Quran with Chichewa translation - Surah Saba’ ayat 31 - سَبإ - Page - Juz 22
﴿وَقَالَ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لَن نُّؤۡمِنَ بِهَٰذَا ٱلۡقُرۡءَانِ وَلَا بِٱلَّذِي بَيۡنَ يَدَيۡهِۗ وَلَوۡ تَرَىٰٓ إِذِ ٱلظَّٰلِمُونَ مَوۡقُوفُونَ عِندَ رَبِّهِمۡ يَرۡجِعُ بَعۡضُهُمۡ إِلَىٰ بَعۡضٍ ٱلۡقَوۡلَ يَقُولُ ٱلَّذِينَ ٱسۡتُضۡعِفُواْ لِلَّذِينَ ٱسۡتَكۡبَرُواْ لَوۡلَآ أَنتُمۡ لَكُنَّا مُؤۡمِنِينَ ﴾
[سَبإ: 31]
﴿وقال الذين كفروا لن نؤمن بهذا القرآن ولا بالذي بين يديه ولو﴾ [سَبإ: 31]
Khaled Ibrahim Betala “Ndipo amene sadakhulupirire akunena: “Sitiikhulupirira Qur’an iyi, ngakhalenso (mabuku) aja apatsogolo pake.” Ndipo ukadawaona achinyengo pamene azikaimiritsidwa pamaso pa Mbuye wawo, (ukadaona zoopsa zazikulu), uku pakati pawo akubwezerana mawu. Amene adaponderezedwa adzanena kwa amene adadzikweza: “Kukadapanda inu (kutipondereza), tikadakhala okhulupirira.” |