Quran with Chichewa translation - Surah Al-Ma’idah ayat 44 - المَائدة - Page - Juz 6
﴿إِنَّآ أَنزَلۡنَا ٱلتَّوۡرَىٰةَ فِيهَا هُدٗى وَنُورٞۚ يَحۡكُمُ بِهَا ٱلنَّبِيُّونَ ٱلَّذِينَ أَسۡلَمُواْ لِلَّذِينَ هَادُواْ وَٱلرَّبَّٰنِيُّونَ وَٱلۡأَحۡبَارُ بِمَا ٱسۡتُحۡفِظُواْ مِن كِتَٰبِ ٱللَّهِ وَكَانُواْ عَلَيۡهِ شُهَدَآءَۚ فَلَا تَخۡشَوُاْ ٱلنَّاسَ وَٱخۡشَوۡنِ وَلَا تَشۡتَرُواْ بِـَٔايَٰتِي ثَمَنٗا قَلِيلٗاۚ وَمَن لَّمۡ يَحۡكُم بِمَآ أَنزَلَ ٱللَّهُ فَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡكَٰفِرُونَ ﴾
[المَائدة: 44]
﴿إنا أنـزلنا التوراة فيها هدى ونور يحكم بها النبيون الذين أسلموا للذين﴾ [المَائدة: 44]
Khaled Ibrahim Betala “Ndithudi, tidaivumbulutsa Taurat yokhala ndi chiongoko ndi kuunika; aneneri (a Allah) omwe adagonjera (Allah), adali kulamulira nayo Ayuda, ndiponso Arabbaniyyuna (aphunzitsi a malamulo) ndi Ahabaru (Ansembe) omwe adapemphedwa kusunga buku la Allah ndipo iwo adali mboni pa ilo, choncho (inu Asilamu) musaope anthu, koma opani Ine. Ndipo musasinthanitse Ayah (ndime) zanga ndi (zinthu za) mtengo wochepa. Ndipo amene sakuweruza ndi chimene Allah wavumbulutsa, iwowo ndiwo osakhulupirira (okana Allah) |