×

سورة غافر باللغة نيانجا

ترجمات القرآنباللغة نيانجا ⬅ سورة غافر

ترجمة معاني سورة غافر باللغة نيانجا - Chichewa

القرآن باللغة نيانجا - سورة غافر مترجمة إلى اللغة نيانجا، Surah Ghafir in Chichewa. نوفر ترجمة دقيقة سورة غافر باللغة نيانجا - Chichewa, الآيات 85 - رقم السورة 40 - الصفحة 467.

بسم الله الرحمن الرحيم

حم (1)
Ha-Mim
تَنزِيلُ الْكِتَابِ مِنَ اللَّهِ الْعَزِيزِ الْعَلِيمِ (2)
Chivumbulutso cha Buku ili ndi chochokera kwa Mulungu, wamphamvu ndi wodziwa zonse
غَافِرِ الذَّنبِ وَقَابِلِ التَّوْبِ شَدِيدِ الْعِقَابِ ذِي الطَّوْلِ ۖ لَا إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ ۖ إِلَيْهِ الْمَصِيرُ (3)
Iye ndi amene amakhululukira machimo ndipo amavomera kulapa. Iye ndi wankhanza popereka chilango ndi Mwini chinthu chilichonse, ndipo kulibe mulungu wina koma Iye yekha. Kwa Iye chilichonse chidzabwerera
مَا يُجَادِلُ فِي آيَاتِ اللَّهِ إِلَّا الَّذِينَ كَفَرُوا فَلَا يَغْرُرْكَ تَقَلُّبُهُمْ فِي الْبِلَادِ (4)
Palibe amene amatsutsa chivumbulutso cha Mulungu kupatula okhawo amene sakhulupirira. Kotero usanyengedwe ndi kuyendayenda kwawo kwa m’mizinda
كَذَّبَتْ قَبْلَهُمْ قَوْمُ نُوحٍ وَالْأَحْزَابُ مِن بَعْدِهِمْ ۖ وَهَمَّتْ كُلُّ أُمَّةٍ بِرَسُولِهِمْ لِيَأْخُذُوهُ ۖ وَجَادَلُوا بِالْبَاطِلِ لِيُدْحِضُوا بِهِ الْحَقَّ فَأَخَذْتُهُمْ ۖ فَكَيْفَ كَانَ عِقَابِ (5)
Anthu a Nowa ndi anthu a magulu ena amene adadza pambuyo pawo adakana Atumwi, ndipo mtundu uliwonse udachita chiwembu pa Mtumwi wawo, kuti amugwire koteroanalikutsutsananayepazinthuzabodzandicholinga choletsa choonadi. Koma Ine ndidawaononga iwo! Kodi chilango changa chidali chowawa bwanji
وَكَذَٰلِكَ حَقَّتْ كَلِمَتُ رَبِّكَ عَلَى الَّذِينَ كَفَرُوا أَنَّهُمْ أَصْحَابُ النَّارِ (6)
Kotero mawu a Ambuye wako adakwaniritsidwa kwa osakhulupirira ndipo iwo ndi amene adzakhala ku Moto
الَّذِينَ يَحْمِلُونَ الْعَرْشَ وَمَنْ حَوْلَهُ يُسَبِّحُونَ بِحَمْدِ رَبِّهِمْ وَيُؤْمِنُونَ بِهِ وَيَسْتَغْفِرُونَ لِلَّذِينَ آمَنُوا رَبَّنَا وَسِعْتَ كُلَّ شَيْءٍ رَّحْمَةً وَعِلْمًا فَاغْفِرْ لِلَّذِينَ تَابُوا وَاتَّبَعُوا سَبِيلَكَ وَقِهِمْ عَذَابَ الْجَحِيمِ (7)
Iwo amene amasunga Mpando wachifumu ndiponso iwo amene amauzungulira iwo, amatamanda Ambuye wawo ndi kukhulupirira mwa Iye ndipo amapempha chitetezo m’malo mwa iwo amene akhulupirira. “Ambuye wathu! Chifundo ndi nzeru zanu zimakhudza aliyense kotero atetezeni onse amene adza kwa Inu ndi kutsatira njira yanu ndiponso apulumutseni iwo ku chilango cha ku Gahena!”
رَبَّنَا وَأَدْخِلْهُمْ جَنَّاتِ عَدْنٍ الَّتِي وَعَدتَّهُمْ وَمَن صَلَحَ مِنْ آبَائِهِمْ وَأَزْوَاجِهِمْ وَذُرِّيَّاتِهِمْ ۚ إِنَّكَ أَنتَ الْعَزِيزُ الْحَكِيمُ (8)
“Ambuye wathu! Alowetseni ku minda ya Paradiso imene inu mudawalonjeza iwo ndiponso iwo amene amachita zabwino, pakati pa atate, akazi ndi ana awo. Ndithudi Inu ndinu wamphamvu ndi wanzeru kwambiri
وَقِهِمُ السَّيِّئَاتِ ۚ وَمَن تَقِ السَّيِّئَاتِ يَوْمَئِذٍ فَقَدْ رَحِمْتَهُ ۚ وَذَٰلِكَ هُوَ الْفَوْزُ الْعَظِيمُ (9)
“Ndipo apulumutseni ku ntchito zoipa. Aliyense amene Inu mumupulumutsa ku zoipa tsiku lalero ndiye kuti Inu mwamuonetsa chisoni chanu ndipo kumeneko ndiko kupambana kwambiri
إِنَّ الَّذِينَ كَفَرُوا يُنَادَوْنَ لَمَقْتُ اللَّهِ أَكْبَرُ مِن مَّقْتِكُمْ أَنفُسَكُمْ إِذْ تُدْعَوْنَ إِلَى الْإِيمَانِ فَتَكْفُرُونَ (10)
Ndithudi iwo amene sakhulupirira adzamva mkuwo ukuti, “Ndithudi mkwiyo wa Mulungu pa inu ndi waukulu kuposa chidani chimene inuyo mumadzionetsera nokha poona kuti munali kuitanidwa kuti mukhulupirire koma inu munali kukana.”
