Quran with Chichewa translation - Surah Saba’ ayat 19 - سَبإ - Page - Juz 22
﴿فَقَالُواْ رَبَّنَا بَٰعِدۡ بَيۡنَ أَسۡفَارِنَا وَظَلَمُوٓاْ أَنفُسَهُمۡ فَجَعَلۡنَٰهُمۡ أَحَادِيثَ وَمَزَّقۡنَٰهُمۡ كُلَّ مُمَزَّقٍۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٖ لِّكُلِّ صَبَّارٖ شَكُورٖ ﴾
[سَبإ: 19]
﴿فقالوا ربنا باعد بين أسفارنا وظلموا أنفسهم فجعلناهم أحاديث ومزقناهم كل ممزق﴾ [سَبإ: 19]
Khaled Ibrahim Betala “Koma (adauda mtendere umenewu;) adati: “E Mbuye wathu! Talikitsani ntunda pakati pa maulendo athu; (kuyandikirana kwa midzi, sikukutisonyeza kuti tili pa ulendo).” Ndipo adadzichitira okha zoipa. Choncho tidawachita kukhala miyambi (imene anthu a pambuyo ankauzana pakati pawo), ndipo tidawabalalitsa; kubalalikana zedi. (Ena adathawira dziko ili, ena dziko lina). Ndithu m’zimenezo muli malingaliro kwa yense wopirira kwabasi ndi wothokoza kwambiri |