تَنزِيلُ الْكِتَابِ مِنَ اللَّهِ الْعَزِيزِ الْحَكِيمِ (1) Chivumbulutso cha Buku ili ndi chochokera kwa Mulungu, Mwini mphamvu ndi Mwini nzeru |
إِنَّا أَنزَلْنَا إِلَيْكَ الْكِتَابَ بِالْحَقِّ فَاعْبُدِ اللَّهَ مُخْلِصًا لَّهُ الدِّينَ (2) Ndithudi tavumbulutsa kwa iwe Buku mwachoonadi. Motero pembedza Mulungu yekha ndipo udzipereke kwa Iye kwathunthu |
أَلَا لِلَّهِ الدِّينُ الْخَالِصُ ۚ وَالَّذِينَ اتَّخَذُوا مِن دُونِهِ أَوْلِيَاءَ مَا نَعْبُدُهُمْ إِلَّا لِيُقَرِّبُونَا إِلَى اللَّهِ زُلْفَىٰ إِنَّ اللَّهَ يَحْكُمُ بَيْنَهُمْ فِي مَا هُمْ فِيهِ يَخْتَلِفُونَ ۗ إِنَّ اللَّهَ لَا يَهْدِي مَنْ هُوَ كَاذِبٌ كَفَّارٌ (3) Ndithudi kumvera ndi kupembedza, ndi kwa Mulungu yekha ndipo iwo amene amasankha ena kuti akhale owasamala m’malo mwa Mulungu amati, “Ife sitiwapembedza iwo ayi koma timafuna kuti iwo atifikitse pafupi ndi Mulungu.” Ndithudi Mulungu adzaweruza pa zonse zimene iwo amatsutsana. Ndithudi Mulungu satsogolera wabodza ndi wosakhulupirira |
لَّوْ أَرَادَ اللَّهُ أَن يَتَّخِذَ وَلَدًا لَّاصْطَفَىٰ مِمَّا يَخْلُقُ مَا يَشَاءُ ۚ سُبْحَانَهُ ۖ هُوَ اللَّهُ الْوَاحِدُ الْقَهَّارُ (4) Ngati Mulungu akadafuna kukhala ndi mwana, ndithudi, Iye akadasankha iwo amene wawafuna kuchokera ku gulu la zolengedwa zake. Koma ulemerero ukhale kwa Iye. Iye ndi Mulungu mmodzi ndi wogonjetsa onse |
خَلَقَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضَ بِالْحَقِّ ۖ يُكَوِّرُ اللَّيْلَ عَلَى النَّهَارِ وَيُكَوِّرُ النَّهَارَ عَلَى اللَّيْلِ ۖ وَسَخَّرَ الشَّمْسَ وَالْقَمَرَ ۖ كُلٌّ يَجْرِي لِأَجَلٍ مُّسَمًّى ۗ أَلَا هُوَ الْعَزِيزُ الْغَفَّارُ (5) Iye adalenga kumwamba ndi dziko lapansi m’choonadi Iye amapanga usiku kuti uphimbe usana ndiponso amapanga usana kuti uphimbe usiku ndipo adalamula dzuwa ndi mwezi kukhala zopanda mphamvu. Chilichonse kumaenda mu msewu wakewake. Ndithudi Iye ndi wamphamvu, ndi wokhululukira nthawi zonse |
خَلَقَكُم مِّن نَّفْسٍ وَاحِدَةٍ ثُمَّ جَعَلَ مِنْهَا زَوْجَهَا وَأَنزَلَ لَكُم مِّنَ الْأَنْعَامِ ثَمَانِيَةَ أَزْوَاجٍ ۚ يَخْلُقُكُمْ فِي بُطُونِ أُمَّهَاتِكُمْ خَلْقًا مِّن بَعْدِ خَلْقٍ فِي ظُلُمَاتٍ ثَلَاثٍ ۚ ذَٰلِكُمُ اللَّهُ رَبُّكُمْ لَهُ الْمُلْكُ ۖ لَا إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ ۖ فَأَنَّىٰ تُصْرَفُونَ (6) Iye adakulengani inu nonse kuchokera kwa munthu mmodzi ndipo adalenga mnzake wolingana naye. Ndipo Iye adakutumizirani inu ng’ombe zisanu ndi zitatu zazimuna ndi zazikazi. Iye adakulengani inu m’mimba mwa amayi anu, chilengedwe chotsagana ndi chilengedwe china, m’magulu atatu a mdima. Iye ndiye Mulungu, Ambuye wanu. Kulibenso Mulungu wina koma Iye yekha. Nanga ndi chifukwa chiyani inu musocheretsedwa |
إِن تَكْفُرُوا فَإِنَّ اللَّهَ غَنِيٌّ عَنكُمْ ۖ وَلَا يَرْضَىٰ لِعِبَادِهِ الْكُفْرَ ۖ وَإِن تَشْكُرُوا يَرْضَهُ لَكُمْ ۗ وَلَا تَزِرُ وَازِرَةٌ وِزْرَ أُخْرَىٰ ۗ ثُمَّ إِلَىٰ رَبِّكُم مَّرْجِعُكُمْ فَيُنَبِّئُكُم بِمَا كُنتُمْ تَعْمَلُونَ ۚ إِنَّهُ عَلِيمٌ بِذَاتِ الصُّدُورِ (7) Ngati inu simukhulupirira, ndithudi, muyenera kudziwa kuti Mulungu ndi woima payekha ndipo alibe nanu kanthu ayi. Iye sakonda kusakhulupirira kwa akapolo ake. Koma ngati inu muthokoza, Iye amasangalala nanu. Ndipo palibe munthu amene adzasenza katundu wa mnzake. Ndipo ndi kwa Ambuye wanu kumene nonse mudzabwerera. Ndipo Iye adzakuuzani zonse zimene mudachita. Ndithudi Iye amadziwa chilichonse chimene chili m’mitima mwanu |
