Quran with Chichewa translation - Surah Al-An‘am ayat 165 - الأنعَام - Page - Juz 8
﴿وَهُوَ ٱلَّذِي جَعَلَكُمۡ خَلَٰٓئِفَ ٱلۡأَرۡضِ وَرَفَعَ بَعۡضَكُمۡ فَوۡقَ بَعۡضٖ دَرَجَٰتٖ لِّيَبۡلُوَكُمۡ فِي مَآ ءَاتَىٰكُمۡۗ إِنَّ رَبَّكَ سَرِيعُ ٱلۡعِقَابِ وَإِنَّهُۥ لَغَفُورٞ رَّحِيمُۢ ﴾
[الأنعَام: 165]
﴿وهو الذي جعلكم خلائف الأرض ورفع بعضكم فوق بعض درجات ليبلوكم في﴾ [الأنعَام: 165]
Khaled Ibrahim Betala “Ndipo Iye ndi Yemwe wakuchitani kukhala am’lowam’malo pa dziko (kulowa m’malo mwa anzanu omwe adaonongeka). Ndipo wawatukula pa ulemelero (ndi pa chuma) ena a inu pamwamba pa ena kuti akuyeseni pa zomwe wakupatsani. (Amene apatsidwa chuma ndi ulemelero athandize amene sadapatsidwe. Ndipo amene sadapatsidwe apirire asalande chinthu chamwini). Ndithudi, Mbuye wako Ngwachangu pokhaulitsa. Ndiponso Iye Ngokhululuka kwabasi Ngwachisoni chosatha |