قَالُوا رَبَّنَا أَمَتَّنَا اثْنَتَيْنِ وَأَحْيَيْتَنَا اثْنَتَيْنِ فَاعْتَرَفْنَا بِذُنُوبِنَا فَهَلْ إِلَىٰ خُرُوجٍ مِّن سَبِيلٍ (11)
Iwo adzati, “Ambuye wathu mudatipha kawiri konse ndipo mudatipatsa moyo kawiri. Tsopano ife tivomereza kuchimwa kwathu. Kodi sitingathe kupulumutsidwa ku chilango cha ku Moto?”
ذَٰلِكُم بِأَنَّهُ إِذَا دُعِيَ اللَّهُ وَحْدَهُ كَفَرْتُمْ ۖ وَإِن يُشْرَكْ بِهِ تُؤْمِنُوا ۚ فَالْحُكْمُ لِلَّهِ الْعَلِيِّ الْكَبِيرِ (12)
“Ichi ndi chifukwa chakuti pamene dzina la Mulungu lokha linali kupembedzedwa, inu simudakhulupirire koma pamene milungu ina inali kupembedzedwa, inu mudakhulupirira. Kotero Mwini wake wa chiweruzo ndi Mulungu Wapamwamba ndi Wamkulukulu.”
هُوَ الَّذِي يُرِيكُمْ آيَاتِهِ وَيُنَزِّلُ لَكُم مِّنَ السَّمَاءِ رِزْقًا ۚ وَمَا يَتَذَكَّرُ إِلَّا مَن يُنِيبُ (13)
Iye ndiye amene amakulangizani inu zizindikiro zake ndipo amakutumizirani chakudya kuchokera ku mitambo. Koma okhawo amene akumbukira ndiwo amene amabwererakwa Mulungu
فَادْعُوا اللَّهَ مُخْلِصِينَ لَهُ الدِّينَ وَلَوْ كَرِهَ الْكَافِرُونَ (14)
Moteropembedzani Mulungu mmodzi yekha, ngakhale kuti anthu osakhulupirira sasangalala
رَفِيعُ الدَّرَجَاتِ ذُو الْعَرْشِ يُلْقِي الرُّوحَ مِنْ أَمْرِهِ عَلَىٰ مَن يَشَاءُ مِنْ عِبَادِهِ لِيُنذِرَ يَوْمَ التَّلَاقِ (15)
Wokweza maudindo anthu okhulupirira ndi Mwini Mpando wachifumu. Iye amatumiza chikumbutso chake kwa aliyense wa akapolo ake amene Iye wamufuna kuti akhoza kuchenjeza anthu za tsiku lachiweruzo
يَوْمَ هُم بَارِزُونَ ۖ لَا يَخْفَىٰ عَلَى اللَّهِ مِنْهُمْ شَيْءٌ ۚ لِّمَنِ الْمُلْكُ الْيَوْمَ ۖ لِلَّهِ الْوَاحِدِ الْقَهَّارِ (16)
Tsiku limene onse adzadza pamodzi, sipadzakhala china chilichonse chobisika kwa Mulungu. Kodi ndani adzakhala ndi ulamuliro wamphamvu pa tsikuli? Ndi Mulungu, mmodzi yekha, Mwini mphamvu zonse
الْيَوْمَ تُجْزَىٰ كُلُّ نَفْسٍ بِمَا كَسَبَتْ ۚ لَا ظُلْمَ الْيَوْمَ ۚ إِنَّ اللَّهَ سَرِيعُ الْحِسَابِ (17)
Tsiku limeneli, mzimu uliwonse udzalandira malipiro ake. Pa tsiku limeneli sikudzakhala kuponderezana. Ndithudi Mulungu ndi wachangu pobwezera
وَأَنذِرْهُمْ يَوْمَ الْآزِفَةِ إِذِ الْقُلُوبُ لَدَى الْحَنَاجِرِ كَاظِمِينَ ۚ مَا لِلظَّالِمِينَ مِنْ حَمِيمٍ وَلَا شَفِيعٍ يُطَاعُ (18)
Achenjeze iwo za tsiku limene lili pafupi kudza, limene mitima idzadza mpaka pakhosi ndi kuwakomola. Palibe bwenzi la pamtima kapena mkhalapakati wa anthu ochita zoipa amene adzayankhulire
يَعْلَمُ خَائِنَةَ الْأَعْيُنِ وَمَا تُخْفِي الصُّدُورُ (19)
Mulungu amadziwa chinyengo cha maso ndi zimene mitima imabisa
وَاللَّهُ يَقْضِي بِالْحَقِّ ۖ وَالَّذِينَ يَدْعُونَ مِن دُونِهِ لَا يَقْضُونَ بِشَيْءٍ ۗ إِنَّ اللَّهَ هُوَ السَّمِيعُ الْبَصِيرُ (20)
Ndipo Mulungu amaweruza mwachilungamo pamene iwo amene amapembedzedwa oonjezera pa Iye sangathe kuweruza. Ndithudi Mulungu amamva ndiponso amaona
۞ أَوَلَمْ يَسِيرُوا فِي الْأَرْضِ فَيَنظُرُوا كَيْفَ كَانَ عَاقِبَةُ الَّذِينَ كَانُوا مِن قَبْلِهِمْ ۚ كَانُوا هُمْ أَشَدَّ مِنْهُمْ قُوَّةً وَآثَارًا فِي الْأَرْضِ فَأَخَذَهُمُ اللَّهُ بِذُنُوبِهِمْ وَمَا كَانَ لَهُم مِّنَ اللَّهِ مِن وَاقٍ (21)
Kodi iwo sadayende pa dziko lapansi ndi kuona zimene zidawachitikira anthu a makedzana? Iwo adali a mphamvu kuposa awa. Koma Mulungu adawalanga chifukwa cha zoipa zawo. Ndipo iwo adalibe wina aliyense wowateteza kwa Mulungu
ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمْ كَانَت تَّأْتِيهِمْ رُسُلُهُم بِالْبَيِّنَاتِ فَكَفَرُوا فَأَخَذَهُمُ اللَّهُ ۚ إِنَّهُ قَوِيٌّ شَدِيدُ الْعِقَابِ (22)
Ichi ndi chifukwa chakuti Atumwi awo adadza kwa iwo ndi zizindikiro zooneka ndi maso koma iwo adakana Atumwiwo. Kotero Mulungu adawaononga iwo. Ndithudi! Iye ndi Wamphamvu ndipo chilango chake ndi chowawa kwambiri
وَلَقَدْ أَرْسَلْنَا مُوسَىٰ بِآيَاتِنَا وَسُلْطَانٍ مُّبِينٍ (23)
Ndipo, ndithudi, tidamutumiza Mose ndi uthenga wathu ndi ulamuliro wooneka
إِلَىٰ فِرْعَوْنَ وَهَامَانَ وَقَارُونَ فَقَالُوا سَاحِرٌ كَذَّابٌ (24)
Kwa Farawo, Hamani ndi Karuni koma iwo adati, “Munthu wamatsenga ndi wabodza.”
