Quran with Chichewa translation - Surah At-Taubah ayat 37 - التوبَة - Page - Juz 10
﴿إِنَّمَا ٱلنَّسِيٓءُ زِيَادَةٞ فِي ٱلۡكُفۡرِۖ يُضَلُّ بِهِ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ يُحِلُّونَهُۥ عَامٗا وَيُحَرِّمُونَهُۥ عَامٗا لِّيُوَاطِـُٔواْ عِدَّةَ مَا حَرَّمَ ٱللَّهُ فَيُحِلُّواْ مَا حَرَّمَ ٱللَّهُۚ زُيِّنَ لَهُمۡ سُوٓءُ أَعۡمَٰلِهِمۡۗ وَٱللَّهُ لَا يَهۡدِي ٱلۡقَوۡمَ ٱلۡكَٰفِرِينَ ﴾
[التوبَة: 37]
﴿إنما النسيء زيادة في الكفر يضل به الذين كفروا يحلونه عاما ويحرمونه﴾ [التوبَة: 37]
Khaled Ibrahim Betala “Ndithu kutalikitsa ndi kuchedwetsa (mwezi wopatulika kuti usafike mwamsanga), kumaonjezera kusakhulupirira (mwa Allah), zoterozo akusokerezedwa nazo amene sadakhulupirire. Chaka china amauyesa wosapatulika pomwe chaka china amauyesa wopatulika ndi cholinga chokwaniritsa chiwerengero cholingana ndi miyezi yomwe Allah adaipatula kukhala yopatulika. Choncho, chimene Allah adaletsa, amachiyesa chololedwa. Zakometsedwa kwa iwo zochita zawo zoipa. Ndipo Allah sawatsogolera anthu osakhulupirira |