حم (1) Ha-Mim |
تَنزِيلُ الْكِتَابِ مِنَ اللَّهِ الْعَزِيزِ الْعَلِيمِ (2) Chivumbulutso cha Buku ili ndi chochokera kwa Mulungu, wamphamvu ndi wodziwa zonse |
غَافِرِ الذَّنبِ وَقَابِلِ التَّوْبِ شَدِيدِ الْعِقَابِ ذِي الطَّوْلِ ۖ لَا إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ ۖ إِلَيْهِ الْمَصِيرُ (3) Iye ndi amene amakhululukira machimo ndipo amavomera kulapa. Iye ndi wankhanza popereka chilango ndi Mwini chinthu chilichonse, ndipo kulibe mulungu wina koma Iye yekha. Kwa Iye chilichonse chidzabwerera |
مَا يُجَادِلُ فِي آيَاتِ اللَّهِ إِلَّا الَّذِينَ كَفَرُوا فَلَا يَغْرُرْكَ تَقَلُّبُهُمْ فِي الْبِلَادِ (4) Palibe amene amatsutsa chivumbulutso cha Mulungu kupatula okhawo amene sakhulupirira. Kotero usanyengedwe ndi kuyendayenda kwawo kwa m’mizinda |
كَذَّبَتْ قَبْلَهُمْ قَوْمُ نُوحٍ وَالْأَحْزَابُ مِن بَعْدِهِمْ ۖ وَهَمَّتْ كُلُّ أُمَّةٍ بِرَسُولِهِمْ لِيَأْخُذُوهُ ۖ وَجَادَلُوا بِالْبَاطِلِ لِيُدْحِضُوا بِهِ الْحَقَّ فَأَخَذْتُهُمْ ۖ فَكَيْفَ كَانَ عِقَابِ (5) Anthu a Nowa ndi anthu a magulu ena amene adadza pambuyo pawo adakana Atumwi, ndipo mtundu uliwonse udachita chiwembu pa Mtumwi wawo, kuti amugwire koteroanalikutsutsananayepazinthuzabodzandicholinga choletsa choonadi. Koma Ine ndidawaononga iwo! Kodi chilango changa chidali chowawa bwanji |
وَكَذَٰلِكَ حَقَّتْ كَلِمَتُ رَبِّكَ عَلَى الَّذِينَ كَفَرُوا أَنَّهُمْ أَصْحَابُ النَّارِ (6) Kotero mawu a Ambuye wako adakwaniritsidwa kwa osakhulupirira ndipo iwo ndi amene adzakhala ku Moto |
الَّذِينَ يَحْمِلُونَ الْعَرْشَ وَمَنْ حَوْلَهُ يُسَبِّحُونَ بِحَمْدِ رَبِّهِمْ وَيُؤْمِنُونَ بِهِ وَيَسْتَغْفِرُونَ لِلَّذِينَ آمَنُوا رَبَّنَا وَسِعْتَ كُلَّ شَيْءٍ رَّحْمَةً وَعِلْمًا فَاغْفِرْ لِلَّذِينَ تَابُوا وَاتَّبَعُوا سَبِيلَكَ وَقِهِمْ عَذَابَ الْجَحِيمِ (7) Iwo amene amasunga Mpando wachifumu ndiponso iwo amene amauzungulira iwo, amatamanda Ambuye wawo ndi kukhulupirira mwa Iye ndipo amapempha chitetezo m’malo mwa iwo amene akhulupirira. “Ambuye wathu! Chifundo ndi nzeru zanu zimakhudza aliyense kotero atetezeni onse amene adza kwa Inu ndi kutsatira njira yanu ndiponso apulumutseni iwo ku chilango cha ku Gahena!” |
رَبَّنَا وَأَدْخِلْهُمْ جَنَّاتِ عَدْنٍ الَّتِي وَعَدتَّهُمْ وَمَن صَلَحَ مِنْ آبَائِهِمْ وَأَزْوَاجِهِمْ وَذُرِّيَّاتِهِمْ ۚ إِنَّكَ أَنتَ الْعَزِيزُ الْحَكِيمُ (8) “Ambuye wathu! Alowetseni ku minda ya Paradiso imene inu mudawalonjeza iwo ndiponso iwo amene amachita zabwino, pakati pa atate, akazi ndi ana awo. Ndithudi Inu ndinu wamphamvu ndi wanzeru kwambiri |
وَقِهِمُ السَّيِّئَاتِ ۚ وَمَن تَقِ السَّيِّئَاتِ يَوْمَئِذٍ فَقَدْ رَحِمْتَهُ ۚ وَذَٰلِكَ هُوَ الْفَوْزُ الْعَظِيمُ (9) “Ndipo apulumutseni ku ntchito zoipa. Aliyense amene Inu mumupulumutsa ku zoipa tsiku lalero ndiye kuti Inu mwamuonetsa chisoni chanu ndipo kumeneko ndiko kupambana kwambiri |
إِنَّ الَّذِينَ كَفَرُوا يُنَادَوْنَ لَمَقْتُ اللَّهِ أَكْبَرُ مِن مَّقْتِكُمْ أَنفُسَكُمْ إِذْ تُدْعَوْنَ إِلَى الْإِيمَانِ فَتَكْفُرُونَ (10) Ndithudi iwo amene sakhulupirira adzamva mkuwo ukuti, “Ndithudi mkwiyo wa Mulungu pa inu ndi waukulu kuposa chidani chimene inuyo mumadzionetsera nokha poona kuti munali kuitanidwa kuti mukhulupirire koma inu munali kukana.” |