فَلَمَّا جَاءَهُم بِالْحَقِّ مِنْ عِندِنَا قَالُوا اقْتُلُوا أَبْنَاءَ الَّذِينَ آمَنُوا مَعَهُ وَاسْتَحْيُوا نِسَاءَهُمْ ۚ وَمَا كَيْدُ الْكَافِرِينَ إِلَّا فِي ضَلَالٍ (25)
Ndipo pamene iye adawauza choonadi chochokera kwa Ife, iwo adati, “Iphani ana onse aamuna a anthu amene akhulupirira ndi iye ndipo musunge ana awo aakazi.” Koma ziwembu za anthu osakhulupirira sizitha bwino chifukwa zilibe maziko enieni
وَقَالَ فِرْعَوْنُ ذَرُونِي أَقْتُلْ مُوسَىٰ وَلْيَدْعُ رَبَّهُ ۖ إِنِّي أَخَافُ أَن يُبَدِّلَ دِينَكُمْ أَوْ أَن يُظْهِرَ فِي الْأَرْضِ الْفَسَادَ (26)
Ndipo Farawo adati, “Mundisiye ine kuti ndiphe Mose ndipo musiyeni iye kuti apemphe kwa Ambuye wake. Ndithudi ine ndiopa kuti iye adzasintha chipembedzo chanu ndi kuyambitsa chisokonezo m’dziko.”
وَقَالَ مُوسَىٰ إِنِّي عُذْتُ بِرَبِّي وَرَبِّكُم مِّن كُلِّ مُتَكَبِّرٍ لَّا يُؤْمِنُ بِيَوْمِ الْحِسَابِ (27)
Ndipo Mose adati, “Ndithudi ine ndithawira kwa Ambuye wanga ndi Ambuye wanu kuti anditeteze kwa aliyense wamwano amene sakhulupirira mu tsiku lachiweruzo.”
وَقَالَ رَجُلٌ مُّؤْمِنٌ مِّنْ آلِ فِرْعَوْنَ يَكْتُمُ إِيمَانَهُ أَتَقْتُلُونَ رَجُلًا أَن يَقُولَ رَبِّيَ اللَّهُ وَقَدْ جَاءَكُم بِالْبَيِّنَاتِ مِن رَّبِّكُمْ ۖ وَإِن يَكُ كَاذِبًا فَعَلَيْهِ كَذِبُهُ ۖ وَإِن يَكُ صَادِقًا يُصِبْكُم بَعْضُ الَّذِي يَعِدُكُمْ ۖ إِنَّ اللَّهَ لَا يَهْدِي مَنْ هُوَ مُسْرِفٌ كَذَّابٌ (28)
Ndipo munthu wamwamuna wokhulupirira wa m’gulu la anthu a Farawo amene adabisa chikhulupiriro chake adati, “Kodi inu mudzapha munthu chifukwa chakuti wanena kuti Ambuye wanga ndi Mulungu pamene iye wadza kwa inu ndi zizindikiro zooneka zochokera kwa Ambuye wanu? Ndipo ngati iye ndi wabodza tchimo likhale pa iye yekha koma ngati iye ali kunena zoona, tsoka limene anena lidzagwa pa inu. Ndithudi Mulungu satsogolera munthu woswa malamulo ndi wabodza.”
يَا قَوْمِ لَكُمُ الْمُلْكُ الْيَوْمَ ظَاهِرِينَ فِي الْأَرْضِ فَمَن يَنصُرُنَا مِن بَأْسِ اللَّهِ إِن جَاءَنَا ۚ قَالَ فِرْعَوْنُ مَا أُرِيكُمْ إِلَّا مَا أَرَىٰ وَمَا أَهْدِيكُمْ إِلَّا سَبِيلَ الرَّشَادِ (29)
“oh inu anthu anga!wanu ndi ufumu walero. Inu muli ndi ulamuliro m’dziko koma ndani amene adzatithandiza ife ku chilango cha Mulungu ngati icho chitagwa pa ife?” Farawo adati, “Ine ndili kungokuuzani zinthu zimene ndimaona ndiponso ndili kukutsogolerani ku njira yoyenera.”
وَقَالَ الَّذِي آمَنَ يَا قَوْمِ إِنِّي أَخَافُ عَلَيْكُم مِّثْلَ يَوْمِ الْأَحْزَابِ (30)
Ndipo iye amene adakhulupirira adati, “oh anthu anga! Ndithudi ine ndili kuopa kuti inu mudzaona zimene zidadza pa anthu akale.”
مِثْلَ دَأْبِ قَوْمِ نُوحٍ وَعَادٍ وَثَمُودَ وَالَّذِينَ مِن بَعْدِهِمْ ۚ وَمَا اللَّهُ يُرِيدُ ظُلْمًا لِّلْعِبَادِ (31)
“Monga zimene zidadza kwa anthu a Nowa, a Aad ndi a Thamoud ndi iwo amene adadza iwo atachoka. Koma Mulungu safuna kupondereza akapolo ake.”
