Quran with Chichewa translation - Surah Az-Zumar ayat 21 - الزُّمَر - Page - Juz 23
﴿أَلَمۡ تَرَ أَنَّ ٱللَّهَ أَنزَلَ مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءٗ فَسَلَكَهُۥ يَنَٰبِيعَ فِي ٱلۡأَرۡضِ ثُمَّ يُخۡرِجُ بِهِۦ زَرۡعٗا مُّخۡتَلِفًا أَلۡوَٰنُهُۥ ثُمَّ يَهِيجُ فَتَرَىٰهُ مُصۡفَرّٗا ثُمَّ يَجۡعَلُهُۥ حُطَٰمًاۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَذِكۡرَىٰ لِأُوْلِي ٱلۡأَلۡبَٰبِ ﴾
[الزُّمَر: 21]
﴿ألم تر أن الله أنـزل من السماء ماء فسلكه ينابيع في الأرض﴾ [الزُّمَر: 21]
Khaled Ibrahim Betala “Kodi suona kuti Allah amatsitsa madzi kuchokera kumwamba, ndipo amawalowetsa mu akasupe mkati mwa nthaka, kenako amatulutsa ndi madziwo mbewu zosiyana mitundu: (chimanga, mpunga, tirigu, ndi zina zotere). Ndipo kenako zimauma (pambuyo pokhala zobiriwira); umaziona zili zachikasu. Kenako amazichita kukhala zidutswazidutswa? Ndithu muzimenezo muli chikumbutso kwa eni nzeru (zofufuzira zinthu) |