قَالُوا رَبَّنَا أَمَتَّنَا اثْنَتَيْنِ وَأَحْيَيْتَنَا اثْنَتَيْنِ فَاعْتَرَفْنَا بِذُنُوبِنَا فَهَلْ إِلَىٰ خُرُوجٍ مِّن سَبِيلٍ (11) Iwo adzati, “Ambuye wathu mudatipha kawiri konse ndipo mudatipatsa moyo kawiri. Tsopano ife tivomereza kuchimwa kwathu. Kodi sitingathe kupulumutsidwa ku chilango cha ku Moto?” |
ذَٰلِكُم بِأَنَّهُ إِذَا دُعِيَ اللَّهُ وَحْدَهُ كَفَرْتُمْ ۖ وَإِن يُشْرَكْ بِهِ تُؤْمِنُوا ۚ فَالْحُكْمُ لِلَّهِ الْعَلِيِّ الْكَبِيرِ (12) “Ichi ndi chifukwa chakuti pamene dzina la Mulungu lokha linali kupembedzedwa, inu simudakhulupirire koma pamene milungu ina inali kupembedzedwa, inu mudakhulupirira. Kotero Mwini wake wa chiweruzo ndi Mulungu Wapamwamba ndi Wamkulukulu.” |
هُوَ الَّذِي يُرِيكُمْ آيَاتِهِ وَيُنَزِّلُ لَكُم مِّنَ السَّمَاءِ رِزْقًا ۚ وَمَا يَتَذَكَّرُ إِلَّا مَن يُنِيبُ (13) Iye ndiye amene amakulangizani inu zizindikiro zake ndipo amakutumizirani chakudya kuchokera ku mitambo. Koma okhawo amene akumbukira ndiwo amene amabwererakwa Mulungu |
فَادْعُوا اللَّهَ مُخْلِصِينَ لَهُ الدِّينَ وَلَوْ كَرِهَ الْكَافِرُونَ (14) Moteropembedzani Mulungu mmodzi yekha, ngakhale kuti anthu osakhulupirira sasangalala |
رَفِيعُ الدَّرَجَاتِ ذُو الْعَرْشِ يُلْقِي الرُّوحَ مِنْ أَمْرِهِ عَلَىٰ مَن يَشَاءُ مِنْ عِبَادِهِ لِيُنذِرَ يَوْمَ التَّلَاقِ (15) Wokweza maudindo anthu okhulupirira ndi Mwini Mpando wachifumu. Iye amatumiza chikumbutso chake kwa aliyense wa akapolo ake amene Iye wamufuna kuti akhoza kuchenjeza anthu za tsiku lachiweruzo |
يَوْمَ هُم بَارِزُونَ ۖ لَا يَخْفَىٰ عَلَى اللَّهِ مِنْهُمْ شَيْءٌ ۚ لِّمَنِ الْمُلْكُ الْيَوْمَ ۖ لِلَّهِ الْوَاحِدِ الْقَهَّارِ (16) Tsiku limene onse adzadza pamodzi, sipadzakhala china chilichonse chobisika kwa Mulungu. Kodi ndani adzakhala ndi ulamuliro wamphamvu pa tsikuli? Ndi Mulungu, mmodzi yekha, Mwini mphamvu zonse |
الْيَوْمَ تُجْزَىٰ كُلُّ نَفْسٍ بِمَا كَسَبَتْ ۚ لَا ظُلْمَ الْيَوْمَ ۚ إِنَّ اللَّهَ سَرِيعُ الْحِسَابِ (17) Tsiku limeneli, mzimu uliwonse udzalandira malipiro ake. Pa tsiku limeneli sikudzakhala kuponderezana. Ndithudi Mulungu ndi wachangu pobwezera |
وَأَنذِرْهُمْ يَوْمَ الْآزِفَةِ إِذِ الْقُلُوبُ لَدَى الْحَنَاجِرِ كَاظِمِينَ ۚ مَا لِلظَّالِمِينَ مِنْ حَمِيمٍ وَلَا شَفِيعٍ يُطَاعُ (18) Achenjeze iwo za tsiku limene lili pafupi kudza, limene mitima idzadza mpaka pakhosi ndi kuwakomola. Palibe bwenzi la pamtima kapena mkhalapakati wa anthu ochita zoipa amene adzayankhulire |
يَعْلَمُ خَائِنَةَ الْأَعْيُنِ وَمَا تُخْفِي الصُّدُورُ (19) Mulungu amadziwa chinyengo cha maso ndi zimene mitima imabisa |
وَاللَّهُ يَقْضِي بِالْحَقِّ ۖ وَالَّذِينَ يَدْعُونَ مِن دُونِهِ لَا يَقْضُونَ بِشَيْءٍ ۗ إِنَّ اللَّهَ هُوَ السَّمِيعُ الْبَصِيرُ (20) Ndipo Mulungu amaweruza mwachilungamo pamene iwo amene amapembedzedwa oonjezera pa Iye sangathe kuweruza. Ndithudi Mulungu amamva ndiponso amaona |
۞ أَوَلَمْ يَسِيرُوا فِي الْأَرْضِ فَيَنظُرُوا كَيْفَ كَانَ عَاقِبَةُ الَّذِينَ كَانُوا مِن قَبْلِهِمْ ۚ كَانُوا هُمْ أَشَدَّ مِنْهُمْ قُوَّةً وَآثَارًا فِي الْأَرْضِ فَأَخَذَهُمُ اللَّهُ بِذُنُوبِهِمْ وَمَا كَانَ لَهُم مِّنَ اللَّهِ مِن وَاقٍ (21) Kodi iwo sadayende pa dziko lapansi ndi kuona zimene zidawachitikira anthu a makedzana? Iwo adali a mphamvu kuposa awa. Koma Mulungu adawalanga chifukwa cha zoipa zawo. Ndipo iwo adalibe wina aliyense wowateteza kwa Mulungu |
ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمْ كَانَت تَّأْتِيهِمْ رُسُلُهُم بِالْبَيِّنَاتِ فَكَفَرُوا فَأَخَذَهُمُ اللَّهُ ۚ إِنَّهُ قَوِيٌّ شَدِيدُ الْعِقَابِ (22) Ichi ndi chifukwa chakuti Atumwi awo adadza kwa iwo ndi zizindikiro zooneka ndi maso koma iwo adakana Atumwiwo. Kotero Mulungu adawaononga iwo. Ndithudi! Iye ndi Wamphamvu ndipo chilango chake ndi chowawa kwambiri |
وَلَقَدْ أَرْسَلْنَا مُوسَىٰ بِآيَاتِنَا وَسُلْطَانٍ مُّبِينٍ (23) Ndipo, ndithudi, tidamutumiza Mose ndi uthenga wathu ndi ulamuliro wooneka |
إِلَىٰ فِرْعَوْنَ وَهَامَانَ وَقَارُونَ فَقَالُوا سَاحِرٌ كَذَّابٌ (24) Kwa Farawo, Hamani ndi Karuni koma iwo adati, “Munthu wamatsenga ndi wabodza.” |
فَلَمَّا جَاءَهُم بِالْحَقِّ مِنْ عِندِنَا قَالُوا اقْتُلُوا أَبْنَاءَ الَّذِينَ آمَنُوا مَعَهُ وَاسْتَحْيُوا نِسَاءَهُمْ ۚ وَمَا كَيْدُ الْكَافِرِينَ إِلَّا فِي ضَلَالٍ (25) Ndipo pamene iye adawauza choonadi chochokera kwa Ife, iwo adati, “Iphani ana onse aamuna a anthu amene akhulupirira ndi iye ndipo musunge ana awo aakazi.” Koma ziwembu za anthu osakhulupirira sizitha bwino chifukwa zilibe maziko enieni |
وَقَالَ فِرْعَوْنُ ذَرُونِي أَقْتُلْ مُوسَىٰ وَلْيَدْعُ رَبَّهُ ۖ إِنِّي أَخَافُ أَن يُبَدِّلَ دِينَكُمْ أَوْ أَن يُظْهِرَ فِي الْأَرْضِ الْفَسَادَ (26) Ndipo Farawo adati, “Mundisiye ine kuti ndiphe Mose ndipo musiyeni iye kuti apemphe kwa Ambuye wake. Ndithudi ine ndiopa kuti iye adzasintha chipembedzo chanu ndi kuyambitsa chisokonezo m’dziko.” |
وَقَالَ مُوسَىٰ إِنِّي عُذْتُ بِرَبِّي وَرَبِّكُم مِّن كُلِّ مُتَكَبِّرٍ لَّا يُؤْمِنُ بِيَوْمِ الْحِسَابِ (27) Ndipo Mose adati, “Ndithudi ine ndithawira kwa Ambuye wanga ndi Ambuye wanu kuti anditeteze kwa aliyense wamwano amene sakhulupirira mu tsiku lachiweruzo.” |
وَقَالَ رَجُلٌ مُّؤْمِنٌ مِّنْ آلِ فِرْعَوْنَ يَكْتُمُ إِيمَانَهُ أَتَقْتُلُونَ رَجُلًا أَن يَقُولَ رَبِّيَ اللَّهُ وَقَدْ جَاءَكُم بِالْبَيِّنَاتِ مِن رَّبِّكُمْ ۖ وَإِن يَكُ كَاذِبًا فَعَلَيْهِ كَذِبُهُ ۖ وَإِن يَكُ صَادِقًا يُصِبْكُم بَعْضُ الَّذِي يَعِدُكُمْ ۖ إِنَّ اللَّهَ لَا يَهْدِي مَنْ هُوَ مُسْرِفٌ كَذَّابٌ (28) Ndipo munthu wamwamuna wokhulupirira wa m’gulu la anthu a Farawo amene adabisa chikhulupiriro chake adati, “Kodi inu mudzapha munthu chifukwa chakuti wanena kuti Ambuye wanga ndi Mulungu pamene iye wadza kwa inu ndi zizindikiro zooneka zochokera kwa Ambuye wanu? Ndipo ngati iye ndi wabodza tchimo likhale pa iye yekha koma ngati iye ali kunena zoona, tsoka limene anena lidzagwa pa inu. Ndithudi Mulungu satsogolera munthu woswa malamulo ndi wabodza.” |
يَا قَوْمِ لَكُمُ الْمُلْكُ الْيَوْمَ ظَاهِرِينَ فِي الْأَرْضِ فَمَن يَنصُرُنَا مِن بَأْسِ اللَّهِ إِن جَاءَنَا ۚ قَالَ فِرْعَوْنُ مَا أُرِيكُمْ إِلَّا مَا أَرَىٰ وَمَا أَهْدِيكُمْ إِلَّا سَبِيلَ الرَّشَادِ (29) “oh inu anthu anga!wanu ndi ufumu walero. Inu muli ndi ulamuliro m’dziko koma ndani amene adzatithandiza ife ku chilango cha Mulungu ngati icho chitagwa pa ife?” Farawo adati, “Ine ndili kungokuuzani zinthu zimene ndimaona ndiponso ndili kukutsogolerani ku njira yoyenera.” |
وَقَالَ الَّذِي آمَنَ يَا قَوْمِ إِنِّي أَخَافُ عَلَيْكُم مِّثْلَ يَوْمِ الْأَحْزَابِ (30) Ndipo iye amene adakhulupirira adati, “oh anthu anga! Ndithudi ine ndili kuopa kuti inu mudzaona zimene zidadza pa anthu akale.” |