۞ وَإِذَا مَسَّ الْإِنسَانَ ضُرٌّ دَعَا رَبَّهُ مُنِيبًا إِلَيْهِ ثُمَّ إِذَا خَوَّلَهُ نِعْمَةً مِّنْهُ نَسِيَ مَا كَانَ يَدْعُو إِلَيْهِ مِن قَبْلُ وَجَعَلَ لِلَّهِ أَندَادًا لِّيُضِلَّ عَن سَبِيلِهِ ۚ قُلْ تَمَتَّعْ بِكُفْرِكَ قَلِيلًا ۖ إِنَّكَ مِنْ أَصْحَابِ النَّارِ (8) Koma pamene mavuto akhazikika pa munthu, iye amapempha Ambuye wake pafupipafupi koma munthuyo akalandira chisomo chochokera kwa Ambuye wake iye amaiwala zimene amalilira poyamba ndipo amakhazikitsa opikisana ndi Mulungu ndi cholinga chosokoneza anthu ku njira yoyenera ya Mulungu. Nena “Basangalalani ndi kusakhulupirira kwanu kwa kanthawi kochepa. Ndithudi inu ndinu okakhala ku moto!” |
أَمَّنْ هُوَ قَانِتٌ آنَاءَ اللَّيْلِ سَاجِدًا وَقَائِمًا يَحْذَرُ الْآخِرَةَ وَيَرْجُو رَحْمَةَ رَبِّهِ ۗ قُلْ هَلْ يَسْتَوِي الَّذِينَ يَعْلَمُونَ وَالَّذِينَ لَا يَعْلَمُونَ ۗ إِنَّمَا يَتَذَكَّرُ أُولُو الْأَلْبَابِ (9) Kodi iye amene amamvera Mulungu ndipo amadzipereka m’mapemphero nthawi ya usiku ndi kugwada kapena kuimirira popembedza ndiponso amene amaopa za m’moyo umene uli nkudza ndipo amalakalaka chisomo cha Ambuye wake ndi wofanana ndi osakhulupirira? Nena, “Kodi iwo amene amadziwa ndi ofanana ndi iwo osadziwa?” Ndi okhawo amene ndi ozindikira amene adzakumbukira |
قُلْ يَا عِبَادِ الَّذِينَ آمَنُوا اتَّقُوا رَبَّكُمْ ۚ لِلَّذِينَ أَحْسَنُوا فِي هَٰذِهِ الدُّنْيَا حَسَنَةٌ ۗ وَأَرْضُ اللَّهِ وَاسِعَةٌ ۗ إِنَّمَا يُوَفَّى الصَّابِرُونَ أَجْرَهُم بِغَيْرِ حِسَابٍ (10) Nena, “oh inu akapolo anga amene mwakhulupirira! opani Ambuye wanu. Mphotho yokoma ili kuwandikira iwo amene amachita zabwino m’dziko lino. Ndipo dziko la Mulungu lili ndi malo ambiri. Ndipo onse amene amapirira, ndithudi adzalandira mphotho yopanda malire.” |
قُلْ إِنِّي أُمِرْتُ أَنْ أَعْبُدَ اللَّهَ مُخْلِصًا لَّهُ الدِّينَ (11) Nena,“Inendalamulidwakutindizipembedza Mulungu ndi mtima wanga wonse.” |
وَأُمِرْتُ لِأَنْ أَكُونَ أَوَّلَ الْمُسْلِمِينَ (12) “Ndiponso ine ndalamulidwa kukhala woyamba pakati pa iwo amene amadzipereka kwa Mulungu, m’Chisilamu.” |
قُلْ إِنِّي أَخَافُ إِنْ عَصَيْتُ رَبِّي عَذَابَ يَوْمٍ عَظِيمٍ (13) Nena, “Ndithudi ngati ine ndikapanda kumvera Ambuye wanga, ine ndimachita mantha ndi chilango cha tsiku loopsa.” |
قُلِ اللَّهَ أَعْبُدُ مُخْلِصًا لَّهُ دِينِي (14) Nena, “Ndi Mulungu yekha amene ine ndimamupembedza ndi mtima wanga wonse.” |
فَاعْبُدُوا مَا شِئْتُم مِّن دُونِهِ ۗ قُلْ إِنَّ الْخَاسِرِينَ الَّذِينَ خَسِرُوا أَنفُسَهُمْ وَأَهْلِيهِمْ يَوْمَ الْقِيَامَةِ ۗ أَلَا ذَٰلِكَ هُوَ الْخُسْرَانُ الْمُبِينُ (15) Motero inu pembedzani aliyense amene mufuna kuonjezera pa Mulungu. “Ndithudi otayika ndi iwo amene adzataya miyoyo yawo ndi anthu awo pa tsiku lachiweruzo. Ndithudi kumeneku ndi kutayika kwenikweni.” |
لَهُم مِّن فَوْقِهِمْ ظُلَلٌ مِّنَ النَّارِ وَمِن تَحْتِهِمْ ظُلَلٌ ۚ ذَٰلِكَ يُخَوِّفُ اللَّهُ بِهِ عِبَادَهُ ۚ يَا عِبَادِ فَاتَّقُونِ (16) Iwo adzakutidwa ndi moto pamwamba pawo ndi magawo a moto pansi pawo. Ndi chimenechi; Mulungu amaopseza akapolo ake. “Oh inu akapolo anga motero opani Ine.” |