وَيَا قَوْمِ إِنِّي أَخَافُ عَلَيْكُمْ يَوْمَ التَّنَادِ (32)
“oh inu anthu anga! Ine ndichita mantha pa zimene zidzaoneka kwa inu pa tsiku louka kwa akufa.”
يَوْمَ تُوَلُّونَ مُدْبِرِينَ مَا لَكُم مِّنَ اللَّهِ مِنْ عَاصِمٍ ۗ وَمَن يُضْلِلِ اللَّهُ فَمَا لَهُ مِنْ هَادٍ (33)
Tsiku limene inu mudzabwerera ndi kuthawa. Inu simudzakhala ndi wokutetezani kwa Mulungu. Ndipo aliyense amene Mulungu amusiya kuti asochere palibe wina amene angamutsogolere
وَلَقَدْ جَاءَكُمْ يُوسُفُ مِن قَبْلُ بِالْبَيِّنَاتِ فَمَا زِلْتُمْ فِي شَكٍّ مِّمَّا جَاءَكُم بِهِ ۖ حَتَّىٰ إِذَا هَلَكَ قُلْتُمْ لَن يَبْعَثَ اللَّهُ مِن بَعْدِهِ رَسُولًا ۚ كَذَٰلِكَ يُضِلُّ اللَّهُ مَنْ هُوَ مُسْرِفٌ مُّرْتَابٌ (34)
Ndithudi Yosefe adadza kwa inu ndi zizindikiro zooneka, koma inu munali kukayika pa zimene iye adabweretsa mpaka pamene iye adafa ndipo inu mudati, “Mulungu sadzadzutsanso Mtumwi wina pambuyo pa iye. Mmenemondimmene Mulunguamamusocheretsamunthu woononga ndi okayika
الَّذِينَ يُجَادِلُونَ فِي آيَاتِ اللَّهِ بِغَيْرِ سُلْطَانٍ أَتَاهُمْ ۖ كَبُرَ مَقْتًا عِندَ اللَّهِ وَعِندَ الَّذِينَ آمَنُوا ۚ كَذَٰلِكَ يَطْبَعُ اللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ قَلْبِ مُتَكَبِّرٍ جَبَّارٍ (35)
Iwo amene amakana uthenga wa Mulungu popanda ulamuliro umene udapatsidwa kwa iwo, zochita zawo ndi zodedwa pamaso pa Mulungu ndi pamaso pa iwo okhulupirira. Mmenemo ndi mmene Mulungu amaphimbira mtima wa munthu wonyada ndi wamwano
وَقَالَ فِرْعَوْنُ يَا هَامَانُ ابْنِ لِي صَرْحًا لَّعَلِّي أَبْلُغُ الْأَسْبَابَ (36)
Ndipo Farawo adati, “oh Hamani! ndimangire nsanja kuti ndikwere.”
أَسْبَابَ السَّمَاوَاتِ فَأَطَّلِعَ إِلَىٰ إِلَٰهِ مُوسَىٰ وَإِنِّي لَأَظُنُّهُ كَاذِبًا ۚ وَكَذَٰلِكَ زُيِّنَ لِفِرْعَوْنَ سُوءُ عَمَلِهِ وَصُدَّ عَنِ السَّبِيلِ ۚ وَمَا كَيْدُ فِرْعَوْنَ إِلَّا فِي تَبَابٍ (37)
“Ndikwere kuti ndikafike kumwamba kuti ndimpeze Mulungu wa Mose koma ine, ndithudi, ndiganiza kuti iye ndi wonama.” Kotero ntchito zoipa za Farao zidaoneka zomusangalatsa, ndipo iye adasocheretsedwa ku njira yoyenera ndipo zochita zake sizinamuthandizechinachilichonseayikomachionongeko
وَقَالَ الَّذِي آمَنَ يَا قَوْمِ اتَّبِعُونِ أَهْدِكُمْ سَبِيلَ الرَّشَادِ (38)
Ndipo iye amene adakhulupirira adati, “oh inu anthu anga! Nditsateni ine. Ine ndidzakutsogolerani ku njira yabwino.”
يَا قَوْمِ إِنَّمَا هَٰذِهِ الْحَيَاةُ الدُّنْيَا مَتَاعٌ وَإِنَّ الْآخِرَةَ هِيَ دَارُ الْقَرَارِ (39)
“Oh inu anthu anga! Moyo wa pa dziko lino ndi chisangalalo cha kanthawi kochepa ndipo, ndithudi, moyo umene uli nkudza ndi wosatha.”
مَنْ عَمِلَ سَيِّئَةً فَلَا يُجْزَىٰ إِلَّا مِثْلَهَا ۖ وَمَنْ عَمِلَ صَالِحًا مِّن ذَكَرٍ أَوْ أُنثَىٰ وَهُوَ مُؤْمِنٌ فَأُولَٰئِكَ يَدْخُلُونَ الْجَنَّةَ يُرْزَقُونَ فِيهَا بِغَيْرِ حِسَابٍ (40)
Aliyense amene achita zoipa adzalandira dipo loipa ndipo aliyense amene achita zabwino kaya ndi wamwamuna kapena wamkazi ndipo ndi wokhulupirira, otere adzalowa ku Paradiso kumene adzapatsidwa madalitso opanda muyeso
۞ وَيَا قَوْمِ مَا لِي أَدْعُوكُمْ إِلَى النَّجَاةِ وَتَدْعُونَنِي إِلَى النَّارِ (41)
“oh inu anthu anga! Kodi mwatani! Ine ndili kukuitanirani ku chipulumutso ndipo inu muli kundiitanira ku moto?”