مِثْلَ دَأْبِ قَوْمِ نُوحٍ وَعَادٍ وَثَمُودَ وَالَّذِينَ مِن بَعْدِهِمْ ۚ وَمَا اللَّهُ يُرِيدُ ظُلْمًا لِّلْعِبَادِ (31) “Monga zimene zidadza kwa anthu a Nowa, a Aad ndi a Thamoud ndi iwo amene adadza iwo atachoka. Koma Mulungu safuna kupondereza akapolo ake.” |
وَيَا قَوْمِ إِنِّي أَخَافُ عَلَيْكُمْ يَوْمَ التَّنَادِ (32) “oh inu anthu anga! Ine ndichita mantha pa zimene zidzaoneka kwa inu pa tsiku louka kwa akufa.” |
يَوْمَ تُوَلُّونَ مُدْبِرِينَ مَا لَكُم مِّنَ اللَّهِ مِنْ عَاصِمٍ ۗ وَمَن يُضْلِلِ اللَّهُ فَمَا لَهُ مِنْ هَادٍ (33) Tsiku limene inu mudzabwerera ndi kuthawa. Inu simudzakhala ndi wokutetezani kwa Mulungu. Ndipo aliyense amene Mulungu amusiya kuti asochere palibe wina amene angamutsogolere |
وَلَقَدْ جَاءَكُمْ يُوسُفُ مِن قَبْلُ بِالْبَيِّنَاتِ فَمَا زِلْتُمْ فِي شَكٍّ مِّمَّا جَاءَكُم بِهِ ۖ حَتَّىٰ إِذَا هَلَكَ قُلْتُمْ لَن يَبْعَثَ اللَّهُ مِن بَعْدِهِ رَسُولًا ۚ كَذَٰلِكَ يُضِلُّ اللَّهُ مَنْ هُوَ مُسْرِفٌ مُّرْتَابٌ (34) Ndithudi Yosefe adadza kwa inu ndi zizindikiro zooneka, koma inu munali kukayika pa zimene iye adabweretsa mpaka pamene iye adafa ndipo inu mudati, “Mulungu sadzadzutsanso Mtumwi wina pambuyo pa iye. Mmenemondimmene Mulunguamamusocheretsamunthu woononga ndi okayika |
الَّذِينَ يُجَادِلُونَ فِي آيَاتِ اللَّهِ بِغَيْرِ سُلْطَانٍ أَتَاهُمْ ۖ كَبُرَ مَقْتًا عِندَ اللَّهِ وَعِندَ الَّذِينَ آمَنُوا ۚ كَذَٰلِكَ يَطْبَعُ اللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ قَلْبِ مُتَكَبِّرٍ جَبَّارٍ (35) Iwo amene amakana uthenga wa Mulungu popanda ulamuliro umene udapatsidwa kwa iwo, zochita zawo ndi zodedwa pamaso pa Mulungu ndi pamaso pa iwo okhulupirira. Mmenemo ndi mmene Mulungu amaphimbira mtima wa munthu wonyada ndi wamwano |
وَقَالَ فِرْعَوْنُ يَا هَامَانُ ابْنِ لِي صَرْحًا لَّعَلِّي أَبْلُغُ الْأَسْبَابَ (36) Ndipo Farawo adati, “oh Hamani! ndimangire nsanja kuti ndikwere.” |
أَسْبَابَ السَّمَاوَاتِ فَأَطَّلِعَ إِلَىٰ إِلَٰهِ مُوسَىٰ وَإِنِّي لَأَظُنُّهُ كَاذِبًا ۚ وَكَذَٰلِكَ زُيِّنَ لِفِرْعَوْنَ سُوءُ عَمَلِهِ وَصُدَّ عَنِ السَّبِيلِ ۚ وَمَا كَيْدُ فِرْعَوْنَ إِلَّا فِي تَبَابٍ (37) “Ndikwere kuti ndikafike kumwamba kuti ndimpeze Mulungu wa Mose koma ine, ndithudi, ndiganiza kuti iye ndi wonama.” Kotero ntchito zoipa za Farao zidaoneka zomusangalatsa, ndipo iye adasocheretsedwa ku njira yoyenera ndipo zochita zake sizinamuthandizechinachilichonseayikomachionongeko |
وَقَالَ الَّذِي آمَنَ يَا قَوْمِ اتَّبِعُونِ أَهْدِكُمْ سَبِيلَ الرَّشَادِ (38) Ndipo iye amene adakhulupirira adati, “oh inu anthu anga! Nditsateni ine. Ine ndidzakutsogolerani ku njira yabwino.” |
يَا قَوْمِ إِنَّمَا هَٰذِهِ الْحَيَاةُ الدُّنْيَا مَتَاعٌ وَإِنَّ الْآخِرَةَ هِيَ دَارُ الْقَرَارِ (39) “Oh inu anthu anga! Moyo wa pa dziko lino ndi chisangalalo cha kanthawi kochepa ndipo, ndithudi, moyo umene uli nkudza ndi wosatha.” |
مَنْ عَمِلَ سَيِّئَةً فَلَا يُجْزَىٰ إِلَّا مِثْلَهَا ۖ وَمَنْ عَمِلَ صَالِحًا مِّن ذَكَرٍ أَوْ أُنثَىٰ وَهُوَ مُؤْمِنٌ فَأُولَٰئِكَ يَدْخُلُونَ الْجَنَّةَ يُرْزَقُونَ فِيهَا بِغَيْرِ حِسَابٍ (40) Aliyense amene achita zoipa adzalandira dipo loipa ndipo aliyense amene achita zabwino kaya ndi wamwamuna kapena wamkazi ndipo ndi wokhulupirira, otere adzalowa ku Paradiso kumene adzapatsidwa madalitso opanda muyeso |
