيَقْدِرُ وَلَٰكِنَّ أَكْثَرَ النَّاسِ لَا يَعْلَمُونَ (36)
Nena, “Ndithudi Ambuye wanga amapereka moolowa manja kwa aliyense amene Iye wamufuna ndi monyalapsa kwa aliyense amene Iye wamufuna. Koma anthu ambiri sadziwa.”
وَمَا أَمْوَالُكُمْ وَلَا أَوْلَادُكُم بِالَّتِي تُقَرِّبُكُمْ عِندَنَا زُلْفَىٰ إِلَّا مَنْ آمَنَ وَعَمِلَ صَالِحًا فَأُولَٰئِكَ لَهُمْ جَزَاءُ الضِّعْفِ بِمَا عَمِلُوا وَهُمْ فِي الْغُرُفَاتِ آمِنُونَ (37)
Si chuma kapena ana anu amene adzakufikitsani kufupi ndi Ife koma okhawo amene amakhulupirira ndi kuchita ntchito zabwino. Otere ndiwo amene ali ndi malipiro odzala manja awiri chifukwa cha ntchito zawo ndipo adzakhala mwamtendere pamalo olemekezeka
وَالَّذِينَ يَسْعَوْنَ فِي آيَاتِنَا مُعَاجِزِينَ أُولَٰئِكَ فِي الْعَذَابِ مُحْضَرُونَ (38)
Ndipo onse amene amalimbikira kutsutsa chiphunzitso chathu adzalangidwa
قُلْ إِنَّ رَبِّي يَبْسُطُ الرِّزْقَ لِمَن يَشَاءُ مِنْ عِبَادِهِ وَيَقْدِرُ لَهُ ۚ وَمَا أَنفَقْتُم مِّن شَيْءٍ فَهُوَ يُخْلِفُهُ ۖ وَهُوَ خَيْرُ الرَّازِقِينَ (39)
Nena, “Ndithudi Ambuye wanga amapereka moolowa manja kwa aliyense wa akapolo ake amene wamufuna ndipo amachepetsa za aliyense amene wamufuna. Ndipo chilichonse chimene mupereka, Iye amalipira mowirikiza ndipo Iye ndiye amapereka kwambiri.”
وَيَوْمَ يَحْشُرُهُمْ جَمِيعًا ثُمَّ يَقُولُ لِلْمَلَائِكَةِ أَهَٰؤُلَاءِ إِيَّاكُمْ كَانُوا يَعْبُدُونَ (40)
Patsiku limene adzawasonkhanitsa onse pamodzi ndi kuwafunsa Angelo kuti, “Kodi ndinu amene anthu awa anali kupembedza?”
قَالُوا سُبْحَانَكَ أَنتَ وَلِيُّنَا مِن دُونِهِم ۖ بَلْ كَانُوا يَعْبُدُونَ الْجِنَّ ۖ أَكْثَرُهُم بِهِم مُّؤْمِنُونَ (41)
Angelo adzati, “Ulemerero ukhale kwa Inu! Inu ndinu Mtetezi wathu osati iwo ayi. Iyayi! Iwo anali kupembedza majini ndipo ambiri a iwo anali kukhulupirira mwa iwo.”
فَالْيَوْمَ لَا يَمْلِكُ بَعْضُكُمْ لِبَعْضٍ نَّفْعًا وَلَا ضَرًّا وَنَقُولُ لِلَّذِينَ ظَلَمُوا ذُوقُوا عَذَابَ النَّارِ الَّتِي كُنتُم بِهَا تُكَذِّبُونَ (42)
Kotero patsiku limeneli, iwo sadzakhala ndi mphamvu zothandizana kapena kupwetekana wina ndi mnzake. Ndipo Ife tidzati kwa anthu ochimwa. “Lawani chilango cha moto chimene inu munali kuchikana.”
