Quran with Chichewa translation - Surah Muhammad ayat 20 - مُحمد - Page - Juz 26
﴿وَيَقُولُ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لَوۡلَا نُزِّلَتۡ سُورَةٞۖ فَإِذَآ أُنزِلَتۡ سُورَةٞ مُّحۡكَمَةٞ وَذُكِرَ فِيهَا ٱلۡقِتَالُ رَأَيۡتَ ٱلَّذِينَ فِي قُلُوبِهِم مَّرَضٞ يَنظُرُونَ إِلَيۡكَ نَظَرَ ٱلۡمَغۡشِيِّ عَلَيۡهِ مِنَ ٱلۡمَوۡتِۖ فَأَوۡلَىٰ لَهُمۡ ﴾
[مُحمد: 20]
﴿ويقول الذين آمنوا لولا نـزلت سورة فإذا أنـزلت سورة محكمة وذكر فيها﴾ [مُحمد: 20]
Khaled Ibrahim Betala “Ndipo amene akhulupirira akunena (chifukwa cha mazunzo omwe amawapeza kuchokera kwa osakhulupirira kuti) kodi nchifukwa ninji siikuvumbulutsidwa sura (yotiloleza kumenyana ndi osakhulupirira Allah amene akutiputa)? Koma ikavumbulutsidwa Sura yokhazikika (lamulo lake), ndipo mkati mwake ndi kutchulidwa nkhani zankhondo, uwaona amene ali ndi matenda m’mitima mwawo akukuyang’ana m’mayang’anidwe a yemwe akukomoka ndi imfa, (chifukwa cha kulida lamulo lomenyana ndi osakhulupirira), basi kuonongeka ndi kwawo |