۞ وَيَا قَوْمِ مَا لِي أَدْعُوكُمْ إِلَى النَّجَاةِ وَتَدْعُونَنِي إِلَى النَّارِ (41) “oh inu anthu anga! Kodi mwatani! Ine ndili kukuitanirani ku chipulumutso ndipo inu muli kundiitanira ku moto?” |
تَدْعُونَنِي لِأَكْفُرَ بِاللَّهِ وَأُشْرِكَ بِهِ مَا لَيْسَ لِي بِهِ عِلْمٌ وَأَنَا أَدْعُوكُمْ إِلَى الْعَزِيزِ الْغَفَّارِ (42) “Inu muli kundiitana kuti ndisakhulupirire mwa Mulungu ndipo kuti ndizimufanizira Iye ndi zinthu zina zimene sindizidziwa pamene ine ndili kukuitanani kuti mudze kwa Mwini mphamvu ndi Mwini chikhululukiro.” |
لَا جَرَمَ أَنَّمَا تَدْعُونَنِي إِلَيْهِ لَيْسَ لَهُ دَعْوَةٌ فِي الدُّنْيَا وَلَا فِي الْآخِرَةِ وَأَنَّ مَرَدَّنَا إِلَى اللَّهِ وَأَنَّ الْمُسْرِفِينَ هُمْ أَصْحَابُ النَّارِ (43) “Mosakayika chimene muli kundiitanira chilibe dzina m’dziko lino ndi m’dziko limene lili nkudza ndipo kuti tidzabwerakwa Mulungu. Ndipoonseoswamalamulo, malo awo adzakhala ku moto.” |
فَسَتَذْكُرُونَ مَا أَقُولُ لَكُمْ ۚ وَأُفَوِّضُ أَمْرِي إِلَى اللَّهِ ۚ إِنَّ اللَّهَ بَصِيرٌ بِالْعِبَادِ (44) “Ndipo inu mudzakumbukira zimene ndili kukuuzani ndipo ine ndiika chikhulupiriro changa mwa Mulungu. Ndithudi Mulungu amaona akapolo ake.” |
فَوَقَاهُ اللَّهُ سَيِّئَاتِ مَا مَكَرُوا ۖ وَحَاقَ بِآلِ فِرْعَوْنَ سُوءُ الْعَذَابِ (45) Kotero Mulungu adamuteteza ku chiwembu chimene iwo adakonza ndipo anthu a Farawo chilango chonyansa chidawagwera |
النَّارُ يُعْرَضُونَ عَلَيْهَا غُدُوًّا وَعَشِيًّا ۖ وَيَوْمَ تَقُومُ السَّاعَةُ أَدْخِلُوا آلَ فِرْعَوْنَ أَشَدَّ الْعَذَابِ (46) Ku moto iwo adzasonkhanitsidwa m’mawa ndi madzulo ndipo chiweruzo chawo chidzagamulidwa pa tsiku limene ola lidzakwaniritsidwa ndi kuti, “Alangeni kwambiri anthu a Farawo.” |
وَإِذْ يَتَحَاجُّونَ فِي النَّارِ فَيَقُولُ الضُّعَفَاءُ لِلَّذِينَ اسْتَكْبَرُوا إِنَّا كُنَّا لَكُمْ تَبَعًا فَهَلْ أَنتُم مُّغْنُونَ عَنَّا نَصِيبًا مِّنَ النَّارِ (47) Ndipo pamene iwo adzakangana wina ndi mnzake ku moto, anthu ochepa mphamvu adzati kwa iwo amene anali kuchita mwano, “Ndithudi ife tidali otsatira anu. Kodi simungatichotserepo chilango cha moto?” |
قَالَ الَّذِينَ اسْتَكْبَرُوا إِنَّا كُلٌّ فِيهَا إِنَّ اللَّهَ قَدْ حَكَمَ بَيْنَ الْعِبَادِ (48) Iwo amene adali a mwano adzati, “Tonse tili kumoto. Zoonadi Mulungu waweruza pakati pa akapolo ake.” |
وَقَالَ الَّذِينَ فِي النَّارِ لِخَزَنَةِ جَهَنَّمَ ادْعُوا رَبَّكُمْ يُخَفِّفْ عَنَّا يَوْمًا مِّنَ الْعَذَابِ (49) Ndipo iwo amene adzakhala kumoto adzati kwa iwo osunga Gahena, “Pemphani kwa Ambuye wanu kuti atichepetsere chilango chathu tsiku limodzi.” |
قَالُوا أَوَلَمْ تَكُ تَأْتِيكُمْ رُسُلُكُم بِالْبَيِّنَاتِ ۖ قَالُوا بَلَىٰ ۚ قَالُوا فَادْعُوا ۗ وَمَا دُعَاءُ الْكَافِرِينَ إِلَّا فِي ضَلَالٍ (50) Iwo adzati, “Kodi kwa inu sikudabwere Atumwi anu ndi zizindikiro zooneka?” Iwo adzayankha kuti, “Inde.” Ndipo iwo adzati, “Kotero pemphani ngati mufuna koma pemphero la iwo amene alibe chikhulupiriro ndi lopanda pake.” |
إِنَّا لَنَنصُرُ رُسُلَنَا وَالَّذِينَ آمَنُوا فِي الْحَيَاةِ الدُّنْيَا وَيَوْمَ يَقُومُ الْأَشْهَادُ (51) Ndithudi Ife tidzapambanitsa Atumwi athu pamodzi ndi iwo amene amakhulupirira m’dziko lino ndi tsiku limene mboni zidzaitanidwa |