وَإِذَا تُتْلَىٰ عَلَيْهِمْ آيَاتُنَا بَيِّنَاتٍ قَالُوا مَا هَٰذَا إِلَّا رَجُلٌ يُرِيدُ أَن يَصُدَّكُمْ عَمَّا كَانَ يَعْبُدُ آبَاؤُكُمْ وَقَالُوا مَا هَٰذَا إِلَّا إِفْكٌ مُّفْتَرًى ۚ وَقَالَ الَّذِينَ كَفَرُوا لِلْحَقِّ لَمَّا جَاءَهُمْ إِنْ هَٰذَا إِلَّا سِحْرٌ مُّبِينٌ (43)
Pamene chiphunzitso chathu chomveka chimalalikiridwa kwa iwo, iwo amati, “Uyu ndi munthu amene afuna kukuletsani chipembedzo cha makolo anu.” Ndipo iwo amati, “Ili ndi bodza limene wapeka.” Ndipo anthu osakhulupirira, pamene choonadi chidza kwa iwo amati, “Awa ndi matsenga.”
وَمَا آتَيْنَاهُم مِّن كُتُبٍ يَدْرُسُونَهَا ۖ وَمَا أَرْسَلْنَا إِلَيْهِمْ قَبْلَكَ مِن نَّذِيرٍ (44)
Ife sitidawatumizire mabuku kuti awaphunzitse kapena kuwatumizira Atumwi iwe usanadze ngati wowachenjeza
وَكَذَّبَ الَّذِينَ مِن قَبْلِهِمْ وَمَا بَلَغُوا مِعْشَارَ مَا آتَيْنَاهُمْ فَكَذَّبُوا رُسُلِي ۖ فَكَيْفَ كَانَ نَكِيرِ (45)
Ndipo iwo amene analipo kale iwo asanadze adakana choonadi. Awa sadalandire, ngakhale gawo la chikhumi la zimene tidawapatsa iwo. Komabe pamene iwo adakana Atumwi anga, kodi chilango changa chinali chowawa bwanji
۞ قُلْ إِنَّمَا أَعِظُكُم بِوَاحِدَةٍ ۖ أَن تَقُومُوا لِلَّهِ مَثْنَىٰ وَفُرَادَىٰ ثُمَّ تَتَفَكَّرُوا ۚ مَا بِصَاحِبِكُم مِّن جِنَّةٍ ۚ إِنْ هُوَ إِلَّا نَذِيرٌ لَّكُم بَيْنَ يَدَيْ عَذَابٍ شَدِيدٍ (46)
Nena, “Ine ndili kukufunsani kuti muchite chinthu chimodzi choti muime pamaso pa Mulungu awiriawiri kapena aliyense payekha ndipo muganize painu nokha. M’bale wanu si wamisala ayi. Iye ali kungokuchenjezani chilango chowawa chisanadze.”
قُلْ مَا سَأَلْتُكُم مِّنْ أَجْرٍ فَهُوَ لَكُمْ ۖ إِنْ أَجْرِيَ إِلَّا عَلَى اللَّهِ ۖ وَهُوَ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ شَهِيدٌ (47)
Nena, “Malipiro ena aliwonse amene ndidakufunsani ndi anu chifukwa malipiro anga ali ndi Mulungu ndipo Iye ndi mboni pa zinthu zonse.”
قُلْ إِنَّ رَبِّي يَقْذِفُ بِالْحَقِّ عَلَّامُ الْغُيُوبِ (48)
Nena, “NdithudiAmbuye wanga amanena zoona ndipo ndi Mwini wodziwa zinthu zobisika.”
قُلْ جَاءَ الْحَقُّ وَمَا يُبْدِئُ الْبَاطِلُ وَمَا يُعِيدُ (49)
Nena, “Choonadi chadza ndipo bodza latha ndipo silidzabwereranso.”
