Quran with Chichewa translation - Surah At-Taubah ayat 69 - التوبَة - Page - Juz 10
﴿كَٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِكُمۡ كَانُوٓاْ أَشَدَّ مِنكُمۡ قُوَّةٗ وَأَكۡثَرَ أَمۡوَٰلٗا وَأَوۡلَٰدٗا فَٱسۡتَمۡتَعُواْ بِخَلَٰقِهِمۡ فَٱسۡتَمۡتَعۡتُم بِخَلَٰقِكُمۡ كَمَا ٱسۡتَمۡتَعَ ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِكُم بِخَلَٰقِهِمۡ وَخُضۡتُمۡ كَٱلَّذِي خَاضُوٓاْۚ أُوْلَٰٓئِكَ حَبِطَتۡ أَعۡمَٰلُهُمۡ فِي ٱلدُّنۡيَا وَٱلۡأٓخِرَةِۖ وَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡخَٰسِرُونَ ﴾
[التوبَة: 69]
﴿كالذين من قبلكم كانوا أشد منكم قوة وأكثر أموالا وأولادا فاستمتعوا بخلاقهم﴾ [التوبَة: 69]
Khaled Ibrahim Betala “(Inu osakhulupirira) ndinu ofanana ndi amene adalipo patsogolo panu. (Tikuonongani monga tidawaonongera iwo; koma) iwo adali ndi nyonga zambiri kuposa inu; adalinso ndi chuma chambiri ndi ana ambiri kuposa inu. Choncho, adasangalalira gawo lawo, inunso mukusangalalira gawo lanu monga momwe adasangalalira gawo lawo omwe adalipo patsogolo panu, ndipo mwamira m’zoipa monga momwe adamilira iwo. Awo ndi amene zochita zawo zidapita pachabe padziko lapansi ndi pa tsiku lachimaliziro. Awo ndi omwe ali otaika (oluza) |