×

سورة الحشر باللغة نيانجا

ترجمات القرآنباللغة نيانجا ⬅ سورة الحشر

ترجمة معاني سورة الحشر باللغة نيانجا - Chichewa

القرآن باللغة نيانجا - سورة الحشر مترجمة إلى اللغة نيانجا، Surah Al Hashr in Chichewa. نوفر ترجمة دقيقة سورة الحشر باللغة نيانجا - Chichewa, الآيات 24 - رقم السورة 59 - الصفحة 545.

بسم الله الرحمن الرحيم

سَبَّحَ لِلَّهِ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَمَا فِي الْأَرْضِ ۖ وَهُوَ الْعَزِيزُ الْحَكِيمُ (1)
Chilichonse chimene chili kumwamba ndi padziko lapansi chimalemekeza Mulungu. Ndipo Iye ndiye Mwini mphamvu zonse ndi wanzeru
هُوَ الَّذِي أَخْرَجَ الَّذِينَ كَفَرُوا مِنْ أَهْلِ الْكِتَابِ مِن دِيَارِهِمْ لِأَوَّلِ الْحَشْرِ ۚ مَا ظَنَنتُمْ أَن يَخْرُجُوا ۖ وَظَنُّوا أَنَّهُم مَّانِعَتُهُمْ حُصُونُهُم مِّنَ اللَّهِ فَأَتَاهُمُ اللَّهُ مِنْ حَيْثُ لَمْ يَحْتَسِبُوا ۖ وَقَذَفَ فِي قُلُوبِهِمُ الرُّعْبَ ۚ يُخْرِبُونَ بُيُوتَهُم بِأَيْدِيهِمْ وَأَيْدِي الْمُؤْمِنِينَ فَاعْتَبِرُوا يَا أُولِي الْأَبْصَارِ (2)
Ndiye amene adachotsa anthu osakhulupirira amene adali pakati pa anthu a m’Buku kuchokera ku nyumba zawo pamene adakumana poyamba. Iwe sumaganiza ndi pang’ono pomwe kuti angachoke. Ndipo iwo anali kuganiza kuti Malinga awo adzawateteza kwa Mulungu! Koma chilango cha Mulungu chidadza pa iwo kuchokera kumbali imene iwo sanali kuyembekezera. Ndipo Iye adaika mantha m’mitima mwawo kotero iwo adagwetsa nyumba ndi manja awo ndiponso manja a anthu okhulupirira. Motero chenjerani tsopano inu amene muli ndi maso
وَلَوْلَا أَن كَتَبَ اللَّهُ عَلَيْهِمُ الْجَلَاءَ لَعَذَّبَهُمْ فِي الدُّنْيَا ۖ وَلَهُمْ فِي الْآخِرَةِ عَذَابُ النَّارِ (3)
Ngati Mulungu akadapanda kuwalamulira kuti achotsedwe, ndithudi, Iye akanawalanga m’dziko lomwe lino ndipo m’moyo umene uli nkudza, ndithudi, iwo adzalandira chilango cha ku Gahena
ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمْ شَاقُّوا اللَّهَ وَرَسُولَهُ ۖ وَمَن يُشَاقِّ اللَّهَ فَإِنَّ اللَّهَ شَدِيدُ الْعِقَابِ (4)
Chifukwa iwo adatsutsa Mulungu ndi Mtumwi mwake. Ndipo ngati wina atsutsa Mulungu ndi Mtumwi wake, ndithudi, Mulungu ali ndi chilango choopsa
مَا قَطَعْتُم مِّن لِّينَةٍ أَوْ تَرَكْتُمُوهَا قَائِمَةً عَلَىٰ أُصُولِهَا فَبِإِذْنِ اللَّهِ وَلِيُخْزِيَ الْفَاسِقِينَ (5)