يَوْمَ لَا يَنفَعُ الظَّالِمِينَ مَعْذِرَتُهُمْ ۖ وَلَهُمُ اللَّعْنَةُ وَلَهُمْ سُوءُ الدَّارِ (52) Tsikuli ndi limene madandaulo a anthu ochita zoipa adzakhala opanda ntchito. Ndipoiwo adzakhala kumalo oipa |
وَلَقَدْ آتَيْنَا مُوسَى الْهُدَىٰ وَأَوْرَثْنَا بَنِي إِسْرَائِيلَ الْكِتَابَ (53) Ndipo Ife, ndithudi ,tidamupatsa Mose langizo. Ndipo tidapereka Buku loti lisungidwe ndi ana a Israyeli |
هُدًى وَذِكْرَىٰ لِأُولِي الْأَلْبَابِ (54) Ma langizo ndi chikumbutso kwa anthu ozindikira |
فَاصْبِرْ إِنَّ وَعْدَ اللَّهِ حَقٌّ وَاسْتَغْفِرْ لِذَنبِكَ وَسَبِّحْ بِحَمْدِ رَبِّكَ بِالْعَشِيِّ وَالْإِبْكَارِ (55) Kotero pirira. Ndithudi lonjezo la Mulungu ndi loona. Ndipo pempha chikhululukiro cha machimo ako ndipo lemekeza Ambuye wako madzulo ndi m’mawa |
إِنَّ الَّذِينَ يُجَادِلُونَ فِي آيَاتِ اللَّهِ بِغَيْرِ سُلْطَانٍ أَتَاهُمْ ۙ إِن فِي صُدُورِهِمْ إِلَّا كِبْرٌ مَّا هُم بِبَالِغِيهِ ۚ فَاسْتَعِذْ بِاللَّهِ ۖ إِنَّهُ هُوَ السَّمِيعُ الْبَصِيرُ (56) Ndithudi iwo amene amatsutsa mawu a Mulungu wopanda lamulo limene ladza kwa iwo, alibe china chilichonse m’mitima mwawo kupatula chilakolako choti akhale a pamwamba koma iwo sadzakhala. Kotero funafuna chitetezo cha Mulungu. Ndithudi Iye amamva ndipo amaona |
لَخَلْقُ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ أَكْبَرُ مِنْ خَلْقِ النَّاسِ وَلَٰكِنَّ أَكْثَرَ النَّاسِ لَا يَعْلَمُونَ (57) Ndithudi chilengedwe cha kumwamba ndi dziko lapansi ndi choposa chilengedwe cha anthu. Koma anthu ambiri sadziwa |
وَمَا يَسْتَوِي الْأَعْمَىٰ وَالْبَصِيرُ وَالَّذِينَ آمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ وَلَا الْمُسِيءُ ۚ قَلِيلًا مَّا تَتَذَكَّرُونَ (58) Ndithudi anthu a khungu ndi anthu openya siofanana ndiponso amene akhulupirira ndi kuchita ntchito zabwino ndi anthu ochita zoipa (safanana). Ndi zochepa zomwe mumakumbukira |
إِنَّ السَّاعَةَ لَآتِيَةٌ لَّا رَيْبَ فِيهَا وَلَٰكِنَّ أَكْثَرَ النَّاسِ لَا يُؤْمِنُونَ (59) Ndithudi ola lidzadza, mosakayika, koma anthu ambiri sakhulupirira |
وَقَالَ رَبُّكُمُ ادْعُونِي أَسْتَجِبْ لَكُمْ ۚ إِنَّ الَّذِينَ يَسْتَكْبِرُونَ عَنْ عِبَادَتِي سَيَدْخُلُونَ جَهَنَّمَ دَاخِرِينَ (60) Ndipo Ambuye wako adati, “Ndipempheni Ine ndipo ndidzayankha pemphero lanu. Ndithudi! Koma iwo amene ndi amwano pondipembedza Ine, ndithudi, adzaponyedwa ku Gahena mochititsa manyazi.” |
اللَّهُ الَّذِي جَعَلَ لَكُمُ اللَّيْلَ لِتَسْكُنُوا فِيهِ وَالنَّهَارَ مُبْصِرًا ۚ إِنَّ اللَّهَ لَذُو فَضْلٍ عَلَى النَّاسِ وَلَٰكِنَّ أَكْثَرَ النَّاسِ لَا يَشْكُرُونَ (61) Ndi Mulungu amene adalenga usiku kuti inu muzipumula ndi usana kuti ukupatseni kuwala. Ndithudi Mulungu amaonetsa chisomo chake kwa anthu koma anthu ambiri sathokoza ayi |
ذَٰلِكُمُ اللَّهُ رَبُّكُمْ خَالِقُ كُلِّ شَيْءٍ لَّا إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ ۖ فَأَنَّىٰ تُؤْفَكُونَ (62) Ameneyu ndiye Mulungu, Ambuye wanu, Namalenga wa zinthu zonse. Kulibe Mulungu wina koma Iye yekha. Nanga ndi chifukwa chiyani inu mumanyengedwa ndi kusiya choonadi |
كَذَٰلِكَ يُؤْفَكُ الَّذِينَ كَانُوا بِآيَاتِ اللَّهِ يَجْحَدُونَ (63) Mmenemo ndi mmene adasiyira choonadi iwo amene adakana uthenga wa Mulungu |
