Quran with Chichewa translation - Surah An-Nisa’ ayat 12 - النِّسَاء - Page - Juz 4
﴿۞ وَلَكُمۡ نِصۡفُ مَا تَرَكَ أَزۡوَٰجُكُمۡ إِن لَّمۡ يَكُن لَّهُنَّ وَلَدٞۚ فَإِن كَانَ لَهُنَّ وَلَدٞ فَلَكُمُ ٱلرُّبُعُ مِمَّا تَرَكۡنَۚ مِنۢ بَعۡدِ وَصِيَّةٖ يُوصِينَ بِهَآ أَوۡ دَيۡنٖۚ وَلَهُنَّ ٱلرُّبُعُ مِمَّا تَرَكۡتُمۡ إِن لَّمۡ يَكُن لَّكُمۡ وَلَدٞۚ فَإِن كَانَ لَكُمۡ وَلَدٞ فَلَهُنَّ ٱلثُّمُنُ مِمَّا تَرَكۡتُمۚ مِّنۢ بَعۡدِ وَصِيَّةٖ تُوصُونَ بِهَآ أَوۡ دَيۡنٖۗ وَإِن كَانَ رَجُلٞ يُورَثُ كَلَٰلَةً أَوِ ٱمۡرَأَةٞ وَلَهُۥٓ أَخٌ أَوۡ أُخۡتٞ فَلِكُلِّ وَٰحِدٖ مِّنۡهُمَا ٱلسُّدُسُۚ فَإِن كَانُوٓاْ أَكۡثَرَ مِن ذَٰلِكَ فَهُمۡ شُرَكَآءُ فِي ٱلثُّلُثِۚ مِنۢ بَعۡدِ وَصِيَّةٖ يُوصَىٰ بِهَآ أَوۡ دَيۡنٍ غَيۡرَ مُضَآرّٖۚ وَصِيَّةٗ مِّنَ ٱللَّهِۗ وَٱللَّهُ عَلِيمٌ حَلِيمٞ ﴾
[النِّسَاء: 12]
﴿ولكم نصف ما ترك أزواجكم إن لم يكن لهن ولد فإن كان﴾ [النِّسَاء: 12]
Khaled Ibrahim Betala “Inunso mupata gawo limodzi mwa magawo awiri (/2) achuma chimene akazi anu asiya ngati alibe mwana (kapena mdzukulu), ngati asiya mwana ndiye kuti inu mupata gawo limodzi m’magawo anayi (1/4) achuma chosiidwacho mutachotsapo zomwe adalamula kuti zipite kwakutikwakuti kapena ngongole zake, naonso akazi anu apata gawo limodzi m’magawo anayi (1/4) pa chuma chomwe mwasiya, ngati mulibe mwana (ndi mdzukulu). Koma ngati mwasiya mwana (ndi mdzukulu), (akaziwo) apata gawo limodzi m’magawo asanu ndi atatu (1/8) pa chuma chomwe mwasiya mutachotsapo chomwe mudanena kuti chipite kwakutikwakuti kapena kulipira ngongole (zanu). Ngati mwamuna kapena mkazi alowedwa m’malo pachuma pomwe alibe mwana (ndi mdzukulu) ngakhale makolo awiri, koma ali naye m’bale wake (wakuchikazi) kapena mlongo wake (wakuchikazinso) aliyense wa iwo apata gawo limodzi m’magawo asanu ndi limodzi (1/6). Ndipo ngati ali ochulukirapo, ndiye kuti agawirana gawo limodzi m’magawo atatu (1/3) a chumacho pambuyo pochotsapo chomwe chidanenedwa kuti chipita kwakutikwakuti kapena kulipira ngongole, popanda kupereka mavuto. Awa ndi malamulo ofunika omwe achokera kwa Allah. Ndipo Allah Ngodziwa kwambiri (pokhazikitsa malamulo); Woleza (pa akapolo Ake) |