Chilichonse chimene mudula cha mitengo ing’ono ing’ono ya tende kapena muisiya kuti ikhale njo pa mizu yake, mumachita ndi chilolezo cha Mulungu, ndi cholinga choti achititse manyazi anthu ochita zoipa
وَمَا أَفَاءَ اللَّهُ عَلَىٰ رَسُولِهِ مِنْهُمْ فَمَا أَوْجَفْتُمْ عَلَيْهِ مِنْ خَيْلٍ وَلَا رِكَابٍ وَلَٰكِنَّ اللَّهَ يُسَلِّطُ رُسُلَهُ عَلَىٰ مَن يَشَاءُ ۚ وَاللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ قَدِيرٌ (6)
Chimene Mulungu wapereka kwa Mtumwi wake ndipo walanda kuchokera kwa iwo, si ndinu amene mudapereka akabvalo kapena ngamira kwa iwo. Koma Mulungu ndiye amene amapereka mphamvu kwa Mtumwi wake kupambana aliyense amene iye wafuna ndipo Mulungu ali ndi mphamvu pa chilichonse
مَّا أَفَاءَ اللَّهُ عَلَىٰ رَسُولِهِ مِنْ أَهْلِ الْقُرَىٰ فَلِلَّهِ وَلِلرَّسُولِ وَلِذِي الْقُرْبَىٰ وَالْيَتَامَىٰ وَالْمَسَاكِينِ وَابْنِ السَّبِيلِ كَيْ لَا يَكُونَ دُولَةً بَيْنَ الْأَغْنِيَاءِ مِنكُمْ ۚ وَمَا آتَاكُمُ الرَّسُولُ فَخُذُوهُ وَمَا نَهَاكُمْ عَنْهُ فَانتَهُوا ۚ وَاتَّقُوا اللَّهَ ۖ إِنَّ اللَّهَ شَدِيدُ الْعِقَابِ (7)
Chilichonse chimene Mulungu wapereka ngati chuma chopeza pa nkhondo kwa Mtumwi wake, kuchokera kwa anthu a m’mizinda, mwini wakendi Mulungu, Mtumwiwakendiabalendiamasiye, ndi anthu osauka, ndi a paulendo ndi cholinga choti asakhale katundu wa anthu olemera amene ali pakati panu. Kotero landirani zimene Mtumwi akupatsani ndipo mulewe chimene akuletsani. Ndipo opani Mulungu. Ndithudi Mulungu amalanga molapitsa
لِلْفُقَرَاءِ الْمُهَاجِرِينَ الَّذِينَ أُخْرِجُوا مِن دِيَارِهِمْ وَأَمْوَالِهِمْ يَبْتَغُونَ فَضْلًا مِّنَ اللَّهِ وَرِضْوَانًا وَيَنصُرُونَ اللَّهَ وَرَسُولَهُ ۚ أُولَٰئِكَ هُمُ الصَّادِقُونَ (8)
Ndi wa amphawi amene adabwera ndi Mtumwi amene adapilikitsidwa m’nyumba zawo ndi katundu wawo pofunafuna chisomo chochokera kwa Mulungu ndi chisangalalo chake. Ndipo amatsatira Mulungu ndi Mtumwi wake. Amenewa, ndithudi, ndiwo olungama
وَالَّذِينَ تَبَوَّءُوا الدَّارَ وَالْإِيمَانَ مِن قَبْلِهِمْ يُحِبُّونَ مَنْ هَاجَرَ إِلَيْهِمْ وَلَا يَجِدُونَ فِي صُدُورِهِمْ حَاجَةً مِّمَّا أُوتُوا وَيُؤْثِرُونَ عَلَىٰ أَنفُسِهِمْ وَلَوْ كَانَ بِهِمْ خَصَاصَةٌ ۚ وَمَن يُوقَ شُحَّ نَفْسِهِ فَأُولَٰئِكَ هُمُ الْمُفْلِحُونَ (9)
Ndipo iwo ndi amene, awa asadadze, adali ndi nyumba zawo ndipo adalowa Chisilamu, ndipo adaonetsa chikondi kwa iwo amene amadza kwa iwo, ndipo samachita kaduka ndi katundu amene aperekedwa kwa iwo koma amalolera kuti iwo akhale otsiliza polandira ngakhale kuti nawonso amazifuna. Ndipo aliyense amene amadziteteza ku zilakolako zake, ndithudi, iye adzakhala opambana