وَالَّذِينَ اجْتَنَبُوا الطَّاغُوتَ أَن يَعْبُدُوهَا وَأَنَابُوا إِلَى اللَّهِ لَهُمُ الْبُشْرَىٰ ۚ فَبَشِّرْ عِبَادِ (17) Ndipo iwo amene sapembedza mafano ndipo amatembenukira kwa Mulungu molapa, iwo adzapeza nkhani zabwino. Kotero auze nkhani yabwino akapolo anga |
الَّذِينَ يَسْتَمِعُونَ الْقَوْلَ فَيَتَّبِعُونَ أَحْسَنَهُ ۚ أُولَٰئِكَ الَّذِينَ هَدَاهُمُ اللَّهُ ۖ وَأُولَٰئِكَ هُمْ أُولُو الْأَلْبَابِ (18) Iwo amene amamva mawu anga ndipo adawatsatira, iwo ndiwo amene Mulungu wawatsogolera ndiponso iwo ndiwo anthu ozindikira |
أَفَمَنْ حَقَّ عَلَيْهِ كَلِمَةُ الْعَذَابِ أَفَأَنتَ تُنقِذُ مَن فِي النَّارِ (19) Kodi iye amene chilango chake chagamulidwa mwachilungamo ndi wofanana ndi munthu wochimwa? Kodi iwe ungamupulumutse iye amene ali m’moto |
لَٰكِنِ الَّذِينَ اتَّقَوْا رَبَّهُمْ لَهُمْ غُرَفٌ مِّن فَوْقِهَا غُرَفٌ مَّبْنِيَّةٌ تَجْرِي مِن تَحْتِهَا الْأَنْهَارُ ۖ وَعْدَ اللَّهِ ۖ لَا يُخْلِفُ اللَّهُ الْمِيعَادَ (20) Koma iwo amene aopa Ambuye wawo ali ndi nyumba zokongola ndi zosanjikizana zimene zamangidwa ndipo pansi pake pamayenda mitsinje. Limeneli ndilo lonjezo la Mulungu ndipo Iye saphwanya lonjezo lake |
أَلَمْ تَرَ أَنَّ اللَّهَ أَنزَلَ مِنَ السَّمَاءِ مَاءً فَسَلَكَهُ يَنَابِيعَ فِي الْأَرْضِ ثُمَّ يُخْرِجُ بِهِ زَرْعًا مُّخْتَلِفًا أَلْوَانُهُ ثُمَّ يَهِيجُ فَتَرَاهُ مُصْفَرًّا ثُمَّ يَجْعَلُهُ حُطَامًا ۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَذِكْرَىٰ لِأُولِي الْأَلْبَابِ (21) Kodi inu simuona mmene Mulungu amatumizira mvula kuchokera kumwamba ndipo amaisiya kuti ilowe pansi m’mitsinje? Mmene Iye amameretsera mbewu za maonekedwe osiyanasiyana zimene zimafota ndipo inu mumaziona zitasanduka zachikasu ndipo amazipanga izo kuti ziume ndi kuthetheka? Ndithudi mu zimenezi muli chikumbutso kwa anthu ozindikira |
أَفَمَن شَرَحَ اللَّهُ صَدْرَهُ لِلْإِسْلَامِ فَهُوَ عَلَىٰ نُورٍ مِّن رَّبِّهِ ۚ فَوَيْلٌ لِّلْقَاسِيَةِ قُلُوبُهُم مِّن ذِكْرِ اللَّهِ ۚ أُولَٰئِكَ فِي ضَلَالٍ مُّبِينٍ (22) Kodi iye amene Mulungu watsekula mtima wake kuti alowe Chisilamu ndi kuona kuwala kochokera kwa Ambuye wake ndi wofanana ndi munthu wouma mtima? Iyayi! Tsoka kwa iwo amene mitima yawo ndi yolimba pokumbukira Mulungu. Ndipo iwo ndi olakwa kwambiri |
اللَّهُ نَزَّلَ أَحْسَنَ الْحَدِيثِ كِتَابًا مُّتَشَابِهًا مَّثَانِيَ تَقْشَعِرُّ مِنْهُ جُلُودُ الَّذِينَ يَخْشَوْنَ رَبَّهُمْ ثُمَّ تَلِينُ جُلُودُهُمْ وَقُلُوبُهُمْ إِلَىٰ ذِكْرِ اللَّهِ ۚ ذَٰلِكَ هُدَى اللَّهِ يَهْدِي بِهِ مَن يَشَاءُ ۚ وَمَن يُضْلِلِ اللَّهُ فَمَا لَهُ مِنْ هَادٍ (23) Mulungu watumiza uthenga wabwino, Buku limene limabwerezabwereza chiphunzitso chake mosiyanasiyana. MatupiaiwoameneamaopaAmbuyewawo, amanjenjemera ndi Bukulo. Ndipo makungu ndi mitima yawo imafewa akamakumbukira Mulungu. Chimenechindichochilangizo cha Mulungu. Iye amatsogolera ndi icho aliyense amene Iye wamufuna. Koma iye amene Mulungu amamusiya kuti asochere, alibe wina woti angamutsogolere |
أَفَمَن يَتَّقِي بِوَجْهِهِ سُوءَ الْعَذَابِ يَوْمَ الْقِيَامَةِ ۚ وَقِيلَ لِلظَّالِمِينَ ذُوقُوا مَا كُنتُمْ تَكْسِبُونَ (24) Kodi iye amene adzapanga nkhope yake kukhala chishango cha chilango chowawa cha tsiku louka kwa akufa adzakhala wofanana ndi iye amene wapulumuka? Ndipo zidzanenedwa kwa anthu ochimwa kuti, “Lawani zipatso za ntchito zanu.” |