تَدْعُونَنِي لِأَكْفُرَ بِاللَّهِ وَأُشْرِكَ بِهِ مَا لَيْسَ لِي بِهِ عِلْمٌ وَأَنَا أَدْعُوكُمْ إِلَى الْعَزِيزِ الْغَفَّارِ (42)
“Inu muli kundiitana kuti ndisakhulupirire mwa Mulungu ndipo kuti ndizimufanizira Iye ndi zinthu zina zimene sindizidziwa pamene ine ndili kukuitanani kuti mudze kwa Mwini mphamvu ndi Mwini chikhululukiro.”
لَا جَرَمَ أَنَّمَا تَدْعُونَنِي إِلَيْهِ لَيْسَ لَهُ دَعْوَةٌ فِي الدُّنْيَا وَلَا فِي الْآخِرَةِ وَأَنَّ مَرَدَّنَا إِلَى اللَّهِ وَأَنَّ الْمُسْرِفِينَ هُمْ أَصْحَابُ النَّارِ (43)
“Mosakayika chimene muli kundiitanira chilibe dzina m’dziko lino ndi m’dziko limene lili nkudza ndipo kuti tidzabwerakwa Mulungu. Ndipoonseoswamalamulo, malo awo adzakhala ku moto.”
فَسَتَذْكُرُونَ مَا أَقُولُ لَكُمْ ۚ وَأُفَوِّضُ أَمْرِي إِلَى اللَّهِ ۚ إِنَّ اللَّهَ بَصِيرٌ بِالْعِبَادِ (44)
“Ndipo inu mudzakumbukira zimene ndili kukuuzani ndipo ine ndiika chikhulupiriro changa mwa Mulungu. Ndithudi Mulungu amaona akapolo ake.”
فَوَقَاهُ اللَّهُ سَيِّئَاتِ مَا مَكَرُوا ۖ وَحَاقَ بِآلِ فِرْعَوْنَ سُوءُ الْعَذَابِ (45)
Kotero Mulungu adamuteteza ku chiwembu chimene iwo adakonza ndipo anthu a Farawo chilango chonyansa chidawagwera
النَّارُ يُعْرَضُونَ عَلَيْهَا غُدُوًّا وَعَشِيًّا ۖ وَيَوْمَ تَقُومُ السَّاعَةُ أَدْخِلُوا آلَ فِرْعَوْنَ أَشَدَّ الْعَذَابِ (46)
Ku moto iwo adzasonkhanitsidwa m’mawa ndi madzulo ndipo chiweruzo chawo chidzagamulidwa pa tsiku limene ola lidzakwaniritsidwa ndi kuti, “Alangeni kwambiri anthu a Farawo.”
وَإِذْ يَتَحَاجُّونَ فِي النَّارِ فَيَقُولُ الضُّعَفَاءُ لِلَّذِينَ اسْتَكْبَرُوا إِنَّا كُنَّا لَكُمْ تَبَعًا فَهَلْ أَنتُم مُّغْنُونَ عَنَّا نَصِيبًا مِّنَ النَّارِ (47)
Ndipo pamene iwo adzakangana wina ndi mnzake ku moto, anthu ochepa mphamvu adzati kwa iwo amene anali kuchita mwano, “Ndithudi ife tidali otsatira anu. Kodi simungatichotserepo chilango cha moto?”
قَالَ الَّذِينَ اسْتَكْبَرُوا إِنَّا كُلٌّ فِيهَا إِنَّ اللَّهَ قَدْ حَكَمَ بَيْنَ الْعِبَادِ (48)
Iwo amene adali a mwano adzati, “Tonse tili kumoto. Zoonadi Mulungu waweruza pakati pa akapolo ake.”
وَقَالَ الَّذِينَ فِي النَّارِ لِخَزَنَةِ جَهَنَّمَ ادْعُوا رَبَّكُمْ يُخَفِّفْ عَنَّا يَوْمًا مِّنَ الْعَذَابِ (49)
Ndipo iwo amene adzakhala kumoto adzati kwa iwo osunga Gahena, “Pemphani kwa Ambuye wanu kuti atichepetsere chilango chathu tsiku limodzi.”
قَالُوا أَوَلَمْ تَكُ تَأْتِيكُمْ رُسُلُكُم بِالْبَيِّنَاتِ ۖ قَالُوا بَلَىٰ ۚ قَالُوا فَادْعُوا ۗ وَمَا دُعَاءُ الْكَافِرِينَ إِلَّا فِي ضَلَالٍ (50)
Iwo adzati, “Kodi kwa inu sikudabwere Atumwi anu ndi zizindikiro zooneka?” Iwo adzayankha kuti, “Inde.” Ndipo iwo adzati, “Kotero pemphani ngati mufuna koma pemphero la iwo amene alibe chikhulupiriro ndi lopanda pake.”