وَالَّذِينَ جَاءُوا مِن بَعْدِهِمْ يَقُولُونَ رَبَّنَا اغْفِرْ لَنَا وَلِإِخْوَانِنَا الَّذِينَ سَبَقُونَا بِالْإِيمَانِ وَلَا تَجْعَلْ فِي قُلُوبِنَا غِلًّا لِّلَّذِينَ آمَنُوا رَبَّنَا إِنَّكَ رَءُوفٌ رَّحِيمٌ (10)
Ndipo iwo amene adadza pambuyo pawo adati: “Ambuye wathu, tikhululukireni ife pamodzi ndi abale athu amene adalowa Chisilamu poyambirira, ndipo musasiye m’mitima mwathu kaduka wowachitira iwo amene adakhulupirira kale. Ambuye wathu! Ndithudi inu ndinu okoma mtima, Mwini chifundo.”
۞ أَلَمْ تَرَ إِلَى الَّذِينَ نَافَقُوا يَقُولُونَ لِإِخْوَانِهِمُ الَّذِينَ كَفَرُوا مِنْ أَهْلِ الْكِتَابِ لَئِنْ أُخْرِجْتُمْ لَنَخْرُجَنَّ مَعَكُمْ وَلَا نُطِيعُ فِيكُمْ أَحَدًا أَبَدًا وَإِن قُوتِلْتُمْ لَنَنصُرَنَّكُمْ وَاللَّهُ يَشْهَدُ إِنَّهُمْ لَكَاذِبُونَ (11)
Kodi iwe sudawaone anthu a chinyengo ali kunena kwa abale awo osakhulupirira amene ali pakati pa anthu a m’Buku? (Ponena kuti): “Ngati iwo akupirikitsani inu, nafenso tidzapita nanu, ndipo sitidzamvera wina aliyense wodana ndi inu. Ngati inu muputidwa, ndithudi, ife tidzakuthandizani.” Koma Mulungu achitira umboni kuti, ndithudi, iwo ndi abodza
لَئِنْ أُخْرِجُوا لَا يَخْرُجُونَ مَعَهُمْ وَلَئِن قُوتِلُوا لَا يَنصُرُونَهُمْ وَلَئِن نَّصَرُوهُمْ لَيُوَلُّنَّ الْأَدْبَارَ ثُمَّ لَا يُنصَرُونَ (12)
Ndithudi ngati iwo apirikitsidwa, iwo sadzapita nawo ayi ndipo ngati inu muputidwa iwo sadzakuthandizani konsekonse. Ndipo ngati iwo atathandiza, iwo adzangobwerera m’mbuyo motero iwo sadzapambana ai
لَأَنتُمْ أَشَدُّ رَهْبَةً فِي صُدُورِهِم مِّنَ اللَّهِ ۚ ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمْ قَوْمٌ لَّا يَفْقَهُونَ (13)
Ndithudi inu mumayambitsa mantha m’mitima mwawo kuposa Mulungu. Ichi ndi chifukwa chakuti iwo ndi anthu osazindikira
لَا يُقَاتِلُونَكُمْ جَمِيعًا إِلَّا فِي قُرًى مُّحَصَّنَةٍ أَوْ مِن وَرَاءِ جُدُرٍ ۚ بَأْسُهُم بَيْنَهُمْ شَدِيدٌ ۚ تَحْسَبُهُمْ جَمِيعًا وَقُلُوبُهُمْ شَتَّىٰ ۚ ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمْ قَوْمٌ لَّا يَعْقِلُونَ (14)
Iwo sadzamenyana nawe ngati gulu limodzi ayi koma mozemba pogwiritsa ntchito Malinga ya m’mizinda kapena pobisala kuzipupa. Mtima womenya nkhondo ulipo pakati pawo moti iwe ukhoza kuganiza kuti ndi ogwirizana. Koma mitima yawo ndi yogawikana chifukwa iwo ndi anthu osadziwa chilichonse
