Quran with Chichewa translation - Surah An-Nisa’ ayat 11 - النِّسَاء - Page - Juz 4
﴿يُوصِيكُمُ ٱللَّهُ فِيٓ أَوۡلَٰدِكُمۡۖ لِلذَّكَرِ مِثۡلُ حَظِّ ٱلۡأُنثَيَيۡنِۚ فَإِن كُنَّ نِسَآءٗ فَوۡقَ ٱثۡنَتَيۡنِ فَلَهُنَّ ثُلُثَا مَا تَرَكَۖ وَإِن كَانَتۡ وَٰحِدَةٗ فَلَهَا ٱلنِّصۡفُۚ وَلِأَبَوَيۡهِ لِكُلِّ وَٰحِدٖ مِّنۡهُمَا ٱلسُّدُسُ مِمَّا تَرَكَ إِن كَانَ لَهُۥ وَلَدٞۚ فَإِن لَّمۡ يَكُن لَّهُۥ وَلَدٞ وَوَرِثَهُۥٓ أَبَوَاهُ فَلِأُمِّهِ ٱلثُّلُثُۚ فَإِن كَانَ لَهُۥٓ إِخۡوَةٞ فَلِأُمِّهِ ٱلسُّدُسُۚ مِنۢ بَعۡدِ وَصِيَّةٖ يُوصِي بِهَآ أَوۡ دَيۡنٍۗ ءَابَآؤُكُمۡ وَأَبۡنَآؤُكُمۡ لَا تَدۡرُونَ أَيُّهُمۡ أَقۡرَبُ لَكُمۡ نَفۡعٗاۚ فَرِيضَةٗ مِّنَ ٱللَّهِۗ إِنَّ ٱللَّهَ كَانَ عَلِيمًا حَكِيمٗا ﴾
[النِّسَاء: 11]
﴿يوصيكم الله في أولادكم للذكر مثل حظ الأنثيين فإن كن نساء فوق﴾ [النِّسَاء: 11]
Khaled Ibrahim Betala “Allah akukulamulani za ana anu achimuna apate gawo lolingana ndi gawo la akazi awiri. Ngati akaziwo ali (opitilira) awiri, ndiye kuti adzalandira zigawo ziwiri mwa zigawo zitatu (/3) za (chumacho) chimene wasiya (womwalira), ngati mwana wamkazi ndi mmodzi, apatsidwe gawo limodzi mwa magawo awiri (1/2), naonso makolo ake awiri aliyense wa iwo alandile gawo limodzi mwa magawo asanu ndi limodzi (1/6) achuma chosiidwacho, ngati (womwalirayo) wasiya mwana (kapena mdzukulu). Koma ngati sadasiye mwana, ndipo makolo ake awiri ndiwo awasiira, ndiye kuti mayi wake alandire gawo limodzi mwamagawo atatu (1/3) achumacho, (ndipo bambo alandire 2/3). Ngati wakufayo wasiya abale, ndiye kuti mayi wake apeza gawo limodzi mwa magawo asanu ndi limodzi (1/6) achumacho. (Kugawa chumaku kuchitike) atachotsapo chimene iye adalamulira kuti adzachipereke kwakutikwakuti, kapena kulipira ngongole (zake). Atate anu ndi ana anu, simudziwa inu kuti ndani mwa iwo amene ali ndi chithandizo chapafupi kwa inu. Amenewa ndi malamulo omwe akhazikitsidwa ndi Allah. Ndithudi, Allah ngodziwa kwambiri, Ngwanzeru zakuya |