إِنَّا لَنَنصُرُ رُسُلَنَا وَالَّذِينَ آمَنُوا فِي الْحَيَاةِ الدُّنْيَا وَيَوْمَ يَقُومُ الْأَشْهَادُ (51)
Ndithudi Ife tidzapambanitsa Atumwi athu pamodzi ndi iwo amene amakhulupirira m’dziko lino ndi tsiku limene mboni zidzaitanidwa
يَوْمَ لَا يَنفَعُ الظَّالِمِينَ مَعْذِرَتُهُمْ ۖ وَلَهُمُ اللَّعْنَةُ وَلَهُمْ سُوءُ الدَّارِ (52)
Tsikuli ndi limene madandaulo a anthu ochita zoipa adzakhala opanda ntchito. Ndipoiwo adzakhala kumalo oipa
وَلَقَدْ آتَيْنَا مُوسَى الْهُدَىٰ وَأَوْرَثْنَا بَنِي إِسْرَائِيلَ الْكِتَابَ (53)
Ndipo Ife, ndithudi ,tidamupatsa Mose langizo. Ndipo tidapereka Buku loti lisungidwe ndi ana a Israyeli
هُدًى وَذِكْرَىٰ لِأُولِي الْأَلْبَابِ (54)
Ma langizo ndi chikumbutso kwa anthu ozindikira
فَاصْبِرْ إِنَّ وَعْدَ اللَّهِ حَقٌّ وَاسْتَغْفِرْ لِذَنبِكَ وَسَبِّحْ بِحَمْدِ رَبِّكَ بِالْعَشِيِّ وَالْإِبْكَارِ (55)
Kotero pirira. Ndithudi lonjezo la Mulungu ndi loona. Ndipo pempha chikhululukiro cha machimo ako ndipo lemekeza Ambuye wako madzulo ndi m’mawa
إِنَّ الَّذِينَ يُجَادِلُونَ فِي آيَاتِ اللَّهِ بِغَيْرِ سُلْطَانٍ أَتَاهُمْ ۙ إِن فِي صُدُورِهِمْ إِلَّا كِبْرٌ مَّا هُم بِبَالِغِيهِ ۚ فَاسْتَعِذْ بِاللَّهِ ۖ إِنَّهُ هُوَ السَّمِيعُ الْبَصِيرُ (56)
Ndithudi iwo amene amatsutsa mawu a Mulungu wopanda lamulo limene ladza kwa iwo, alibe china chilichonse m’mitima mwawo kupatula chilakolako choti akhale a pamwamba koma iwo sadzakhala. Kotero funafuna chitetezo cha Mulungu. Ndithudi Iye amamva ndipo amaona
لَخَلْقُ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ أَكْبَرُ مِنْ خَلْقِ النَّاسِ وَلَٰكِنَّ أَكْثَرَ النَّاسِ لَا يَعْلَمُونَ (57)
Ndithudi chilengedwe cha kumwamba ndi dziko lapansi ndi choposa chilengedwe cha anthu. Koma anthu ambiri sadziwa
وَمَا يَسْتَوِي الْأَعْمَىٰ وَالْبَصِيرُ وَالَّذِينَ آمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ وَلَا الْمُسِيءُ ۚ قَلِيلًا مَّا تَتَذَكَّرُونَ (58)
Ndithudi anthu a khungu ndi anthu openya siofanana ndiponso amene akhulupirira ndi kuchita ntchito zabwino ndi anthu ochita zoipa (safanana). Ndi zochepa zomwe mumakumbukira
إِنَّ السَّاعَةَ لَآتِيَةٌ لَّا رَيْبَ فِيهَا وَلَٰكِنَّ أَكْثَرَ النَّاسِ لَا يُؤْمِنُونَ (59)
Ndithudi ola lidzadza, mosakayika, koma anthu ambiri sakhulupirira
وَقَالَ رَبُّكُمُ ادْعُونِي أَسْتَجِبْ لَكُمْ ۚ إِنَّ الَّذِينَ يَسْتَكْبِرُونَ عَنْ عِبَادَتِي سَيَدْخُلُونَ جَهَنَّمَ دَاخِرِينَ (60)
Ndipo Ambuye wako adati, “Ndipempheni Ine ndipo ndidzayankha pemphero lanu. Ndithudi! Koma iwo amene ndi amwano pondipembedza Ine, ndithudi, adzaponyedwa ku Gahena mochititsa manyazi.”
اللَّهُ الَّذِي جَعَلَ لَكُمُ اللَّيْلَ لِتَسْكُنُوا فِيهِ وَالنَّهَارَ مُبْصِرًا ۚ إِنَّ اللَّهَ لَذُو فَضْلٍ عَلَى النَّاسِ وَلَٰكِنَّ أَكْثَرَ النَّاسِ لَا يَشْكُرُونَ (61)
Ndi Mulungu amene adalenga usiku kuti inu muzipumula ndi usana kuti ukupatseni kuwala. Ndithudi Mulungu amaonetsa chisomo chake kwa anthu koma anthu ambiri sathokoza ayi
ذَٰلِكُمُ اللَّهُ رَبُّكُمْ خَالِقُ كُلِّ شَيْءٍ لَّا إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ ۖ فَأَنَّىٰ تُؤْفَكُونَ (62)
Ameneyu ndiye Mulungu, Ambuye wanu, Namalenga wa zinthu zonse. Kulibe Mulungu wina koma Iye yekha. Nanga ndi chifukwa chiyani inu mumanyengedwa ndi kusiya choonadi
كَذَٰلِكَ يُؤْفَكُ الَّذِينَ كَانُوا بِآيَاتِ اللَّهِ يَجْحَدُونَ (63)
Mmenemo ndi mmene adasiyira choonadi iwo amene adakana uthenga wa Mulungu
اللَّهُ الَّذِي جَعَلَ لَكُمُ الْأَرْضَ قَرَارًا وَالسَّمَاءَ بِنَاءً وَصَوَّرَكُمْ فَأَحْسَنَ صُوَرَكُمْ وَرَزَقَكُم مِّنَ الطَّيِّبَاتِ ۚ ذَٰلِكُمُ اللَّهُ رَبُّكُمْ ۖ فَتَبَارَكَ اللَّهُ رَبُّ الْعَالَمِينَ (64)