قُلْ إِن ضَلَلْتُ فَإِنَّمَا أَضِلُّ عَلَىٰ نَفْسِي ۖ وَإِنِ اهْتَدَيْتُ فَبِمَا يُوحِي إِلَيَّ رَبِّي ۚ إِنَّهُ سَمِيعٌ قَرِيبٌ (50)
Nena, “Ngati ine ndilakwa, ndilakwira mzimu wanga ndipo ngati ndatsatira njira yolungama ndi chifukwa cha zimene Ambuye wanga amavumbulutsa kwa ine. Ndithudi Iye amamva ndipo ali pafupi.”
وَلَوْ تَرَىٰ إِذْ فَزِعُوا فَلَا فَوْتَ وَأُخِذُوا مِن مَّكَانٍ قَرِيبٍ (51)
Ndipo iwe ukadangoona nthawi imene adzachite mantha komabe iwo sadzathawa ndipo iwo adzagwidwa asanapitepatali
وَقَالُوا آمَنَّا بِهِ وَأَنَّىٰ لَهُمُ التَّنَاوُشُ مِن مَّكَانٍ بَعِيدٍ (52)
Ndipoiwoadzati,“Ifetilikukhulupirira.” Kodi kukhulupirira kwawo kudzawathandiza bwanji kuchokera kutali
وَقَدْ كَفَرُوا بِهِ مِن قَبْلُ ۖ وَيَقْذِفُونَ بِالْغَيْبِ مِن مَّكَانٍ بَعِيدٍ (53)
Ndipo iwo sadakhulupirire kale ndipo amanena kuti ndi nkhani za m’maluwa kuchokera kutali
وَحِيلَ بَيْنَهُمْ وَبَيْنَ مَا يَشْتَهُونَ كَمَا فُعِلَ بِأَشْيَاعِهِم مِّن قَبْلُ ۚ إِنَّهُمْ كَانُوا فِي شَكٍّ مُّرِيبٍ (54)
Ndipo chipupa chidzakhazikitsidwa pakati pawo ndi zofuna zawo monga momwe adachitira ndi anthu ena a kale. Ndithudi iwo ndi okayika kwambiri
❮ السورة السابقة السورة التـالية ❯

قراءة المزيد من سور القرآن الكريم :

1- الفاتحة2- البقرة3- آل عمران
4- النساء5- المائدة6- الأنعام
7- الأعراف8- الأنفال9- التوبة
10- يونس11- هود12- يوسف
13- الرعد14- إبراهيم15- الحجر
16- النحل17- الإسراء18- الكهف
19- مريم20- طه21- الأنبياء
22- الحج23- المؤمنون24- النور
25- الفرقان26- الشعراء27- النمل
28- القصص29- العنكبوت30- الروم
31- لقمان32- السجدة33- الأحزاب
34- سبأ35- فاطر36- يس
37- الصافات38- ص39- الزمر
40- غافر41- فصلت42- الشورى
43- الزخرف44- الدخان45- الجاثية
46- الأحقاف47- محمد48- الفتح
49- الحجرات50- ق51- الذاريات
52- الطور53- النجم54- القمر
55- الرحمن56- الواقعة57- الحديد
58- المجادلة59- الحشر60- الممتحنة
61- الصف62- الجمعة63- المنافقون
64- التغابن65- الطلاق66- التحريم
67- الملك68- القلم69- الحاقة
70- المعارج71- نوح72- الجن
73- المزمل74- المدثر75- القيامة
76- الإنسان77- المرسلات78- النبأ
79- النازعات80- عبس81- التكوير
82- الإنفطار83- المطففين84- الانشقاق
85- البروج86- الطارق87- الأعلى
88- الغاشية89- الفجر90- البلد
91- الشمس92- الليل93- الضحى
94- الشرح95- التين96- العلق
97- القدر98- البينة99- الزلزلة
100- العاديات101- القارعة102- التكاثر
103- العصر104- الهمزة105- الفيل
106- قريش107- الماعون108- الكوثر
109- الكافرون110- النصر111- المسد
112- الإخلاص113- الفلق114- الناس