Quran with Chichewa translation - Surah al-‘Imran ayat 154 - آل عِمران - Page - Juz 4
﴿ثُمَّ أَنزَلَ عَلَيۡكُم مِّنۢ بَعۡدِ ٱلۡغَمِّ أَمَنَةٗ نُّعَاسٗا يَغۡشَىٰ طَآئِفَةٗ مِّنكُمۡۖ وَطَآئِفَةٞ قَدۡ أَهَمَّتۡهُمۡ أَنفُسُهُمۡ يَظُنُّونَ بِٱللَّهِ غَيۡرَ ٱلۡحَقِّ ظَنَّ ٱلۡجَٰهِلِيَّةِۖ يَقُولُونَ هَل لَّنَا مِنَ ٱلۡأَمۡرِ مِن شَيۡءٖۗ قُلۡ إِنَّ ٱلۡأَمۡرَ كُلَّهُۥ لِلَّهِۗ يُخۡفُونَ فِيٓ أَنفُسِهِم مَّا لَا يُبۡدُونَ لَكَۖ يَقُولُونَ لَوۡ كَانَ لَنَا مِنَ ٱلۡأَمۡرِ شَيۡءٞ مَّا قُتِلۡنَا هَٰهُنَاۗ قُل لَّوۡ كُنتُمۡ فِي بُيُوتِكُمۡ لَبَرَزَ ٱلَّذِينَ كُتِبَ عَلَيۡهِمُ ٱلۡقَتۡلُ إِلَىٰ مَضَاجِعِهِمۡۖ وَلِيَبۡتَلِيَ ٱللَّهُ مَا فِي صُدُورِكُمۡ وَلِيُمَحِّصَ مَا فِي قُلُوبِكُمۡۚ وَٱللَّهُ عَلِيمُۢ بِذَاتِ ٱلصُّدُورِ ﴾
[آل عِمران: 154]
﴿ثم أنـزل عليكم من بعد الغم أمنة نعاسا يغشى طائفة منكم وطائفة﴾ [آل عِمران: 154]
Khaled Ibrahim Betala “Kenako pambuyo pa kudandaula, adakutsitsirani mpumulo - tulo tomwe tidaphimba gulu lina mwa inu. Padali gulu lina lomwe maganizo awo adawatangwanitsa namuganizira Allah ndizoganizira zopanda choonadi, zoganizira zaumbuli; ankati: “Ha! Kodi tili ndi chiyani ife pa chinthu ichi?” Nena: “Zinthu zonse nza Allah.” Akubisa m’mitima mwawo zomwe sakuzionetsa kwa iwe. Akunena: “Tidakakhala ndi chilichonse pa chinthu ichi, sitikadaphedwa apa.” Nena: “Ngakhale mukadakhala m’nyumba zanu, ndithudi kwa iwo amene imfa idalembedwa (kuti amwalire) akadapita kumalo omwalilirawo, koma Allah (adachita izi) kuti awonetse poyera zomwe zili m’zifuwa zanu. Ndikuyeretsa zomwe zili m’mitima mwanu. Ndipo Allah Ngodziwa za mzifuwa.” |