Quran with Chichewa translation - Surah An-Nisa’ ayat 153 - النِّسَاء - Page - Juz 6
﴿يَسۡـَٔلُكَ أَهۡلُ ٱلۡكِتَٰبِ أَن تُنَزِّلَ عَلَيۡهِمۡ كِتَٰبٗا مِّنَ ٱلسَّمَآءِۚ فَقَدۡ سَأَلُواْ مُوسَىٰٓ أَكۡبَرَ مِن ذَٰلِكَ فَقَالُوٓاْ أَرِنَا ٱللَّهَ جَهۡرَةٗ فَأَخَذَتۡهُمُ ٱلصَّٰعِقَةُ بِظُلۡمِهِمۡۚ ثُمَّ ٱتَّخَذُواْ ٱلۡعِجۡلَ مِنۢ بَعۡدِ مَا جَآءَتۡهُمُ ٱلۡبَيِّنَٰتُ فَعَفَوۡنَا عَن ذَٰلِكَۚ وَءَاتَيۡنَا مُوسَىٰ سُلۡطَٰنٗا مُّبِينٗا ﴾
[النِّسَاء: 153]
﴿يسألك أهل الكتاب أن تنـزل عليهم كتابا من السماء فقد سألوا موسى﴾ [النِّسَاء: 153]
Khaled Ibrahim Betala “Anthu amene adapatsidwa buku (Ayuda) akukupempha (iwe Mtumiki) kuti uwatsitsire buku kuchokera kumwamba. Ndithudi, adampemphanso Mûsa zazikulu kuposa zimenezi pomwe adati: “Tiwonetse Allah poyera.” Choncho udawagwira moto wamphenzi chifukwa cha kuipitsa kwao (motowo udachotsa miyoyo yawo chifukwa cha kusakhulupirira kwawo. Zitatero Allah adawapatsa moyo kachiwiri). Kenako iwo adapanga thole (mwana wang’ombe monga mulungu wawo) pambuyo powafikira chisonyezo choonekera. Koma tidawakhululukira zimenezo, ndipo tidampatsa Mûsa chisonyezo choonekera poyera |