كَذَّبَ الَّذِينَ مِن قَبْلِهِمْ فَأَتَاهُمُ الْعَذَابُ مِنْ حَيْثُ لَا يَشْعُرُونَ (25) Iwo amene adalipo kale nawonso adakana kotero chilango chidadza pa iwo kuchokera kumbali imene iwo sanali kuyembekezera |
فَأَذَاقَهُمُ اللَّهُ الْخِزْيَ فِي الْحَيَاةِ الدُّنْيَا ۖ وَلَعَذَابُ الْآخِرَةِ أَكْبَرُ ۚ لَوْ كَانُوا يَعْلَمُونَ (26) Kotero Mulungu adawachititsa manyazi m’moyo uno koma chilango cha m’moyo umene uli nkudza ndi chachikulu iwo akadadziwa |
وَلَقَدْ ضَرَبْنَا لِلنَّاسِ فِي هَٰذَا الْقُرْآنِ مِن كُلِّ مَثَلٍ لَّعَلَّهُمْ يَتَذَكَّرُونَ (27) Ndipo Ife tawaikira anthu, m’Buku la Korani, fanizo la mtundu uliwonse ndi cholinga chakuti azikumbukira |
قُرْآنًا عَرَبِيًّا غَيْرَ ذِي عِوَجٍ لَّعَلَّهُمْ يَتَّقُونَ (28) Korani ya chiyankhulo cha Chiarabu, ndipo mulibe zinthu zolakwa, kuti iwo akhoza kulewa zoipa zimene Mulungu wawalamula |
ضَرَبَ اللَّهُ مَثَلًا رَّجُلًا فِيهِ شُرَكَاءُ مُتَشَاكِسُونَ وَرَجُلًا سَلَمًا لِّرَجُلٍ هَلْ يَسْتَوِيَانِ مَثَلًا ۚ الْحَمْدُ لِلَّهِ ۚ بَلْ أَكْثَرُهُمْ لَا يَعْلَمُونَ (29) Mulungu ali kupereka fanizo la kapolo amene ali ndi mabwana ambiri ndi kapolo amene ali ndi bwana mmodzi yekha. Kodi anthu awiriwa ndi ofanana m’machitidwe awo? Ulemerero ukhale kwa Mulungu! Koma anthu ambiri sadziwa |
إِنَّكَ مَيِّتٌ وَإِنَّهُم مَّيِّتُونَ (30) Ndithudi iwe udzafa ndipo iwo adzafa |
ثُمَّ إِنَّكُمْ يَوْمَ الْقِيَامَةِ عِندَ رَبِّكُمْ تَخْتَصِمُونَ (31) Ndipo patsiku louka kwa akufa, nonse mudzatsutsana wina ndi mnzake pamaso pa Ambuye wanu |
۞ فَمَنْ أَظْلَمُ مِمَّن كَذَبَ عَلَى اللَّهِ وَكَذَّبَ بِالصِّدْقِ إِذْ جَاءَهُ ۚ أَلَيْسَ فِي جَهَنَّمَ مَثْوًى لِّلْكَافِرِينَ (32) Kodi wolakwa kwambiri ndani kuposa iye amene amapeka bodza lokhudza Mulungu ndipo amakana choonadi pamene chidza kwa iye? Kodi ku Gahena kulibe malo okhalamo anthu osakhulupirira |
وَالَّذِي جَاءَ بِالصِّدْقِ وَصَدَّقَ بِهِ ۙ أُولَٰئِكَ هُمُ الْمُتَّقُونَ (33) Ndipo iye amene wabweretsa choonadi ndi amene adakhulupirira choonadi, ndithudi, amenewa ndiwo amene amachita bwino |
لَهُم مَّا يَشَاءُونَ عِندَ رَبِّهِمْ ۚ ذَٰلِكَ جَزَاءُ الْمُحْسِنِينَ (34) Iwo adzapeza zonse zimene afuna kuchokera kwa Ambuye wawo. Imeneyi ndiyo mphotho ya anthu abwino |
لِيُكَفِّرَ اللَّهُ عَنْهُمْ أَسْوَأَ الَّذِي عَمِلُوا وَيَجْزِيَهُمْ أَجْرَهُم بِأَحْسَنِ الَّذِي كَانُوا يَعْمَلُونَ (35) Kuti Mulungu adzawakhululukira zoipitsitsa zimene amachita ndi kuwapatsa mphotho yawo molingana ndi ntchito zawo zabwino zimene adachita |
أَلَيْسَ اللَّهُ بِكَافٍ عَبْدَهُ ۖ وَيُخَوِّفُونَكَ بِالَّذِينَ مِن دُونِهِ ۚ وَمَن يُضْلِلِ اللَّهُ فَمَا لَهُ مِنْ هَادٍ (36) Kodi Mulungu sakwana kuthandiza akapolo ake? Komabe iwo amayesetsa kukuopseza ndi milungu ina yoonjezera pa Iye. Ndipo aliyense amene Mulungu amusocheza alibe wina womutsogolera |
وَمَن يَهْدِ اللَّهُ فَمَا لَهُ مِن مُّضِلٍّ ۗ أَلَيْسَ اللَّهُ بِعَزِيزٍ ذِي انتِقَامٍ (37) Ndipo iye amene Mulungu amamutsogolera palibe wina amene angamusocheze. Kodi Mulungu si wamphamvu zambiri ndiponso Ambuye wodziwa kubwezera |
