Quran with Chichewa translation - Surah As-saff ayat 14 - الصَّف - Page - Juz 28
﴿يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ كُونُوٓاْ أَنصَارَ ٱللَّهِ كَمَا قَالَ عِيسَى ٱبۡنُ مَرۡيَمَ لِلۡحَوَارِيِّـۧنَ مَنۡ أَنصَارِيٓ إِلَى ٱللَّهِۖ قَالَ ٱلۡحَوَارِيُّونَ نَحۡنُ أَنصَارُ ٱللَّهِۖ فَـَٔامَنَت طَّآئِفَةٞ مِّنۢ بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ وَكَفَرَت طَّآئِفَةٞۖ فَأَيَّدۡنَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ عَلَىٰ عَدُوِّهِمۡ فَأَصۡبَحُواْ ظَٰهِرِينَ ﴾
[الصَّف: 14]
﴿ياأيها الذين آمنوا كونوا أنصار الله كما قال عيسى ابن مريم للحواريين﴾ [الصَّف: 14]
Khaled Ibrahim Betala “E inu amene mwakhulupirira! Khalani othangata (kufalitsa chipembedzo cha) Allah (pamene Mtumiki akukuitanani kuti mumthangate) monga momwe adanenera Isa (Yesu) mwana wa Mariya powauza otsatira ake: “Ndani adzandithangata pa ntchito ya Allah (yofalitsa chipembedzo Chake)? Otsatira ake adanena: “Ife ndife othangata (kufalitsa chipembedzo cha) Allah.” Choncho gulu lina la ana a Israyeli lidakhululupirira, ndipo gulu lina silidakhululupirire, tero tidawapatsa mphamvu amene adakhulupirira pa adani awo, ndipo adali opambana |