كَمَثَلِ الَّذِينَ مِن قَبْلِهِمْ قَرِيبًا ۖ ذَاقُوا وَبَالَ أَمْرِهِمْ وَلَهُمْ عَذَابٌ أَلِيمٌ (15)
Iwo ali ngati amene adadza pambuyo pawo amene adalandira dipo loipa chifukwa cha ntchito zawo ndipo iwo adzalandira chilango chowawa kwambiri
كَمَثَلِ الشَّيْطَانِ إِذْ قَالَ لِلْإِنسَانِ اكْفُرْ فَلَمَّا كَفَرَ قَالَ إِنِّي بَرِيءٌ مِّنكَ إِنِّي أَخَافُ اللَّهَ رَبَّ الْعَالَمِينَ (16)
Monga Satana pamene amamuuza munthu kuti: “Usakhulupirire mwa Mulungu.” Ndipo pamene munthu sakhulupirira mwa Mulungu, Satana amati: “Ndathana nawe tsopano chifukwa ine ndimaopa Mulungu, Ambuye wazolengedwa zonse.”
فَكَانَ عَاقِبَتَهُمَا أَنَّهُمَا فِي النَّارِ خَالِدَيْنِ فِيهَا ۚ وَذَٰلِكَ جَزَاءُ الظَّالِمِينَ (17)
Motero mapeto awo ndi akuti onsewa adzapsa ku moto kumene adzakhalako mpaka kalekale. Limenelo ndilo dipo la anthu ochita zoipa
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا اتَّقُوا اللَّهَ وَلْتَنظُرْ نَفْسٌ مَّا قَدَّمَتْ لِغَدٍ ۖ وَاتَّقُوا اللَّهَ ۚ إِنَّ اللَّهَ خَبِيرٌ بِمَا تَعْمَلُونَ (18)
oh inu anthu okhulupirira! opani Mulungu. Ndipo kwaniritsani udindo wanu kwa Iye. Ndipo ulekeni mzimu uliwonse uganize zimene udzalandire mawa ndipo opani Mulungu. Ndithudi Mulungu amadziwa chilichonse chimene mumachita
وَلَا تَكُونُوا كَالَّذِينَ نَسُوا اللَّهَ فَأَنسَاهُمْ أَنفُسَهُمْ ۚ أُولَٰئِكَ هُمُ الْفَاسِقُونَ (19)
Ndipo inu musakhale ngati iwo amene adaiwala Mulungu ndipo Iye adawachititsa kuti adziiwale eni ake. Amenewa ndiwo amene amaphwanya malamulo mopitiriza
لَا يَسْتَوِي أَصْحَابُ النَّارِ وَأَصْحَابُ الْجَنَّةِ ۚ أَصْحَابُ الْجَنَّةِ هُمُ الْفَائِزُونَ (20)
Anthu a ku Gahena siofanana ndi anthu a ku Paradiso. Ndi anthu a ku Paradiso amene adzakhala opambana
لَوْ أَنزَلْنَا هَٰذَا الْقُرْآنَ عَلَىٰ جَبَلٍ لَّرَأَيْتَهُ خَاشِعًا مُّتَصَدِّعًا مِّنْ خَشْيَةِ اللَّهِ ۚ وَتِلْكَ الْأَمْثَالُ نَضْرِبُهَا لِلنَّاسِ لَعَلَّهُمْ يَتَفَكَّرُونَ (21)
Ife tikadatumiza Buku la Korani ili pa phiri, ndithudi; iwe ukadaona ilo lili kudzichepetsa ndi kung’ambika chifukwa cha mantha ndi Mulungu. Zimenezi ndi zitsanzo zimene timaulula kwa anthu kuti atha kuganiza