وَلَئِن سَأَلْتَهُم مَّنْ خَلَقَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضَ لَيَقُولُنَّ اللَّهُ ۚ قُلْ أَفَرَأَيْتُم مَّا تَدْعُونَ مِن دُونِ اللَّهِ إِنْ أَرَادَنِيَ اللَّهُ بِضُرٍّ هَلْ هُنَّ كَاشِفَاتُ ضُرِّهِ أَوْ أَرَادَنِي بِرَحْمَةٍ هَلْ هُنَّ مُمْسِكَاتُ رَحْمَتِهِ ۚ قُلْ حَسْبِيَ اللَّهُ ۖ عَلَيْهِ يَتَوَكَّلُ الْمُتَوَكِّلُونَ (38) Ndipo, ndithudi, ngati ungawafunse kuti, “Kodi ndani adalenga kumwamba ndi dziko lapansi?” Ndithudi iwo adzayankha kuti, “Ndi Mulungu.” Nena, “Kodi zinthu zimene mumapembedza m’malo mwa Mulungu, ngati Mulungu afuna kugwetsa mavuto pa ine, kodi zinthuzo zingathe kuchotsa mavutowo? Kapena ngati Iye alangiza chisomo chake pa ine, kodi izo zingakanize chisomo chake?” Nena, “Mulungu ndi wokwana kwa ine. Mwa Iye onse okhulupirira ayenera kuika chikhulupiriro chawo.” |
قُلْ يَا قَوْمِ اعْمَلُوا عَلَىٰ مَكَانَتِكُمْ إِنِّي عَامِلٌ ۖ فَسَوْفَ تَعْلَمُونَ (39) Nena, “oh inu anthu anga! Gwirani ntchito yanu ndipo ine ndigwira yanga, ndipo inu mudzadziwa.” |
مَن يَأْتِيهِ عَذَابٌ يُخْزِيهِ وَيَحِلُّ عَلَيْهِ عَذَابٌ مُّقِيمٌ (40) Iye amene alandira chilango chochititsa manyazi ndi iye amene alandira chilango chamuyaya |
إِنَّا أَنزَلْنَا عَلَيْكَ الْكِتَابَ لِلنَّاسِ بِالْحَقِّ ۖ فَمَنِ اهْتَدَىٰ فَلِنَفْسِهِ ۖ وَمَن ضَلَّ فَإِنَّمَا يَضِلُّ عَلَيْهَا ۖ وَمَا أَنتَ عَلَيْهِم بِوَكِيلٍ (41) Ndithudi tavumbulutsa kwa iwe Buku la ulangizi kwa anthu mwachoonadi. Kotero aliyense amene atsatira njira yoyenera amapulumutsa mzimu wake ndipo aliyense amene asochera alanga mzimu wake. Ndipo iwe sindiwe msungi wawo ayi |
اللَّهُ يَتَوَفَّى الْأَنفُسَ حِينَ مَوْتِهَا وَالَّتِي لَمْ تَمُتْ فِي مَنَامِهَا ۖ فَيُمْسِكُ الَّتِي قَضَىٰ عَلَيْهَا الْمَوْتَ وَيُرْسِلُ الْأُخْرَىٰ إِلَىٰ أَجَلٍ مُّسَمًّى ۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَآيَاتٍ لِّقَوْمٍ يَتَفَكَّرُونَ (42) Ndi Mulungu amene amachotsa mizimu ya anthu pa nthawi ya imfa ndi mizimu ya anthu a moyo akamagona. Iye amasunga mizimu ya amene adalamula kuti afe ndi kubweza mizimu ya ena mpaka nthawi yawo itakwana. Ndithudi mu zimenezi muli zizindikiro kwa iwo amene amaganiza kwambiri |
أَمِ اتَّخَذُوا مِن دُونِ اللَّهِ شُفَعَاءَ ۚ قُلْ أَوَلَوْ كَانُوا لَا يَمْلِكُونَ شَيْئًا وَلَا يَعْقِلُونَ (43) Kodi iwo asankha ena ngati a mkhalapakati poonjezera pa Mulungu? Nena, “Ngakhale kuti iwo alibe mphamvu iliyonse ndiponso alibe nzeru?” |
قُل لِّلَّهِ الشَّفَاعَةُ جَمِيعًا ۖ لَّهُ مُلْكُ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۖ ثُمَّ إِلَيْهِ تُرْجَعُونَ (44) Nena “Mphamvu zonse za mkhalapakati zili m’manja mwa Mulungu. Iye ndiye Mwini wa chilichonse chimene chili kumwamba ndi pa dziko lapansi. Ndipo ndi kwa Iye kumene mudzabwerera.” |
وَإِذَا ذُكِرَ اللَّهُ وَحْدَهُ اشْمَأَزَّتْ قُلُوبُ الَّذِينَ لَا يُؤْمِنُونَ بِالْآخِرَةِ ۖ وَإِذَا ذُكِرَ الَّذِينَ مِن دُونِهِ إِذَا هُمْ يَسْتَبْشِرُونَ (45) Ndipo pamene dzina la Mulungu lokha litchulidwa, mitima ya iwo amene sakhulupirira za m’moyo umene uli nkudza imakhumudwa koma pamene milungu ina kupatula Mulungu weniweni itchulidwa, iwo amasangalala kwambiri |
قُلِ اللَّهُمَّ فَاطِرَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ عَالِمَ الْغَيْبِ وَالشَّهَادَةِ أَنتَ تَحْكُمُ بَيْنَ عِبَادِكَ فِي مَا كَانُوا فِيهِ يَخْتَلِفُونَ (46) Nena, “oh Mulungu! Namalenga wakumwamba ndi dziko lapansi, Wodziwa zobisika ndi zooneka! Inu mudzaweruza pakati pa akapolo anu pa zimene amatsutsana.” |