اللَّهُ الَّذِي جَعَلَ لَكُمُ الْأَرْضَ قَرَارًا وَالسَّمَاءَ بِنَاءً وَصَوَّرَكُمْ فَأَحْسَنَ صُوَرَكُمْ وَرَزَقَكُم مِّنَ الطَّيِّبَاتِ ۚ ذَٰلِكُمُ اللَّهُ رَبُّكُمْ ۖ فَتَبَارَكَ اللَّهُ رَبُّ الْعَالَمِينَ (64) Ndi Mulungu amene adalenga dziko lapansi kukhala malo anu okhalamo ndi mtambo ngati chotchinga. Iye ndiye amene adaumba matupi anu ndipo adawaumba ndi maonekedwe abwino ndipo wakupatsani inu zinthu zabwino. Ameneyu ndiye Mulungu, Ambuye wanu. Ulemerero ukhale kwa Mulungu, Ambuye wa zolengedwa zonse |
هُوَ الْحَيُّ لَا إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ فَادْعُوهُ مُخْلِصِينَ لَهُ الدِّينَ ۗ الْحَمْدُ لِلَّهِ رَبِّ الْعَالَمِينَ (65) Iye ndi wamuyaya. Kulibe Mulungu wina koma Iye yekha. Mupempheni Iye ndipo mudzipereke kwathunthu kwa Iye yekha. Ulemerero wonse ukhale kwa Mulungu, Ambuye wa zolengedwa zonse |
۞ قُلْ إِنِّي نُهِيتُ أَنْ أَعْبُدَ الَّذِينَ تَدْعُونَ مِن دُونِ اللَّهِ لَمَّا جَاءَنِيَ الْبَيِّنَاتُ مِن رَّبِّي وَأُمِرْتُ أَنْ أُسْلِمَ لِرَبِّ الْعَالَمِينَ (66) Nena, “Ine ndinaletsedwa kupembedza iwo amene inu mumapembedza kuonjezera pa Mulungu weniweni pamene malangizo abwino anadza kwa ine kuchokera kwa Ambuye wanga. Ndipo ine ndalamulidwa kuti ndizimvera Ambuye wa zolengedwa zonse |
هُوَ الَّذِي خَلَقَكُم مِّن تُرَابٍ ثُمَّ مِن نُّطْفَةٍ ثُمَّ مِنْ عَلَقَةٍ ثُمَّ يُخْرِجُكُمْ طِفْلًا ثُمَّ لِتَبْلُغُوا أَشُدَّكُمْ ثُمَّ لِتَكُونُوا شُيُوخًا ۚ وَمِنكُم مَّن يُتَوَفَّىٰ مِن قَبْلُ ۖ وَلِتَبْلُغُوا أَجَلًا مُّسَمًّى وَلَعَلَّكُمْ تَعْقِلُونَ (67) Ndiye amene adakulengani inu kuchokera ku dothi ndipo kuchokera ku dontho la umuna losakanizana ndi ukazi ndi kuchokera ku magazi oundana ndipo amakutulutsani kukhala mwana ndipo amakukuzani kufika pa msinkhu wanu ndi kukhala wamphamvu, ndipo Iye amakukalambitsani. Ngakhale ena a inu amafa msanga, Iye amakusiyani inu kuti mufike patsiku loikidwa kuti mukhoza kuzindikira |
هُوَ الَّذِي يُحْيِي وَيُمِيتُ ۖ فَإِذَا قَضَىٰ أَمْرًا فَإِنَّمَا يَقُولُ لَهُ كُن فَيَكُونُ (68) Iye ndiye amene amapereka moyo ndi imfa ndipo pamene Iye afuna chinthu, Iye amangonena kwa icho kuti, “Khala” ndipo chimakhala |
أَلَمْ تَرَ إِلَى الَّذِينَ يُجَادِلُونَ فِي آيَاتِ اللَّهِ أَنَّىٰ يُصْرَفُونَ (69) Kodi siudawaone iwo amene amatsutsa uthenga wa Mulungu? Kodi iwo amabwezedwa bwanji ku choonadi |
الَّذِينَ كَذَّبُوا بِالْكِتَابِ وَبِمَا أَرْسَلْنَا بِهِ رُسُلَنَا ۖ فَسَوْفَ يَعْلَمُونَ (70) Iwo amene amakana Buku ndi uthenga umene tidatumiza ndi Atumwi athu, koma posachedwapa iwo adzadziwa |
إِذِ الْأَغْلَالُ فِي أَعْنَاقِهِمْ وَالسَّلَاسِلُ يُسْحَبُونَ (71) Pamene magoli ndi unyolo udzakhala pa khosi pawo, iwo adzaduduluzidwa |
فِي الْحَمِيمِ ثُمَّ فِي النَّارِ يُسْجَرُونَ (72) M’madzi owira ndipo iwo adzatenthedwa ku moto |
ثُمَّ قِيلَ لَهُمْ أَيْنَ مَا كُنتُمْ تُشْرِكُونَ (73) Ndipo zidzanenedwa kwa iwo, “Kodi zili kuti izo zimene munali kuzipembedza?” |
مِن دُونِ اللَّهِ ۖ قَالُوا ضَلُّوا عَنَّا بَل لَّمْ نَكُن نَّدْعُو مِن قَبْلُ شَيْئًا ۚ كَذَٰلِكَ يُضِلُّ اللَّهُ الْكَافِرِينَ (74) “Poonjezera Mulungu?” Iwo adzati, “Zatithawira. Iyayi ife sitimapembedza zina zake.” Kotero Mulungu amasocheretsa anthu osakhulupirira |
ذَٰلِكُم بِمَا كُنتُمْ تَفْرَحُونَ فِي الْأَرْضِ بِغَيْرِ الْحَقِّ وَبِمَا كُنتُمْ تَمْرَحُونَ (75) Ichi ndi chifukwa chakuti inu munali kusangalala ndi zinthu zachabechabe padziko ndipo munali ndi mwano |
