×

Koma yense amene amanena kwa makolo ake kuti, “Asa! Kodi inu muli 46:17 Chichewa translation

Quran infoChichewaSurah Al-Ahqaf ⮕ (46:17) ayat 17 in Chichewa

46:17 Surah Al-Ahqaf ayat 17 in Chichewa (نيانجا)

Quran with Chichewa translation - Surah Al-Ahqaf ayat 17 - الأحقَاف - Page - Juz 26

﴿وَٱلَّذِي قَالَ لِوَٰلِدَيۡهِ أُفّٖ لَّكُمَآ أَتَعِدَانِنِيٓ أَنۡ أُخۡرَجَ وَقَدۡ خَلَتِ ٱلۡقُرُونُ مِن قَبۡلِي وَهُمَا يَسۡتَغِيثَانِ ٱللَّهَ وَيۡلَكَ ءَامِنۡ إِنَّ وَعۡدَ ٱللَّهِ حَقّٞ فَيَقُولُ مَا هَٰذَآ إِلَّآ أَسَٰطِيرُ ٱلۡأَوَّلِينَ ﴾
[الأحقَاف: 17]

Koma yense amene amanena kwa makolo ake kuti, “Asa! Kodi inu muli kundilonjeza kuti ine ndidzaukitsidwa pamene mibadwo ina yambiri idapita kale ine ndisanabadwe?” Ndipo iwo amapempha chithandizo cha Mulungu nati, “Tsoka kwa iwe! Khulupirira! Ndithudi lonjezo la Mulungu ndi loona.” Koma iye amati, “Ichi si chinthu china koma nkhani zachabe za anthu amakedzana.”

❮ Previous Next ❯

ترجمة: والذي قال لوالديه أف لكما أتعدانني أن أخرج وقد خلت القرون من, باللغة نيانجا

﴿والذي قال لوالديه أف لكما أتعدانني أن أخرج وقد خلت القرون من﴾ [الأحقَاف: 17]

Khaled Ibrahim Betala
“Tsono (mwana woipa) amene akunena kwa makolo ake, (akamuitanira ku chikhulupiliro kuti): “Ndithu ndinu oipa (pa zimene mukundiitanirazi)! Mukundilonjeza kuti ndidzatulutsidwa mmanda ndili wamoyo, chikhalirecho mibadwo ndi mibadwo idapita kumanda ine kulibe (koma mpaka lero siidauke)?” Ndipo uku makolo ake akupempha Allah kuti ampulumutse ndi kumuongola ndi kunena kwa iye: “Tsoka kwa iwe khulupirira (Allah ndi kuuka ku imfa, ngati sutero waonongeka). Ndithu lonjezo la Allah ndiloona.” Koma iye nkumanena (kuti): “Mukunenazi sikanthu koma ndi nthano za anthu akale.”
❮ Previous Next ❯

Verse in more languages

Transliteration Bangla Bosnian German English Persian French Hindi Indonesian Kazakh Dutch Russian Spanish Turkish Urdu Uzbek