وَلَوْ أَنَّ لِلَّذِينَ ظَلَمُوا مَا فِي الْأَرْضِ جَمِيعًا وَمِثْلَهُ مَعَهُ لَافْتَدَوْا بِهِ مِن سُوءِ الْعَذَابِ يَوْمَ الْقِيَامَةِ ۚ وَبَدَا لَهُم مِّنَ اللَّهِ مَا لَمْ يَكُونُوا يَحْتَسِبُونَ (47) Ngakhale anthu ochita zoipa akadakhala ndi zinthu zonse zimene zili pa dziko lapansi kapena zochuluka kuonjezera pa izi, ndithudi iwo akadazipereka izo ngati dipo kuti ziwapulumutse ku zowawa za chilango cha tsiku lachiweruzo. Ndipo chimene samachiganizira, chidzasonyezedwa kwa iwo ndi Mulungu |
وَبَدَا لَهُمْ سَيِّئَاتُ مَا كَسَبُوا وَحَاقَ بِهِم مَّا كَانُوا بِهِ يَسْتَهْزِئُونَ (48) Mphotho za ntchito zawo zonse zoipa zidzaonekera poyera ndipo zonse zimene amazinyoza zidzawazungulira iwo |
فَإِذَا مَسَّ الْإِنسَانَ ضُرٌّ دَعَانَا ثُمَّ إِذَا خَوَّلْنَاهُ نِعْمَةً مِّنَّا قَالَ إِنَّمَا أُوتِيتُهُ عَلَىٰ عِلْمٍ ۚ بَلْ هِيَ فِتْنَةٌ وَلَٰكِنَّ أَكْثَرَهُمْ لَا يَعْلَمُونَ (49) Pamene vuto ligwa pa munthu, iye amatipempha Ife, koma pamene timuonetsa chifundo chathu, iye amati, “Izi zapatsidwa kwa ine chifukwa cha nzeru zanga.” Iyayi! Awa ndi mayesero chabe koma ambiri a iwo sadziwa chilichonse |
قَدْ قَالَهَا الَّذِينَ مِن قَبْلِهِمْ فَمَا أَغْنَىٰ عَنْهُم مَّا كَانُوا يَكْسِبُونَ (50) Ndithudi iwo amene adalipo kale anali kunena chimodzimodzi koma chilichonse chimene anali kuchita chidali chopanda phindu kwa iwo |
فَأَصَابَهُمْ سَيِّئَاتُ مَا كَسَبُوا ۚ وَالَّذِينَ ظَلَمُوا مِنْ هَٰؤُلَاءِ سَيُصِيبُهُمْ سَيِّئَاتُ مَا كَسَبُوا وَمَا هُم بِمُعْجِزِينَ (51) Motero zoipa zimene adachita zidawatsata iwo. Ndipo iwo ochita zoipa a m’badwo uno zotsatira za ntchito zawo zidzawapeza ndipo iwo sadzatha kuthawa ayi |
أَوَلَمْ يَعْلَمُوا أَنَّ اللَّهَ يَبْسُطُ الرِّزْقَ لِمَن يَشَاءُ وَيَقْدِرُ ۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَآيَاتٍ لِّقَوْمٍ يُؤْمِنُونَ (52) Kodi iwo sadziwa kuti Mulungu amapereka moolowa manja kapena monyalapsa kwa aliyense amene Iye wamufuna? Ndithudi mu zimenezi muli zizindikiro kwa iwo amene ama amakhulupirira |
۞ قُلْ يَا عِبَادِيَ الَّذِينَ أَسْرَفُوا عَلَىٰ أَنفُسِهِمْ لَا تَقْنَطُوا مِن رَّحْمَةِ اللَّهِ ۚ إِنَّ اللَّهَ يَغْفِرُ الذُّنُوبَ جَمِيعًا ۚ إِنَّهُ هُوَ الْغَفُورُ الرَّحِيمُ (53) Nena, “Oh akapolo anga amene mwalakwira mizimu yanu! Musakayike za chisomo cha Mulungu. Ndithudi Mulungu amakhululukira machimo onse. Ndithudi Iye amakhululukira nthawi zonse ndipo ndiye Mwini chisoni chosatha.” |
وَأَنِيبُوا إِلَىٰ رَبِّكُمْ وَأَسْلِمُوا لَهُ مِن قَبْلِ أَن يَأْتِيَكُمُ الْعَذَابُ ثُمَّ لَا تُنصَرُونَ (54) Lapani kwa Ambuye wanu nthawi ndi nthawi ndipo mudzipereke kwathunthu kwa Iye chilango chisanadze kwa inu chifukwa sipadzakhala wina wothandiza inu |
وَاتَّبِعُوا أَحْسَنَ مَا أُنزِلَ إِلَيْكُم مِّن رَّبِّكُم مِّن قَبْلِ أَن يَأْتِيَكُمُ الْعَذَابُ بَغْتَةً وَأَنتُمْ لَا تَشْعُرُونَ (55) Ndipotsatiranizabwinozonsezimenezavumbulutsidwa kwa inu kuchokera kwa Ambuye wanu chilango chake chisanadze kwa inu mwadzidzidzi pamene inu simuli kuchiganizira |
