سَبَّحَ لِلَّهِ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَمَا فِي الْأَرْضِ ۖ وَهُوَ الْعَزِيزُ الْحَكِيمُ (1) Chilichonse chimene chili mlengalenga ndi padziko lapansi, chimalemekeza Mulungu. Ndipo Iye ndiye Mwini mphamvu zonse ndi Mwini nzeru |
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا لِمَ تَقُولُونَ مَا لَا تَفْعَلُونَ (2) oh inu okhulupirira! Kodi bwanji mumanena zinthu zimene simuchita |
كَبُرَ مَقْتًا عِندَ اللَّهِ أَن تَقُولُوا مَا لَا تَفْعَلُونَ (3) Ndithudi ndi chinthu chonyansa kwambiri pamaso pa Mulungu kuti muzinena chinthu chimene simuchita |
إِنَّ اللَّهَ يُحِبُّ الَّذِينَ يُقَاتِلُونَ فِي سَبِيلِهِ صَفًّا كَأَنَّهُم بُنْيَانٌ مَّرْصُوصٌ (4) Ndithudi Mulungu amakonda iwo amene amamenya nkhondo ndi cholinga chokhazikitsa ulamuliro wake molimba, m’magulu, ngati chipupa cha miyala |
وَإِذْ قَالَ مُوسَىٰ لِقَوْمِهِ يَا قَوْمِ لِمَ تُؤْذُونَنِي وَقَد تَّعْلَمُونَ أَنِّي رَسُولُ اللَّهِ إِلَيْكُمْ ۖ فَلَمَّا زَاغُوا أَزَاغَ اللَّهُ قُلُوبَهُمْ ۚ وَاللَّهُ لَا يَهْدِي الْقَوْمَ الْفَاسِقِينَ (5) Ndi pamene Mose adanena ndi anthu ake: “oh inu anthu anga! Kodi bwanji mukundikwiyitsa pamene muli kudziwa kuti ine ndine Mtumwi wa Mulungu kwa inuyo?” Ndipo pamene iwo adalakwa, Mulungu adalola kuti mitima yawo ilakwe. Ndipo Mulungu satsogolera anthu ophwanya malamulo |
وَإِذْ قَالَ عِيسَى ابْنُ مَرْيَمَ يَا بَنِي إِسْرَائِيلَ إِنِّي رَسُولُ اللَّهِ إِلَيْكُم مُّصَدِّقًا لِّمَا بَيْنَ يَدَيَّ مِنَ التَّوْرَاةِ وَمُبَشِّرًا بِرَسُولٍ يَأْتِي مِن بَعْدِي اسْمُهُ أَحْمَدُ ۖ فَلَمَّا جَاءَهُم بِالْبَيِّنَاتِ قَالُوا هَٰذَا سِحْرٌ مُّبِينٌ (6) Ndi pamene Yesu, mwana wa mwamuna wa Maria, adati: “oh inu ana a Israyeli! Ine ndine Mtumwi wa Mulungu amene ndatumidwa kwa inu, kutsimikizira za Buku la Chipangano chakale limene lidadza ine ndisanadze, ndi kuulula nkhani yabwino ya Mtumwi Ahmad amene adzabwera ine nditachoka.” Koma pamene iye adadza kwa iwo ndi zizindikiro zooneka, iwo adati: “Awa ndiwo matsenga enieni.” |
وَمَنْ أَظْلَمُ مِمَّنِ افْتَرَىٰ عَلَى اللَّهِ الْكَذِبَ وَهُوَ يُدْعَىٰ إِلَى الْإِسْلَامِ ۚ وَاللَّهُ لَا يَهْدِي الْقَوْمَ الظَّالِمِينَ (7) Kodi amalakwa kwambiri ndani kuposa As-Saff 597 iye amene amapeka bodza lokhudza Mulungu ngakhale pamene ali kuitanidwa kuti alowe Chisilamu? Ndipo Mulungu satsogolera iwo amene amachita zoipa |