هُوَ اللَّهُ الَّذِي لَا إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ ۖ عَالِمُ الْغَيْبِ وَالشَّهَادَةِ ۖ هُوَ الرَّحْمَٰنُ الرَّحِيمُ (22)
Iye ndiye Mulungu ndipo kupatula Iye kulibe Mulungu wina amene amadziwa zinthu zonse zachinsinsi ndi zolankhula mokweza. Iye ndi Wachifundo, Mwini chisoni chosatha
هُوَ اللَّهُ الَّذِي لَا إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ الْمَلِكُ الْقُدُّوسُ السَّلَامُ الْمُؤْمِنُ الْمُهَيْمِنُ الْعَزِيزُ الْجَبَّارُ الْمُتَكَبِّرُ ۚ سُبْحَانَ اللَّهِ عَمَّا يُشْرِكُونَ (23)
Iye ndiye Mulungu ndipo kupatula Iye kulibe Mulungu wina. Iye ndi Mwini Ufumu, Woyera, Maziko a mtendere, Mtetezi ndi Mwini ukulu. Ulemerero ukhale kwa Mulungu kuposa zimene amamusinjirira
هُوَ اللَّهُ الْخَالِقُ الْبَارِئُ الْمُصَوِّرُ ۖ لَهُ الْأَسْمَاءُ الْحُسْنَىٰ ۚ يُسَبِّحُ لَهُ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۖ وَهُوَ الْعَزِيزُ الْحَكِيمُ (24)
Iye ndi Mulungu, Namalenga, Chiyambi ndi Mkonzi. Ake ndi mayina abwino okhaokha. Chilichonse chimene chili kumwamba ndi padziko lapansi chimamulemekeza ndi kumuyamika ndipo Iye ndi Wolemekezeka, Wamphamvu ndi Wanzeru
❮ السورة السابقة السورة التـالية ❯

قراءة المزيد من سور القرآن الكريم :

1- الفاتحة2- البقرة3- آل عمران
4- النساء5- المائدة6- الأنعام
7- الأعراف8- الأنفال9- التوبة
10- يونس11- هود12- يوسف
13- الرعد14- إبراهيم15- الحجر
16- النحل17- الإسراء18- الكهف
19- مريم20- طه21- الأنبياء
22- الحج23- المؤمنون24- النور
25- الفرقان26- الشعراء27- النمل
28- القصص29- العنكبوت30- الروم
31- لقمان32- السجدة33- الأحزاب
34- سبأ35- فاطر36- يس
37- الصافات38- ص39- الزمر
40- غافر41- فصلت42- الشورى
43- الزخرف44- الدخان45- الجاثية
46- الأحقاف47- محمد48- الفتح
49- الحجرات50- ق51- الذاريات
52- الطور53- النجم54- القمر
55- الرحمن56- الواقعة57- الحديد
58- المجادلة59- الحشر60- الممتحنة
61- الصف62- الجمعة63- المنافقون
64- التغابن65- الطلاق66- التحريم
67- الملك68- القلم69- الحاقة
70- المعارج71- نوح72- الجن
73- المزمل74- المدثر75- القيامة
76- الإنسان77- المرسلات78- النبأ
79- النازعات80- عبس81- التكوير
82- الإنفطار83- المطففين84- الانشقاق
85- البروج86- الطارق87- الأعلى
88- الغاشية89- الفجر90- البلد
91- الشمس92- الليل93- الضحى
94- الشرح95- التين96- العلق
97- القدر98- البينة99- الزلزلة
100- العاديات101- القارعة102- التكاثر
103- العصر104- الهمزة105- الفيل
106- قريش107- الماعون108- الكوثر
109- الكافرون110- النصر111- المسد
112- الإخلاص113- الفلق114- الناس