Quran with Chichewa translation - Surah Al-hashr ayat 7 - الحَشر - Page - Juz 28
﴿مَّآ أَفَآءَ ٱللَّهُ عَلَىٰ رَسُولِهِۦ مِنۡ أَهۡلِ ٱلۡقُرَىٰ فَلِلَّهِ وَلِلرَّسُولِ وَلِذِي ٱلۡقُرۡبَىٰ وَٱلۡيَتَٰمَىٰ وَٱلۡمَسَٰكِينِ وَٱبۡنِ ٱلسَّبِيلِ كَيۡ لَا يَكُونَ دُولَةَۢ بَيۡنَ ٱلۡأَغۡنِيَآءِ مِنكُمۡۚ وَمَآ ءَاتَىٰكُمُ ٱلرَّسُولُ فَخُذُوهُ وَمَا نَهَىٰكُمۡ عَنۡهُ فَٱنتَهُواْۚ وَٱتَّقُواْ ٱللَّهَۖ إِنَّ ٱللَّهَ شَدِيدُ ٱلۡعِقَابِ ﴾
[الحَشر: 7]
﴿ما أفاء الله على رسوله من أهل القرى فلله وللرسول ولذي القربى﴾ [الحَشر: 7]
Khaled Ibrahim Betala “Chuma chimene Allah wachipereka kwa mtumiki Wake kuchokera kwa anthu am’midzi (yapafupi ndi mzinda wa Madina) chimenecho ncha Allah, ndi Mtumiki, ndi abale a mtumiki ndi amasiye, ndi masikini, ndiponso apaulendo; kuti chisakhale chongozungulira pakati pa olemera okha mwa inu. Ndipo chimene wakupatsani Mtumiki, chilandireni; ndipo chimene Wakuletsani chisiyeni. Muopeni Allah (potsatira malamulo Ake). Ndithu Allah Ngwaukali polanga |