×

Ndipo munthu wamwamuna wokhulupirira wa m’gulu la anthu a Farawo amene adabisa 40:28 Chichewa translation

Quran infoChichewaSurah Ghafir ⮕ (40:28) ayat 28 in Chichewa

40:28 Surah Ghafir ayat 28 in Chichewa (نيانجا)

Quran with Chichewa translation - Surah Ghafir ayat 28 - غَافِر - Page - Juz 24

﴿وَقَالَ رَجُلٞ مُّؤۡمِنٞ مِّنۡ ءَالِ فِرۡعَوۡنَ يَكۡتُمُ إِيمَٰنَهُۥٓ أَتَقۡتُلُونَ رَجُلًا أَن يَقُولَ رَبِّيَ ٱللَّهُ وَقَدۡ جَآءَكُم بِٱلۡبَيِّنَٰتِ مِن رَّبِّكُمۡۖ وَإِن يَكُ كَٰذِبٗا فَعَلَيۡهِ كَذِبُهُۥۖ وَإِن يَكُ صَادِقٗا يُصِبۡكُم بَعۡضُ ٱلَّذِي يَعِدُكُمۡۖ إِنَّ ٱللَّهَ لَا يَهۡدِي مَنۡ هُوَ مُسۡرِفٞ كَذَّابٞ ﴾
[غَافِر: 28]

Ndipo munthu wamwamuna wokhulupirira wa m’gulu la anthu a Farawo amene adabisa chikhulupiriro chake adati, “Kodi inu mudzapha munthu chifukwa chakuti wanena kuti Ambuye wanga ndi Mulungu pamene iye wadza kwa inu ndi zizindikiro zooneka zochokera kwa Ambuye wanu? Ndipo ngati iye ndi wabodza tchimo likhale pa iye yekha koma ngati iye ali kunena zoona, tsoka limene anena lidzagwa pa inu. Ndithudi Mulungu satsogolera munthu woswa malamulo ndi wabodza.”

❮ Previous Next ❯

ترجمة: وقال رجل مؤمن من آل فرعون يكتم إيمانه أتقتلون رجلا أن يقول, باللغة نيانجا

﴿وقال رجل مؤمن من آل فرعون يكتم إيمانه أتقتلون رجلا أن يقول﴾ [غَافِر: 28]

Khaled Ibrahim Betala
“Ndipo munthu wokhulupirira, wochokera kubanja la Farawo yemwe adali kubisa chikhulupiliro chake, adawalankhula (anthu ake): “Kodi muphe munthu chifukwa chakuti iye akunena kuti: ‘Mbuye wanga ndi Allah,’ chikhalirecho wakubweretserani zisonyezo zoonekera poyera, zochokera kwa Mbuye wanu? Ndipo ngati ali wabodza pa zomwe akunena ndiye kuti kuipa kwa bodzalo kum’bwerera yekha. Koma ngati ali woona (pazomwe akukulonjezani), ndiye kuti gawo lina la zomwe (chilango) akukulonjezani likupezani; ndithu Allah saongola munthu wopyola malire, wabodza la mkunkhuniza!”
❮ Previous Next ❯

Verse in more languages

Transliteration Bangla Bosnian German English Persian French Hindi Indonesian Kazakh Dutch Russian Spanish Turkish Urdu Uzbek