Quran with Chichewa translation - Surah At-Taubah ayat 74 - التوبَة - Page - Juz 10
﴿يَحۡلِفُونَ بِٱللَّهِ مَا قَالُواْ وَلَقَدۡ قَالُواْ كَلِمَةَ ٱلۡكُفۡرِ وَكَفَرُواْ بَعۡدَ إِسۡلَٰمِهِمۡ وَهَمُّواْ بِمَا لَمۡ يَنَالُواْۚ وَمَا نَقَمُوٓاْ إِلَّآ أَنۡ أَغۡنَىٰهُمُ ٱللَّهُ وَرَسُولُهُۥ مِن فَضۡلِهِۦۚ فَإِن يَتُوبُواْ يَكُ خَيۡرٗا لَّهُمۡۖ وَإِن يَتَوَلَّوۡاْ يُعَذِّبۡهُمُ ٱللَّهُ عَذَابًا أَلِيمٗا فِي ٱلدُّنۡيَا وَٱلۡأٓخِرَةِۚ وَمَا لَهُمۡ فِي ٱلۡأَرۡضِ مِن وَلِيّٖ وَلَا نَصِيرٖ ﴾
[التوبَة: 74]
﴿يحلفون بالله ما قالوا ولقد قالوا كلمة الكفر وكفروا بعد إسلامهم وهموا﴾ [التوبَة: 74]
Khaled Ibrahim Betala “(Achiphamaso pambuyo pomunenera Allah ndi Mtumiki Wake mawu oipa), akulumbira potchula dzina la Allah (kuti) sadanene (zonyoza), pomwe adanenadi mawu aukafiri, ndipo akana chikhulupiliro pambuyo posonyeza Chisilamu chawo (chabodza); ndipo adatsimikiza (kuchita) zomwe sadathe kuzifika. Komatu sadaone choipa (m’kudza kwa Chisilamu), koma kuti Allah ndi Mtumiki Wake adawalemeretsa ndi zabwino zake. Choncho Ngati alapa, zikhala zabwino kwa iwo. Ndipo ngati anyoza, Allah awalanga ndi chilango chowawa pa moyo wa pa dziko lapansi ndi patsiku lachimaliziro. Ndipo sadzakhala ndi mtetezi ngakhale aliyense wowapulumutsa pa dziko |