Quran with Chichewa translation - Surah Al-A‘raf ayat 187 - الأعرَاف - Page - Juz 9
﴿يَسۡـَٔلُونَكَ عَنِ ٱلسَّاعَةِ أَيَّانَ مُرۡسَىٰهَاۖ قُلۡ إِنَّمَا عِلۡمُهَا عِندَ رَبِّيۖ لَا يُجَلِّيهَا لِوَقۡتِهَآ إِلَّا هُوَۚ ثَقُلَتۡ فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ لَا تَأۡتِيكُمۡ إِلَّا بَغۡتَةٗۗ يَسۡـَٔلُونَكَ كَأَنَّكَ حَفِيٌّ عَنۡهَاۖ قُلۡ إِنَّمَا عِلۡمُهَا عِندَ ٱللَّهِ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَ ٱلنَّاسِ لَا يَعۡلَمُونَ ﴾
[الأعرَاف: 187]
﴿يسألونك عن الساعة أيان مرساها قل إنما علمها عند ربي لا يجليها﴾ [الأعرَاف: 187]
Khaled Ibrahim Betala “Akukufunsa za nthawi (ya Qiyâma) kuti idzakhalako liti? Nena: “Kudziwika kwa nthawi yake kuli kwa Mbuye wanga. palibe amene angaionetse poyera nthawi yake koma Iye. Nkovuta kwambiri kumwamba ndi pansi (kuizindikira nthawi yake). Siidzakudzerani koma mwadzidzidzi.” Akukufunsa ngati kuti iwe ukudziwa bwino za nthawiyo. Nena: “Kudziwika kwa nthawi yake kuli kwa Allah. Koma anthu ambiri sadziwa.” |