Ndi Mulungu amene adalenga dziko lapansi kukhala malo anu okhalamo ndi mtambo ngati chotchinga. Iye ndiye amene adaumba matupi anu ndipo adawaumba ndi maonekedwe abwino ndipo wakupatsani inu zinthu zabwino. Ameneyu ndiye Mulungu, Ambuye wanu. Ulemerero ukhale kwa Mulungu, Ambuye wa zolengedwa zonse
هُوَ الْحَيُّ لَا إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ فَادْعُوهُ مُخْلِصِينَ لَهُ الدِّينَ ۗ الْحَمْدُ لِلَّهِ رَبِّ الْعَالَمِينَ (65)
Iye ndi wamuyaya. Kulibe Mulungu wina koma Iye yekha. Mupempheni Iye ndipo mudzipereke kwathunthu kwa Iye yekha. Ulemerero wonse ukhale kwa Mulungu, Ambuye wa zolengedwa zonse
۞ قُلْ إِنِّي نُهِيتُ أَنْ أَعْبُدَ الَّذِينَ تَدْعُونَ مِن دُونِ اللَّهِ لَمَّا جَاءَنِيَ الْبَيِّنَاتُ مِن رَّبِّي وَأُمِرْتُ أَنْ أُسْلِمَ لِرَبِّ الْعَالَمِينَ (66)
Nena, “Ine ndinaletsedwa kupembedza iwo amene inu mumapembedza kuonjezera pa Mulungu weniweni pamene malangizo abwino anadza kwa ine kuchokera kwa Ambuye wanga. Ndipo ine ndalamulidwa kuti ndizimvera Ambuye wa zolengedwa zonse
هُوَ الَّذِي خَلَقَكُم مِّن تُرَابٍ ثُمَّ مِن نُّطْفَةٍ ثُمَّ مِنْ عَلَقَةٍ ثُمَّ يُخْرِجُكُمْ طِفْلًا ثُمَّ لِتَبْلُغُوا أَشُدَّكُمْ ثُمَّ لِتَكُونُوا شُيُوخًا ۚ وَمِنكُم مَّن يُتَوَفَّىٰ مِن قَبْلُ ۖ وَلِتَبْلُغُوا أَجَلًا مُّسَمًّى وَلَعَلَّكُمْ تَعْقِلُونَ (67)
Ndiye amene adakulengani inu kuchokera ku dothi ndipo kuchokera ku dontho la umuna losakanizana ndi ukazi ndi kuchokera ku magazi oundana ndipo amakutulutsani kukhala mwana ndipo amakukuzani kufika pa msinkhu wanu ndi kukhala wamphamvu, ndipo Iye amakukalambitsani. Ngakhale ena a inu amafa msanga, Iye amakusiyani inu kuti mufike patsiku loikidwa kuti mukhoza kuzindikira
هُوَ الَّذِي يُحْيِي وَيُمِيتُ ۖ فَإِذَا قَضَىٰ أَمْرًا فَإِنَّمَا يَقُولُ لَهُ كُن فَيَكُونُ (68)
Iye ndiye amene amapereka moyo ndi imfa ndipo pamene Iye afuna chinthu, Iye amangonena kwa icho kuti, “Khala” ndipo chimakhala
أَلَمْ تَرَ إِلَى الَّذِينَ يُجَادِلُونَ فِي آيَاتِ اللَّهِ أَنَّىٰ يُصْرَفُونَ (69)
Kodi siudawaone iwo amene amatsutsa uthenga wa Mulungu? Kodi iwo amabwezedwa bwanji ku choonadi
الَّذِينَ كَذَّبُوا بِالْكِتَابِ وَبِمَا أَرْسَلْنَا بِهِ رُسُلَنَا ۖ فَسَوْفَ يَعْلَمُونَ (70)
Iwo amene amakana Buku ndi uthenga umene tidatumiza ndi Atumwi athu, koma posachedwapa iwo adzadziwa
إِذِ الْأَغْلَالُ فِي أَعْنَاقِهِمْ وَالسَّلَاسِلُ يُسْحَبُونَ (71)
Pamene magoli ndi unyolo udzakhala pa khosi pawo, iwo adzaduduluzidwa
فِي الْحَمِيمِ ثُمَّ فِي النَّارِ يُسْجَرُونَ (72)
M’madzi owira ndipo iwo adzatenthedwa ku moto
ثُمَّ قِيلَ لَهُمْ أَيْنَ مَا كُنتُمْ تُشْرِكُونَ (73)
Ndipo zidzanenedwa kwa iwo, “Kodi zili kuti izo zimene munali kuzipembedza?”
مِن دُونِ اللَّهِ ۖ قَالُوا ضَلُّوا عَنَّا بَل لَّمْ نَكُن نَّدْعُو مِن قَبْلُ شَيْئًا ۚ كَذَٰلِكَ يُضِلُّ اللَّهُ الْكَافِرِينَ (74)
“Poonjezera Mulungu?” Iwo adzati, “Zatithawira. Iyayi ife sitimapembedza zina zake.” Kotero Mulungu amasocheretsa anthu osakhulupirira
ذَٰلِكُم بِمَا كُنتُمْ تَفْرَحُونَ فِي الْأَرْضِ بِغَيْرِ الْحَقِّ وَبِمَا كُنتُمْ تَمْرَحُونَ (75)
Ichi ndi chifukwa chakuti inu munali kusangalala ndi zinthu zachabechabe padziko ndipo munali ndi mwano
ادْخُلُوا أَبْوَابَ جَهَنَّمَ خَالِدِينَ فِيهَا ۖ فَبِئْسَ مَثْوَى الْمُتَكَبِّرِينَ (76)
Lowani m’zipata za ku Gahena kuti mukhale m’menemo. Iwowo ndi malo oipa omwe anthu onyada adzakhaleko
فَاصْبِرْ إِنَّ وَعْدَ اللَّهِ حَقٌّ ۚ فَإِمَّا نُرِيَنَّكَ بَعْضَ الَّذِي نَعِدُهُمْ أَوْ نَتَوَفَّيَنَّكَ فَإِلَيْنَا يُرْجَعُونَ (77)
Kotero pirira. Ndithudi lonjezo la Mulungu ndi loona. Kaya tikuonetsa gawo la zimene tili kuwaopseza nazo kapena tikupha, komatu kwa Ife iwo adzabwerera
وَلَقَدْ أَرْسَلْنَا رُسُلًا مِّن قَبْلِكَ مِنْهُم مَّن قَصَصْنَا عَلَيْكَ وَمِنْهُم مَّن لَّمْ نَقْصُصْ عَلَيْكَ ۗ وَمَا كَانَ لِرَسُولٍ أَن يَأْتِيَ بِآيَةٍ إِلَّا بِإِذْنِ اللَّهِ ۚ فَإِذَا جَاءَ أَمْرُ اللَّهِ قُضِيَ بِالْحَقِّ وَخَسِرَ هُنَالِكَ الْمُبْطِلُونَ (78)
