Quran with Chichewa translation - Surah Az-Zumar ayat 6 - الزُّمَر - Page - Juz 23
﴿خَلَقَكُم مِّن نَّفۡسٖ وَٰحِدَةٖ ثُمَّ جَعَلَ مِنۡهَا زَوۡجَهَا وَأَنزَلَ لَكُم مِّنَ ٱلۡأَنۡعَٰمِ ثَمَٰنِيَةَ أَزۡوَٰجٖۚ يَخۡلُقُكُمۡ فِي بُطُونِ أُمَّهَٰتِكُمۡ خَلۡقٗا مِّنۢ بَعۡدِ خَلۡقٖ فِي ظُلُمَٰتٖ ثَلَٰثٖۚ ذَٰلِكُمُ ٱللَّهُ رَبُّكُمۡ لَهُ ٱلۡمُلۡكُۖ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَۖ فَأَنَّىٰ تُصۡرَفُونَ ﴾
[الزُّمَر: 6]
﴿خلقكم من نفس واحدة ثم جعل منها زوجها وأنـزل لكم من الأنعام﴾ [الزُّمَر: 6]
Khaled Ibrahim Betala “Adakulengani kuchokera mu mzimu umodzi (womwe ndi Adam; tate wa anthu). Ndipo kenako adalenga kuchokera mu mzimu umenewo mnzake, (mkazi wake, Hawa); ndipo adakutsitsirani mitundu isanu ndi itatu ya nyama ziwiriziwiri (zomwe ndi: Ngamira yaimuna ndi yaikazi, ng’ombe yaimuna ndi yaikazi, mbuzi yaimuna ndi yaikazi ndi nkhosa yaimuna ndi yaikazi. Zonse pamodzi, zisanu ndi zitatu, zomwe mumathandizidwa nazo kwambiri). Amakuumbani m’mimba mwa mayi anu mkaumbidwe kosiyanasiyana, mu mdima utatu; (mu mdima wa mimba, chiberekero ndi mdima wa nembanemba). Ameneyo (adakuchitirani zonsezi), ndi Allah, Mleri wanu; ufumu ngwa Iye. Palibe wopembedzedwa mwa choona, koma Iye. Kodi nanga mukutembunuzidwa bwanji (kusiya Allah) |