ادْخُلُوا أَبْوَابَ جَهَنَّمَ خَالِدِينَ فِيهَا ۖ فَبِئْسَ مَثْوَى الْمُتَكَبِّرِينَ (76) Lowani m’zipata za ku Gahena kuti mukhale m’menemo. Iwowo ndi malo oipa omwe anthu onyada adzakhaleko |
فَاصْبِرْ إِنَّ وَعْدَ اللَّهِ حَقٌّ ۚ فَإِمَّا نُرِيَنَّكَ بَعْضَ الَّذِي نَعِدُهُمْ أَوْ نَتَوَفَّيَنَّكَ فَإِلَيْنَا يُرْجَعُونَ (77) Kotero pirira. Ndithudi lonjezo la Mulungu ndi loona. Kaya tikuonetsa gawo la zimene tili kuwaopseza nazo kapena tikupha, komatu kwa Ife iwo adzabwerera |
وَلَقَدْ أَرْسَلْنَا رُسُلًا مِّن قَبْلِكَ مِنْهُم مَّن قَصَصْنَا عَلَيْكَ وَمِنْهُم مَّن لَّمْ نَقْصُصْ عَلَيْكَ ۗ وَمَا كَانَ لِرَسُولٍ أَن يَأْتِيَ بِآيَةٍ إِلَّا بِإِذْنِ اللَّهِ ۚ فَإِذَا جَاءَ أَمْرُ اللَّهِ قُضِيَ بِالْحَقِّ وَخَسِرَ هُنَالِكَ الْمُبْطِلُونَ (78) Ndithudi Ife tidatumiza Atumwi iwe usanabadwe. Alipo ena amene takuuza za iwo ndipo alipo ena amene sitidakuuze za iwo ndipo sichidali choyenera kuti Mtumwi abweretse chizindikiro kupatula ndi chilolezo cha Mulungu. Koma pamene ulamuliro wa Mulungu udadza, chiweruzo chidaperekedwa mwachilungamo. Ndipo onse, amene ankati ndi zabodza, adatayika |
اللَّهُ الَّذِي جَعَلَ لَكُمُ الْأَنْعَامَ لِتَرْكَبُوا مِنْهَا وَمِنْهَا تَأْكُلُونَ (79) Mulungu ndiye amene adakulengerani nyama kuti mukhoza kukwera zina za izo ndi kudya zina za izo |
وَلَكُمْ فِيهَا مَنَافِعُ وَلِتَبْلُغُوا عَلَيْهَا حَاجَةً فِي صُدُورِكُمْ وَعَلَيْهَا وَعَلَى الْفُلْكِ تُحْمَلُونَ (80) Ndipo muli zambiri zabwino mu nyamazo kuti inu mukhoza kukwaniritsa zofuna zanu zimene zili m’mitima mwanu.Ndipopaizondim’masitimainumumanyamulidwa |
وَيُرِيكُمْ آيَاتِهِ فَأَيَّ آيَاتِ اللَّهِ تُنكِرُونَ (81) Ndipo Iye amakuonetsani zizindikiro zake. Kodi ndi ziti za zizindikiro za Mulungu zimene mumakana |
أَفَلَمْ يَسِيرُوا فِي الْأَرْضِ فَيَنظُرُوا كَيْفَ كَانَ عَاقِبَةُ الَّذِينَ مِن قَبْلِهِمْ ۚ كَانُوا أَكْثَرَ مِنْهُمْ وَأَشَدَّ قُوَّةً وَآثَارًا فِي الْأَرْضِ فَمَا أَغْنَىٰ عَنْهُم مَّا كَانُوا يَكْسِبُونَ (82) Kodi inu simudayende m’dziko ndi kuona zimene zidawachitikira anthu ena amene adalipo iwo asanabadwe? Iwo adali ambiri kuposa awa ndipo adali ndi mphamvu zambiri. Ndipo mwa zinthu zomwe iwo adazisiya pa dziko lapansi ndi zomwe anali kuchita, zonsezi sizidawathandize |
فَلَمَّا جَاءَتْهُمْ رُسُلُهُم بِالْبَيِّنَاتِ فَرِحُوا بِمَا عِندَهُم مِّنَ الْعِلْمِ وَحَاقَ بِهِم مَّا كَانُوا بِهِ يَسْتَهْزِئُونَ (83) Pamene Atumwi awo adadza kwa iwo ndi zizindikiro zooneka, iwo adadzitama chifukwa cha nzeru zimene adali nazo. Ndipo chimene anali kutsutsa chidagwa pa iwo |
فَلَمَّا رَأَوْا بَأْسَنَا قَالُوا آمَنَّا بِاللَّهِ وَحْدَهُ وَكَفَرْنَا بِمَا كُنَّا بِهِ مُشْرِكِينَ (84) Koma pamene iwo adaona chilango chathu, iwo adati, “Ife takhulupirira mwa Mulungu mmodzi yekha ndipo tili kuzikana zonse zimene tidali nazo zoonjezera pa Iye.” |
فَلَمْ يَكُ يَنفَعُهُمْ إِيمَانُهُمْ لَمَّا رَأَوْا بَأْسَنَا ۖ سُنَّتَ اللَّهِ الَّتِي قَدْ خَلَتْ فِي عِبَادِهِ ۖ وَخَسِرَ هُنَالِكَ الْكَافِرُونَ (85) Koma chikhulupiriro chawo sichidawathandize china chilichonse pamene adaona chilango chathu. Ili ndi lamulo la Mulungu limene amaweruzira akapolo ake. Ndipo pamenepo, anthu okana Mulungu adatayika kwambiri |