أَن تَقُولَ نَفْسٌ يَا حَسْرَتَا عَلَىٰ مَا فَرَّطتُ فِي جَنبِ اللَّهِ وَإِن كُنتُ لَمِنَ السَّاخِرِينَ (56) Mwina mzimu ungadzanene kuti, “Oh tsoka kwa ine chifukwa chakulephera kwanga pokwaniritsa udindo wanga kwa Mulungu! Ndithudi ine ndidali mmodzi wa iwo amene anali kunyoza.” |
أَوْ تَقُولَ لَوْ أَنَّ اللَّهَ هَدَانِي لَكُنتُ مِنَ الْمُتَّقِينَ (57) Kapena akhoza kunena kuti, “Akadakhala kuti Mulungu adanditsogolera, ndithudi, ine ndikadakhala m’gulu la anthu angwiro.” |
أَوْ تَقُولَ حِينَ تَرَى الْعَذَابَ لَوْ أَنَّ لِي كَرَّةً فَأَكُونَ مِنَ الْمُحْسِنِينَ (58) Kapena pamene aona akhoza kunena chilango kuti, “N’kadakhala ndidali ndi mwayi wina, ndithudi, ndikadakhala m’gulu la iwo ochita zabwino.” |
بَلَىٰ قَدْ جَاءَتْكَ آيَاتِي فَكَذَّبْتَ بِهَا وَاسْتَكْبَرْتَ وَكُنتَ مِنَ الْكَافِرِينَ (59) Inde! Ndithudi ulangizi wanga unadza kwa inu koma inu munaukana. Inu munali kunyada ndipo munali m’gulu la anthu osakhulupirira |
وَيَوْمَ الْقِيَامَةِ تَرَى الَّذِينَ كَذَبُوا عَلَى اللَّهِ وُجُوهُهُم مُّسْوَدَّةٌ ۚ أَلَيْسَ فِي جَهَنَّمَ مَثْوًى لِّلْمُتَكَبِّرِينَ (60) Ndipo patsiku louka kwa akufa, iwe udzaona nkhope zonse za amene amanamizira Mulungu, zitadetsedwa. Kodi ku Gahena kulibe malo okhalako anthu a mwano |
وَيُنَجِّي اللَّهُ الَّذِينَ اتَّقَوْا بِمَفَازَتِهِمْ لَا يَمَسُّهُمُ السُّوءُ وَلَا هُمْ يَحْزَنُونَ (61) Ndipo Mulungu adzapereka onse amene amalewa zoipa ku malo awo opambana. Palibe choipa chimene chidzagwa pa iwo, ndipo iwo sadzamva chisoni ayi |
اللَّهُ خَالِقُ كُلِّ شَيْءٍ ۖ وَهُوَ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ وَكِيلٌ (62) Mulungu ndiye Namalenga wa zinthu zonse, Wosamalira ndiponso Mgawi wa zinthu zonse |
لَّهُ مَقَالِيدُ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۗ وَالَّذِينَ كَفَرُوا بِآيَاتِ اللَّهِ أُولَٰئِكَ هُمُ الْخَاسِرُونَ (63) Chake ndi chuma chonse cha kumwamba ndi cha padziko lapansi. Ndipo iwo amene sakhulupirira muchivumbulutso cha Mulungu, amenewo ndiwo amene adzakhala olephera |
قُلْ أَفَغَيْرَ اللَّهِ تَأْمُرُونِّي أَعْبُدُ أَيُّهَا الْجَاهِلُونَ (64) Nena, “Kodi inu muli kundilamula kuti ndipembedze wina wake osati Mulungu? Oh inu anthu osadziwa!” |
وَلَقَدْ أُوحِيَ إِلَيْكَ وَإِلَى الَّذِينَ مِن قَبْلِكَ لَئِنْ أَشْرَكْتَ لَيَحْبَطَنَّ عَمَلُكَ وَلَتَكُونَنَّ مِنَ الْخَاسِرِينَ (65) Ndipo, ndithudi, zavumbulutsidwa kwa iwe ndi kwa iwo amene adalipo kale kuti, “Ndithudi ngati inu muphatikiza Mulungu ndi china chake, ndithudi, ntchito zanu zidzakhala zopanda phindu. Ndithudi inu mudzakhala m’gulu la anthu olephera.” |
بَلِ اللَّهَ فَاعْبُدْ وَكُن مِّنَ الشَّاكِرِينَ (66) Iyayi! Koma iwe upembedze Mulungu m’modzi yekha ndipo khala m’gulu la iwo amene amathokoza |
وَمَا قَدَرُوا اللَّهَ حَقَّ قَدْرِهِ وَالْأَرْضُ جَمِيعًا قَبْضَتُهُ يَوْمَ الْقِيَامَةِ وَالسَّمَاوَاتُ مَطْوِيَّاتٌ بِيَمِينِهِ ۚ سُبْحَانَهُ وَتَعَالَىٰ عَمَّا يُشْرِكُونَ (67) Ndipo iwo sadamulemekeze Mulungu ndi ulemu umene uli woyenera kwa Iye ndipo dziko lapansi lidzakhala pa chikhato pake pa tsiku lachiweruzo. Kumwamba kudzakulungidwa m’dzanja lake lamanja. Ulemerero ukhale kwa Iye ndipo Iye ndi woposa mafano amene amamufanizira nawo |