يُرِيدُونَ لِيُطْفِئُوا نُورَ اللَّهِ بِأَفْوَاهِهِمْ وَاللَّهُ مُتِمُّ نُورِهِ وَلَوْ كَرِهَ الْكَافِرُونَ (8) Cholinga chawo ndikufuna kuzimitsa nyali ya Mulungu ndi milomo yawo. Koma Mulungu adzateteza nyali yake ngakhale kuti anthu osakhulupirira sakondwera nazo |
هُوَ الَّذِي أَرْسَلَ رَسُولَهُ بِالْهُدَىٰ وَدِينِ الْحَقِّ لِيُظْهِرَهُ عَلَى الدِّينِ كُلِّهِ وَلَوْ كَرِهَ الْمُشْرِكُونَ (9) Ndiye amene watumiza Mtumwi wake ndi ulangizi ndiponso chipembedzo choonadi kuti chikhale chapamwamba pa zipembedzo zina zonse ngakhale kuti anthu osakhulupirira sakondwera nazo |
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا هَلْ أَدُلُّكُمْ عَلَىٰ تِجَارَةٍ تُنجِيكُم مِّنْ عَذَابٍ أَلِيمٍ (10) Oh inu anthu okhulupirira! Kodi ndikulangizeni malonda apafupi amene angakuomboleni ku chilango choopsa |
تُؤْمِنُونَ بِاللَّهِ وَرَسُولِهِ وَتُجَاهِدُونَ فِي سَبِيلِ اللَّهِ بِأَمْوَالِكُمْ وَأَنفُسِكُمْ ۚ ذَٰلِكُمْ خَيْرٌ لَّكُمْ إِن كُنتُمْ تَعْلَمُونَ (11) Kuti mukhulupirire mwa Mulungu ndi mwa Mtumwi wake, kuti mudzipereke kwathunthu mu njira ya Mulungu pogwiritsa ntchito chuma chanu ndi inu eni ake. Chimenechi ndicho chinthu chabwino kwa inu ngati inu mukadadziwa |
يَغْفِرْ لَكُمْ ذُنُوبَكُمْ وَيُدْخِلْكُمْ جَنَّاتٍ تَجْرِي مِن تَحْتِهَا الْأَنْهَارُ وَمَسَاكِنَ طَيِّبَةً فِي جَنَّاتِ عَدْنٍ ۚ ذَٰلِكَ الْفَوْزُ الْعَظِيمُ (12) Iyeadzakukhululukiraniinumachimoanu ndi kukulandirani m’minda imene pansi pake pamayenda mitsinje, ndipo adzakulowetsani m’nyumba zokongola ndi zaulemu za m’Paradiso. Kumeneko, ndithudi, ndiko kupambana kwenikweni |
وَأُخْرَىٰ تُحِبُّونَهَا ۖ نَصْرٌ مِّنَ اللَّهِ وَفَتْحٌ قَرِيبٌ ۗ وَبَشِّرِ الْمُؤْمِنِينَ (13) Ndipo Iye adzakupatsani madalitso ena amene mumakonda. Chithandizo chochokera kwa Mulungu ndi kupambana mwamsanga. Kotero auze nkhani yabwino anthu okhulupirira |
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا كُونُوا أَنصَارَ اللَّهِ كَمَا قَالَ عِيسَى ابْنُ مَرْيَمَ لِلْحَوَارِيِّينَ مَنْ أَنصَارِي إِلَى اللَّهِ ۖ قَالَ الْحَوَارِيُّونَ نَحْنُ أَنصَارُ اللَّهِ ۖ فَآمَنَت طَّائِفَةٌ مِّن بَنِي إِسْرَائِيلَ وَكَفَرَت طَّائِفَةٌ ۖ فَأَيَّدْنَا الَّذِينَ آمَنُوا عَلَىٰ عَدُوِّهِمْ فَأَصْبَحُوا ظَاهِرِينَ (14) oh inu okhulupirira! Khalani otumikira Mulungu monga momwe ananenera Yesu, mwana wa mwamuna wa Maria, kwa ophunzira ake: “Kodi ndani andithandiza ine potumikira Mulungu?” Iwo adayankha: “Ife ndife othandiza Mulungu.” Kotero ena mwa ana a Israyeli adakhulupirira pamene ena sadakhulupirire. Motero Ife tidawapatsa mphamvu iwo amene adakhulupirira zopambana adani awo ndipo iwo adapambanadi |