Ndithudi Ife tidatumiza Atumwi iwe usanabadwe. Alipo ena amene takuuza za iwo ndipo alipo ena amene sitidakuuze za iwo ndipo sichidali choyenera kuti Mtumwi abweretse chizindikiro kupatula ndi chilolezo cha Mulungu. Koma pamene ulamuliro wa Mulungu udadza, chiweruzo chidaperekedwa mwachilungamo. Ndipo onse, amene ankati ndi zabodza, adatayika
اللَّهُ الَّذِي جَعَلَ لَكُمُ الْأَنْعَامَ لِتَرْكَبُوا مِنْهَا وَمِنْهَا تَأْكُلُونَ (79)
Mulungu ndiye amene adakulengerani nyama kuti mukhoza kukwera zina za izo ndi kudya zina za izo
وَلَكُمْ فِيهَا مَنَافِعُ وَلِتَبْلُغُوا عَلَيْهَا حَاجَةً فِي صُدُورِكُمْ وَعَلَيْهَا وَعَلَى الْفُلْكِ تُحْمَلُونَ (80)
Ndipo muli zambiri zabwino mu nyamazo kuti inu mukhoza kukwaniritsa zofuna zanu zimene zili m’mitima mwanu.Ndipopaizondim’masitimainumumanyamulidwa
وَيُرِيكُمْ آيَاتِهِ فَأَيَّ آيَاتِ اللَّهِ تُنكِرُونَ (81)
Ndipo Iye amakuonetsani zizindikiro zake. Kodi ndi ziti za zizindikiro za Mulungu zimene mumakana
أَفَلَمْ يَسِيرُوا فِي الْأَرْضِ فَيَنظُرُوا كَيْفَ كَانَ عَاقِبَةُ الَّذِينَ مِن قَبْلِهِمْ ۚ كَانُوا أَكْثَرَ مِنْهُمْ وَأَشَدَّ قُوَّةً وَآثَارًا فِي الْأَرْضِ فَمَا أَغْنَىٰ عَنْهُم مَّا كَانُوا يَكْسِبُونَ (82)
Kodi inu simudayende m’dziko ndi kuona zimene zidawachitikira anthu ena amene adalipo iwo asanabadwe? Iwo adali ambiri kuposa awa ndipo adali ndi mphamvu zambiri. Ndipo mwa zinthu zomwe iwo adazisiya pa dziko lapansi ndi zomwe anali kuchita, zonsezi sizidawathandize
فَلَمَّا جَاءَتْهُمْ رُسُلُهُم بِالْبَيِّنَاتِ فَرِحُوا بِمَا عِندَهُم مِّنَ الْعِلْمِ وَحَاقَ بِهِم مَّا كَانُوا بِهِ يَسْتَهْزِئُونَ (83)
Pamene Atumwi awo adadza kwa iwo ndi zizindikiro zooneka, iwo adadzitama chifukwa cha nzeru zimene adali nazo. Ndipo chimene anali kutsutsa chidagwa pa iwo
فَلَمَّا رَأَوْا بَأْسَنَا قَالُوا آمَنَّا بِاللَّهِ وَحْدَهُ وَكَفَرْنَا بِمَا كُنَّا بِهِ مُشْرِكِينَ (84)
Koma pamene iwo adaona chilango chathu, iwo adati, “Ife takhulupirira mwa Mulungu mmodzi yekha ndipo tili kuzikana zonse zimene tidali nazo zoonjezera pa Iye.”
فَلَمْ يَكُ يَنفَعُهُمْ إِيمَانُهُمْ لَمَّا رَأَوْا بَأْسَنَا ۖ سُنَّتَ اللَّهِ الَّتِي قَدْ خَلَتْ فِي عِبَادِهِ ۖ وَخَسِرَ هُنَالِكَ الْكَافِرُونَ (85)
Koma chikhulupiriro chawo sichidawathandize china chilichonse pamene adaona chilango chathu. Ili ndi lamulo la Mulungu limene amaweruzira akapolo ake. Ndipo pamenepo, anthu okana Mulungu adatayika kwambiri
❮ السورة السابقة السورة التـالية ❯

قراءة المزيد من سور القرآن الكريم :

1- الفاتحة2- البقرة3- آل عمران
4- النساء5- المائدة6- الأنعام
7- الأعراف8- الأنفال9- التوبة
10- يونس11- هود12- يوسف
13- الرعد14- إبراهيم15- الحجر
16- النحل17- الإسراء18- الكهف
19- مريم20- طه21- الأنبياء
22- الحج23- المؤمنون24- النور
25- الفرقان26- الشعراء27- النمل
28- القصص29- العنكبوت30- الروم
31- لقمان32- السجدة33- الأحزاب
34- سبأ35- فاطر36- يس
37- الصافات38- ص39- الزمر
40- غافر41- فصلت42- الشورى
43- الزخرف44- الدخان45- الجاثية
46- الأحقاف47- محمد48- الفتح
49- الحجرات50- ق51- الذاريات
52- الطور53- النجم54- القمر
55- الرحمن56- الواقعة57- الحديد
58- المجادلة59- الحشر60- الممتحنة
61- الصف62- الجمعة63- المنافقون
64- التغابن65- الطلاق66- التحريم
67- الملك68- القلم69- الحاقة
70- المعارج71- نوح72- الجن
73- المزمل74- المدثر75- القيامة
76- الإنسان77- المرسلات78- النبأ
79- النازعات80- عبس81- التكوير
82- الإنفطار83- المطففين84- الانشقاق
85- البروج86- الطارق87- الأعلى
88- الغاشية89- الفجر90- البلد
91- الشمس92- الليل93- الضحى
94- الشرح95- التين96- العلق
97- القدر98- البينة99- الزلزلة
100- العاديات101- القارعة102- التكاثر
103- العصر104- الهمزة105- الفيل
106- قريش107- الماعون108- الكوثر
109- الكافرون110- النصر111- المسد
112- الإخلاص113- الفلق114- الناس