وَنُفِخَ فِي الصُّورِ فَصَعِقَ مَن فِي السَّمَاوَاتِ وَمَن فِي الْأَرْضِ إِلَّا مَن شَاءَ اللَّهُ ۖ ثُمَّ نُفِخَ فِيهِ أُخْرَىٰ فَإِذَا هُمْ قِيَامٌ يَنظُرُونَ (68) Ndipo lipenga lidzalizidwa kotero onse amene ali kumwamba ndi onse amene ali padziko lapansi adzakomoka kupatula okhawo amene Mulungu wawafuna. Ndipo lidzalizidwanso kachiwiri ndipo onse adzakhala choimirira ndi kumangoyembekezera |
وَأَشْرَقَتِ الْأَرْضُ بِنُورِ رَبِّهَا وَوُضِعَ الْكِتَابُ وَجِيءَ بِالنَّبِيِّينَ وَالشُّهَدَاءِ وَقُضِيَ بَيْنَهُم بِالْحَقِّ وَهُمْ لَا يُظْلَمُونَ (69) Ndipo dziko lapansi lidzawala ndi muuni wa Ambuye wako ndipo Buku lidzatsekulidwa. Atumwi ndi mboni zidzaitanidwa ndipo chiweruzo chidzaperekedwa mwachilungamo pakati pawo ndipo iwo sadzaponderezedwa konse |
وَوُفِّيَتْ كُلُّ نَفْسٍ مَّا عَمِلَتْ وَهُوَ أَعْلَمُ بِمَا يَفْعَلُونَ (70) Ndipo mzimu uliwonse udzalipidwa mokwanira molingana ndi zimene udachita ndipo Iye amadziwa bwino zonse zimene mumachita |
وَسِيقَ الَّذِينَ كَفَرُوا إِلَىٰ جَهَنَّمَ زُمَرًا ۖ حَتَّىٰ إِذَا جَاءُوهَا فُتِحَتْ أَبْوَابُهَا وَقَالَ لَهُمْ خَزَنَتُهَا أَلَمْ يَأْتِكُمْ رُسُلٌ مِّنكُمْ يَتْلُونَ عَلَيْكُمْ آيَاتِ رَبِّكُمْ وَيُنذِرُونَكُمْ لِقَاءَ يَوْمِكُمْ هَٰذَا ۚ قَالُوا بَلَىٰ وَلَٰكِنْ حَقَّتْ كَلِمَةُ الْعَذَابِ عَلَى الْكَافِرِينَ (71) Ndipo onse osakhulupirira adzatengedwa paulendo wa ku Gahena m’magulumagulu ndipo pamene azidzafika pafupi, makomo ake adzatsekulidwa ndipo oyang’anira kumeneko adzati kwa iwo, “Kodi sikunadze kwa inu Atumwi a mtundu wanu kukulalikirani ulangizi wa Ambuye wanu ndi kukuchenjezani za kukumana kwanu ndi tsiku lino?” Iwo adzati, “Inde!” Koma chilango chakwaniritsidwa kwa anthu osakhulupirira |
قِيلَ ادْخُلُوا أَبْوَابَ جَهَنَّمَ خَالِدِينَ فِيهَا ۖ فَبِئْسَ مَثْوَى الْمُتَكَبِّرِينَ (72) Iwo adzauzidwa kuti, “Lowani nonse m’zipata za Gahena kuti muzikhala m’menemo.” Ndipo ndi oipa malowa womwe anthu onyada adzakhaleko |
وَسِيقَ الَّذِينَ اتَّقَوْا رَبَّهُمْ إِلَى الْجَنَّةِ زُمَرًا ۖ حَتَّىٰ إِذَا جَاءُوهَا وَفُتِحَتْ أَبْوَابُهَا وَقَالَ لَهُمْ خَزَنَتُهَا سَلَامٌ عَلَيْكُمْ طِبْتُمْ فَادْخُلُوهَا خَالِدِينَ (73) Ndipo onse amene amaopa Ambuye wawo adzatsogozedwa ku Paradiso m’magulumagulu. Ndipo pamene iwo azidzafika pafupi, taonani makomo azipata adzatsekulidwa, ndipo oyang’anira kumeneko adzati, “Mtendere ukhale kwa inu!” Inu mudzakhala mosangalala kotero lowani kuti muzikhala momwemo.” |
وَقَالُوا الْحَمْدُ لِلَّهِ الَّذِي صَدَقَنَا وَعْدَهُ وَأَوْرَثَنَا الْأَرْضَ نَتَبَوَّأُ مِنَ الْجَنَّةِ حَيْثُ نَشَاءُ ۖ فَنِعْمَ أَجْرُ الْعَامِلِينَ (74) Ndipo iwo adzati, “Ulemerero ukhale kwa Mulungu amene wakwaniritsa kwa ife lonjezo lake ndipo watilola ife kuti tikhale m’dziko ili. Ife tidzakhala m’minda imene tifuna.” Kotero yabwino ndi mphotho ya anthu ogwira ntchito zabwino |
وَتَرَى الْمَلَائِكَةَ حَافِّينَ مِنْ حَوْلِ الْعَرْشِ يُسَبِّحُونَ بِحَمْدِ رَبِّهِمْ ۖ وَقُضِيَ بَيْنَهُم بِالْحَقِّ وَقِيلَ الْحَمْدُ لِلَّهِ رَبِّ الْعَالَمِينَ (75) Ndipo iwe udzaona angelo atazungulira Mpando Wachifumu mbali zonse, ali kuimba mayamiko ndi kulemekeza Ambuye wawo. Ndipo chiweruzo chidzaperekedwa kwa zolengedwa zonse mwachilungamo ndipo kudzanenedwa kuti, “Kuyamikidwa konse ndi kwa Mulungu, Ambuye wa zolengedwa zonse.” Sura 40 • al-mu’min |