Quran with Chichewa translation - Surah Al-Ma’idah ayat 33 - المَائدة - Page - Juz 6
﴿إِنَّمَا جَزَٰٓؤُاْ ٱلَّذِينَ يُحَارِبُونَ ٱللَّهَ وَرَسُولَهُۥ وَيَسۡعَوۡنَ فِي ٱلۡأَرۡضِ فَسَادًا أَن يُقَتَّلُوٓاْ أَوۡ يُصَلَّبُوٓاْ أَوۡ تُقَطَّعَ أَيۡدِيهِمۡ وَأَرۡجُلُهُم مِّنۡ خِلَٰفٍ أَوۡ يُنفَوۡاْ مِنَ ٱلۡأَرۡضِۚ ذَٰلِكَ لَهُمۡ خِزۡيٞ فِي ٱلدُّنۡيَاۖ وَلَهُمۡ فِي ٱلۡأٓخِرَةِ عَذَابٌ عَظِيمٌ ﴾
[المَائدة: 33]
﴿إنما جزاء الذين يحاربون الله ورسوله ويسعون في الأرض فسادا أن يقتلوا﴾ [المَائدة: 33]
Khaled Ibrahim Betala “Ndithu mphoto ya amene akulimbana ndi Allah ndi Mtumiki Wake (pochita zomwe waletsa) ndi kudzetsa chionongeko pa dziko, aphedwe kapena apachikidwe pa mtanda, kapena adulidwe manja awo ndi miyendo yawo mosemphanitsa (dzanja lakumanja ndi phazi lakumanzere, ndipo dzanja lakumanzere ndi phazi lakumanja); kapena apirikitsidwe mdzikomo. Uku ndikuyaluka kwawo pa dziko lapansi. Ndipo iwo pa tsiku lachimaliziro adzalandira chilango chachikulu |